Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Mmene Kutha Kwa Banja Kumakhudzira Ana

Mmene Kutha Kwa Banja Kumakhudzira Ana

 Anthu ena amene banja lawo silikuyenda bwino amadziuza kuti kuthetsa banjalo kungathandize ana awo, kusiyana n’kuti anawo azikhala ndi makolo omwe sakugwirizana. Koma kodi kafukufuku pa nkhaniyi anapeza zotani?

 Kodi kutha kwa banja kumakhudza bwanji ana?

 Kafukufuku akusonyeza kuti kuthetsa banja kumabweretsa mavuto ambiri kwa ana. Nthawi zambiri ana omwe makolo awo athetsa banja:

  •   amakhala okwiya, a nkhawa, komanso amavutika maganizo

  •   amayamba makhalidwe oipa

  •   sachita bwino kusukulu kapena amasiya kumene

  •   amadwaladwala

 Kuonjezera pamenepo, ana ambiri amadziimba mlandu chifukwa cha kutha kwa banja la makolo awo. Iwo amaganiza kuti ndi iwowo amene anachititsa, kapena akanatha kuchita zinazake kuti banjalo lisathe.

 Mavuto a ana amene banja la makolo awo linatha amapitirirabe ngakhale anawo atakula. Iwo akhoza kumadziona kuti ndi achabechabe komanso zimawavuta kukhulupirira anthu ena. Nawonso akadzakula akhoza kudzathetsa mabanja awo ngati sakuyenda bwino.

 Mfundo yofunika kwambiri: Ngakhale kuti anthu ena omwe akuganiza zothetsa banja amaganiza kuti kuchita zimenezi kungathandize ana awo, kafukufuku akusonyeza kuti zimenezi si zoona. Katswiri pa nkhani zosamalira ana, dzina lake Penelope Leach anati: “Kuthetsa banja kumachititsa ana kuvutika.” a

 Mfundo ya m’Baibulo: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.

 Kodi mwana wanga adzakhala wosangalala kwambiri ngati banja langa litatha?

 Anthu ena akhoza kunena kuti inde. Koma kumbukirani kuti zofuna za kholo nthawi zambiri zimakhala zosiyana ndi zofuna za mwana. Munthu amene akuganiza zothetsa banja amafuna kuti moyo wake usinthe. Koma nthawi zambiri mwana safuna kuti moyo wake usinthe ndipo amafuna kuti azikhalabe ndi makolo ake.

 Atachita kafukufuku pa mabanja masauzande ambiri omwe anatha, amene analemba buku lakuti The Unexpected Legacy of Divorce ananena kuti: “Mfundo imodzi ndi yoonekeratu: ana sanena kuti ndi osangalala kwambiri kuposa kale. M’malomwake, iwo amati, ‘Tsiku limene makolo anga anathetsa banja ndi limene ndinasiya kukhala wosangalala.’” Bukuli linawonjezeranso kuti anawa amaona kuti dzikoli “ndi losadalirika kwenikweni, ndi malo oopsa kwambiri chifukwa ubwenzi wa anthu omwe anawo anali nawo pafupi kwambiri m’moyo wawo unali wosalimba.”

 Mfundo yofunika kwambiri: Ana sasangalala banja la makolo awo likatha.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—Miyambo 17:22.

 Kodi ndiyenera kudziwa zotani zokhudza kulerera limodzi ana pamene banja latha?

 Makolo ena amene banja lawo latha amayesa kulera ana awo ngati kuti akadali limodzi, ndipo amaganiza kuti akhoza kugawana udindowu mofanana. Komatu kulera ana mwa njira imeneyi n’kovuta. Kafukufuku akusonyeza kuti makolo omwe banja lawo latha, nthawi zambiri:

  •   sakhala ndi ana awo kwa nthawi yaitali

  •   amaphunzitsa ana awo zinthu zosiyana

  •   amalola ana awo kuchita zilizonse zimene akufuna chifukwa amadziona kuti analakwitsa kapena chifukwa chotopa.

 Mwana amene banja la makolo ake linatha akhoza kumaganiza kuti sakuyenera kumvera zonena za makolo akewo. Iye amaona kuti makolowo analephera kuchita zinthu zoyenera monga kukhala wokhulupirika komanso kusunga malonjezo awo. Mwanayo akhoza kumadzifunsa kuti, ‘Ndiye ndiyenera kuwamvera iwowo chifukwa chiyani?’

 Mfundo yofunika kwambiri: Nthawi zambiri kulerera ana limodzi kumakhala kovuta kwa makolo omwe banja lawo latha. Koma anawo ndi amene amakumana ndi mavuto aakulu kwambiri.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”—Akolose 3:21.

 Kodi pali njira yabwino yothetsera mavuto a m’banja?

 Nthawi zambiri, pamafunika khama kuti munthu ayambenso kukhala yekha banja likatha, khama lomwe likanatha kugwiritsidwa ntchito kuti banja lake lisathe. Buku lakuti The Case for Marriage linanena kuti: “M’banja limene muli mavuto si kuti mudzakhala mavuto mpaka kalekale ngati mmene nthawi zina timaganizira. N’kupita kwa nthawi, mwamuna ndi mkazi omwe sakusangalala amadzayambanso kusangalala ngati atasankha kuti asathetse banja lawo.” Nthawi zambiri, ana zinthu zimawayendera bwino ngati makolo awo ali limodzi.

 Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu okwatirana sangasankhe kuthetsa banja. Baibulo limavomereza kuthetsa banja ngati wina wachita dama. (Mateyu 19:9) Komabe, Baibulo limanenanso kuti “wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Amuna komanso akazi amene banja lawo silikuyenda bwino, akuyenera kuganizira zinthu zosiyanasiyana ngati akufuna kuthetsa banjalo, kuphatikizapo mmene kuchita zimenezi kukhudzire ana awo.

 N’zodziwikiratu kuti pangafunike kuchita zinazake kusiyana n’kumangopirira koma osachita chilichonse. M’Baibulo muli malangizo abwino kwambiri amene angathandize amuna ndi akazi kukhala ndi makhalidwe omwe angawathandize kuti akhale ndi banja lolimba komanso losangalala. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Yehova, yemwe analemba Baibulo, ndi amene anayambitsa banja.—Mateyu 19:4-6.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.”—Yesaya 48:17.

a Kuchokera m’buku lakuti Your Growing Child—From Babyhood Through Adolescence.