Pitani ku nkhani yake

ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

N’chifukwa Chiyani Kuwerenga ndi Kofunika Kwambiri kwa Ana?​—Mbali Yachiwiri: Kodi Aziwerenga Zinthu Zochita Kupulinta Kapena za Pazipangizo Zamakono?

N’chifukwa Chiyani Kuwerenga ndi Kofunika Kwambiri kwa Ana?​—Mbali Yachiwiri: Kodi Aziwerenga Zinthu Zochita Kupulinta Kapena za Pazipangizo Zamakono?

 Kodi mwana wanu amakonda kuwerenga zinthu za pazipangizo zamakono kapena zochita kupulinta?

 Ana ambiri angakonde kuwerengera zinthu pafoni kapena patabuleti. Dr. Jean M. Twenge amene ndi katswiri woona za kaganizidwe ka anthu ananena kuti: “Ana omwe anazolowera kuwerenga nkhani pafoni kapena tabuleti ndipo amangodina linki kapena kuyendetsa chala pasikilini kuti apite patsamba lina, kuwerenga nkhani mu buku lochita kupulinta angakuone kukhala kotopetsa.” a

 Kuwerengera zinthu pafoni kapena patabuleti kuli ndi ubwino wake. Mnyamata wina wazaka 20 dzina lake John ananena kuti: “Kusukulu kwathu tinkawerenga mabuku pafoni kapena patabuleti. Kuti ndipeze zomwe ndikufuna mwachangu, ndinkagwiritsa ntchito kabokosi kofufuzira.”

 Kuwerenga nkhani pazipangizo zamakono kumaphweketsa zinthu. Mwachitsanzo, kungodina linki ina yake pachipangizo chako, ukhoza kupeza matanthauzo a mawu, kutsegula odiyo, kuonera vidiyo kapenanso kupeza mfundo zina zofunika pa nkhani yomwe ukuwerengayo. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti kuwerenga nkhani zochita kupulinta n’kosathandiza kwenikweni?

 Ena amaona kuti kuwerenga nkhani yochita kupulinta, kumawathandiza kuti aimvetse bwino. N’chifukwa chiyani zili choncho?

  •   Kusokonezedwa. Mnyamata wina dzina lake Nathan ananena kuti: “Ndikamawerenga nkhani pafoni kapena patabuleti, pasikilini pamakonda kubwera timauthenga tamalonda tomwe timandisokoneza kuti ndisaganizire kwambiri zomwe ndikuwerenga.”

     Mtsikana wina wazaka 20 dzina lake Karen, nayenso anafotokoza za vuto lomweli. Iye ananena kuti: “Ndikamawerenga pafoni kapena patabuleti, sindichedwa kusokonezeka. Ndimangopezeka kuti ndatsegulanso apu ina kapena kuyamba kusewera gemu.”

     Mfundo za m’Baibulo: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”​—Akolose 4:5.

     Zoti Muganizire: Kodi mwana wanu amatha kudziletsa kuti asaone zinthu zomwe zingamusokoneze panthawi yomwe akuwerenga pafoni kapena patabuleti? Ngati sichoncho, kodi mungamuthandize bwanji kuti asamasokonezeke ndi zinthu zina?

     Zimene Zingakuthandizeni: Thandizani mwana wanu kudziwa kuti kuyang’ana zinthu zina zomwe zabwera pasikilini, kumachititsa kuti awononge nthawi yambiri yomwe akanatha kuigwiritsa ntchito pa zinthu zina.

  •   Kumvetsa Nkhani: Buku lina linanena kuti: “Kafukufuku anasonyeza kuti zimakhala zovuta kuti anthu amvetse bwino nkhani akamaiwerengera pazipangizo zamakono poyerekezera ndi nkhani yochita kupulinta.”​—Be the Parent, Please.

     Chifukwa chimodzi ndi choti anthu omwe amawerengera nkhani pazipangizozi, amangowerenga nkhaniyo mothamanga koma saganizira zomwe akuwerengazo. Wolemba mabuku wina dzina lake Nicholas Carr ananena kuti: “Ukamawerenga nkhani pa intaneti, umafuna kupeza mfundo zambiri m’kanthawi kochepa.” b

     Nthawi zina kuwerenga mothamanga kumathandiza. Koma mogwirizana ndi zomwe Carr ananena, vuto ndi loti ukamawerenga mwanjira imeneyi “chimadzakhala chizolowezi.” Zotsatirapo zake ndi zakuti, mwana amayamba kuzolowera kuwerenga nkhani mongodutsa ndipo samvetsa zomwe wawerenga.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Pa zinthu zonse zimene upeze, upezenso luso lomvetsa zinthu.”​—Miyambo 4:7.

     Zoti Muganizire: Kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti azimvetsa zomwe akuwerenga, kaya zomwe akuwerengazo zili pazipangizo zamakono kapena papepala?

     Zimene Zingakuthandizeni: Muziona zinthu moyenera. Nkhani si yowerengera pachipangizo kapena papepala. Zonse zili ndi ubwino wake. Ndi zoona kuti zinthu zina za pazipangizo zikhoza kuthandiza munthu kumvetsa zomwe akuwerenga. Choncho ndi bwino kuona zinthu moyenera mukamafotokozera mwana wanu za ubwino ndi kuipa kwa njira iliyonse. Muzikumbukiranso kuti ana amasiyana.

  •   Kukumbukira Zomwe Mwawerenga: Poyerekezera zomwe zimachitika munthu akamawerenga nkhani pa zipangizo kapena yochita kupulinta, wolemba mabuku wina dzina lake Ferris Jabr, analemba m’buku lina kuti, kuwerenga pogwiritsa ntchito zipangizo ngati mafoni: “kumatopetsa ubongo ndipo munthu amavutika kukumbukira zomwe anawerenga.”​—Scientific American.

     Mwachitsanzo, kuwerenga m’buku lochita kupulinta kumathandiza pokumbukira zinthu moti ukhoza kukumbukira mbali ya tsamba pomwe unapezapo mfundo ina yake. Chimenechi chimakhala ngati chizindikiro chokuthandiza kukumbukira pomwe unapeza mfundoyo ngati utaifunanso nthawi ina.

     Kuwonjezera pamenepa, ochita kafukufuku anapeza kuti anthu amene amawerenga nkhani zochita kupulinta amamvetsa bwino zomwe awerenga. Amakumbukira zomwe awerenga chifukwa pa nthawi yomwe akuwerenga amakhala ngati akudziphunzitsa.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Usunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.”​—Miyambo 3:21.

     Zoti Muganizire: Ngati mwana wanu amavutika kumvetsa kapena kukumbukira zomwe wawerenga kapena kuphunzira, kodi mungamuthandize bwanji? Kodi mungamulimbikitse kuwerenga nkhani zochita kupulinta?

     Zimene Zingakuthandizeni: Muziganizira njira zophunzirira zomwe zingathandize mwana wanu m’malo mongoganizira zomwe amakonda. Anthu akhoza kuona kuti kuwerenga pogwiritsa ntchito zipangizo ngati mafoni ndi matabuleti ndiye kothandiza kwambiri.

a Kuchokera m’buku lakuti iGen.

b Kuchokera m’buku lakuti The Shallows.