Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

Kodi Mungatani Kuti Muzikhululukirana?

Kodi Mungatani Kuti Muzikhululukirana?

ZIMENE ZIMACHITIKA

Mukasemphana maganizo ndi mwamuna kapena mkazi wanu, mumayamba kumukumba zimene analakwitsa kalekale. Kodi vuto limakhala chiyani? N’kutheka kuti mmodzi wa inu kapena nonse awiri simukhululuka.

Koma n’zotheka kumakhululukirana. Choyamba tiyeni tione zimene zingapangitse anthu okwatirana kuti asamakhululukirane.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Kufuna kulamulira mnzawoyo. Anthu ena samakhululukira mwamuna kapena mkazi wawo chifukwa amafuna kuti azingomulamulira. Ndiye zimene zimachitika n’zakuti, awiriwa akasemphana maganizo pa nkhani ina, wolakwiridwayo amakumbutsa zimene mwamuna kapena mkazi wake anamulakwira n’cholinga choti alolere zimene iyeyo akufuna pa nkhani imene asemphana maganizoyo.

Kusunga chakukhosi. Pamatenga nthawi kuti munthu amene walakwiridwa aiwale zimene zinachitikazo. Nthawi zina wolakwiridwayo anganene kuti wakhululuka koma atasungabe chakukhosi, mwinanso kumaganiza zoti adzabwezere.

Ngati zimene timayembekezera sizinachitike. Anthu ena akakwatirana, amakhala ndi maganizo oti azingokondana nthawi zonse. Ndiye amati akasemphana maganizo amakhumudwa chifukwa amaona kuti zimene amayembekezera sizikuchitika. Zimenezi zingachititse kuti azingotolana zifukwa komanso asamakhululukirane.

Kusamvetsetsa. Anthu ambiri okwatirana sakhululukirana chifukwa amaganiza kuti akakhululukirana ndiye kuti:

Akuchepetsa nkhaniyo.

Ayenera kuiwala zimene zachitikazo.

Mnzawoyo akhoza kuwalakwiranso mwadala.

Koma zoona zake n’zakuti kukhululukirana sikutanthauza zimenezi. Komabe kukhululukirana sikophweka, makamaka pakati pa mwamuna ndi mkazi amene ndi okwatirana.

 ZIMENE MUNGACHITE

Muzimvetsa bwino tanthauzo la kukhululukirana. Nthawi zina Baibulo likamanena mawu akuti “kukhululuka” limatanthauza “kusiya.” Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi zina, munthu safunika kungoiwala kapena kuchepetsa cholakwacho. Angafunike kungoisiya nkhaniyo. Zimenezi zingapangitse kuti wolakwiridwayo komanso banja lake likhalebe losangalala.

Dziwani kuipa kosakhululukirana. Akatswiri ena amanena kuti kusunga chakukhosi kungapangitse kuti munthu azidwaladwala matenda monga kuthamanga kwa magazi komanso kuvutika maganizo. Kungabweretsenso mavuto ena m’banjamo. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.”—Aefeso 4:32.

Dziwani ubwino wokhululukirana. Mukamakhululukirana, simumakayikirana komanso simumasungirana chakukhosi. Zimenezi zimathandiza kuti muzikondana kwambiri.—Lemba lothandiza: Akolose 3:13.

Muzichita zinthu mozindikira. Anthu okwatirana savutika kukhululukirana akamakumbukira kuti onse amalakwitsa. Buku lina linanena kuti: “Munthu akamangoganizira zimene mnzake amalakwitsa, samaona zinthu zabwino zimene amachita. Kodi inuyo mungakonde kuganizira kwambiri ziti, zimene mnzanuyo amalakwitsa kapena zabwino zimene amachita?” (Fighting for Your Marriage) Muzikumbukira kuti aliyense amalakwitsa, ndi inu nomwe.—Lemba lothandiza: Yakobo 3:2.

Muzikhala ololera. Mwamuna kapena mkazi wanu akadzachitanso chinachake chokukhumudwitsani, mudzadzifunse kuti: ‘Kodi nkhaniyi ndi yaikulu? Kodi akufunikadi kundipepesa kapena ndikhoza kungoiwala?’—Lemba lothandiza: 1 Petulo 4:8.

Muzikambirana. Ngati mukuona kuti nkhaniyo ndi yaikulu, muzifotokoza modekha chimene chakukhumudwitsani. Muzipewa mawu osonyeza kuti mukumuweruza mnzanuyo kapena mukumukayikira chifukwa zimenezi zingachititse kuti ayambe kudziikira kumbuyo. Muzingofotokoza mmene zimene wachitazo zakukhudzirani.