Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Kodi Mumakonda Masewera Oika Moyo Pangozi?

Kodi Mumakonda Masewera Oika Moyo Pangozi?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Leon anati: “Ndinkakonda kuima pafupi kwambiri ndi sitima imene ikuthamanga. Mumtimamu ndinkamva bwino moti ndinkangoona kuti ndilibiletu mavuto.” *

Larissa anati: “Ndinkaima paphiri lalitali n’kumadumphira m’madzi, zinkandisangalatsa koma nthawi zina ndinkachita mantha.”

Mofanana ndi Leon komanso Larissa, achinyamata ambiri amafuna kudziwa ngati angakwanitse kuchita masewera enaake. Koma nthawi zina amachita zinthu zimene zingaike moyo wawo pangozi. Kodi nanunso zimenezi zimakuchitikirani? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani kwambiri.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Munthu angamavutike kuti asiye masewera oika moyo pangozi. Munthu akayamba kuchita masewerawa, amaona kuti ndi osangalatsa kwambiri ndipo amafuna kuti azingochitabe. Marco, mofanana ndi Leon, nayenso ankakonda kuima pafupi kwambiri ndi sitima imene ikuthamanga. Iye anati: “Ngakhale kuti ndinkasangalala kwa kanthawi, zinali zochititsa mantha. Koma ndinkafuna kuti ndizingochitabe zimenezi.”

Justin ankachita masewero ozendewera galimoto zimene zikudutsa n’kumakokeka atavala nsapato zamateyala. Iye anati: “Ndinkafuna ndizingochitabe masewerawo kuti anthu azisilira. Koma zotsatira zake ndinavulala mpaka kuchipatala.”

Anzanu angakukakamizeni kuti muzingotsatira zofuna zawo. Mnyamata wina dzina lake Marvin ananena kuti: “Anzanga anandikakamiza kuti ndikwere khoma lalitali la nyumba, amvekere, ‘Takwera iwe, usakayikire ukwanitsa.’ Koma ine ndinkachita mantha kwambiri moti pamene ndinkakwera ndinkanjenjemera.” Larissa tinamutchula poyamba paja anati: “Ndinkachita zimenezi chifukwa anzanga ankachitanso zomwezo ndipo ndinangozolowera.”

Pa intaneti, anthu amaikapo zinthu zimene zimakopa achinyamata kuti azichita masewera oika moyo pangozi koma safotokozapo mavuto ake. Ndipotu mavidiyo osonyeza anthu akuchita masewerawa akangoikidwa pa intaneti, m’kanthawi kochepa anthu ambiri amakhala atawaonera.

Mavidiyo ambiri otchuka amasonyeza anthu akukwera komanso kudumpha zinthu zitalizitali monga makoma, nyumba kapena masitepe mothamanga kwambiri koma alibe zovala zodzitetezera pangozi. Zimenezi zingakuchititseni kuyamba kuganiza molakwika n’kumaona kuti (1) zilibe vuto kwenikweni komanso (2) aliyense akhoza kukwanitsa. Zotsatira zake n’zakuti nanunso mungatengeke n’kumafuna kuchita zinthu zimene zingaike moyo wanu pangozi.

Pali zinthu zina zimene zingakuthandizeni kudziwa malire anu ochitira zinthu. Baibulo limati: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa pang’ono.” (1 Timoteyo 4:8) Koma limatichenjezanso kuti tiyenera “kukhala amaganizo abwino.” (Tito 2:12) Kodi tingatani kuti tikhale ndi maganizo abwinowo?

ZIMENE MUNGACHITE

Muziganizira zotsatirapo zake. Baibulo limati: “Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira, koma wopusa amafalitsa uchitsiru.” (Miyambo 13:16) Musanapange masewera enaake kapena zinazake, muzidziwiratu mavuto ake. Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi zimenezi sizingandibweretsere mavuto aakulu mwina kuvulala kapena kufa kumene?’​—Lemba lothandiza: Miyambo 14:15.

Muzicheza ndi anzanu amene amalemekeza moyo. Anzanu abwino sangakulimbikitseni kuti muchite zinthu zimene zingaike moyo wanu pangozi kapena zimene simukusangalala nazo. Larissa ananena kuti: “Anzanga abwino komanso odalirika anandithandiza kuti ndizisankha mwanzeru masewera kapena zimene ndikufuna kuchita. Chifukwa choti ndinapeza anzanga abwino, moyo wanga unasintha.”​—Lemba lothandiza: Miyambo 13:20.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi zimene ndikuchitazi sizingandibweretsere mavuto aakulu mwina kuvulala kwambiri kapena kufa kumene?’

Muzigwiritsa ntchito bwino luso lanu popanda kuika moyo pangozi. Buku lina linanena kuti wachinyamata akamakula amayenera kuti “azikhala ndi mfundo zokhazikika zoti azitsatira komanso azidziwa malire ake ochitira zinthu.” N’zotheka kudziwa malire anu ochitira zinthu popanda kuika moyo wanu pangozi. Ngati mukuchita masewera enaake muzivala zodzitetezera komanso kutsatira malangizo ake.

Muzichita zinthu zoti anthu azikulemekezani. Anthu angayambe kukulemekezani akaona kuti mumayesetsa kuthana ndi mavuto amene mumakumana nawo, osati chifukwa choti mukuchita masewera enaake oika moyo pangozi. Larissa ananena kuti: “Nditangoyamba masewera okwera paphiri lalitali n’kudumphira m’madzi, ndinayamba kuchitanso zinthu zina zomwe zikanaika moyo wanga pangozi. Ndimaona kuti zikanakhala bwino ndikanapanda kuphunzira masewerawa.”

Mfundo yofunika kwambiri: Muzisankha bwino zosangalatsa zimene mumafuna kuchita m’malo mochita zinthu zomwe zingaike moyo wanu pangozi.​—Lemba lothandiza: Miyambo 15:24.

^ ndime 4 Mayina ena asinthidwa munkhaniyi.