Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Kodi Mungatani Ngati Mumasowa Wocheza Naye?

Kodi Mungatani Ngati Mumasowa Wocheza Naye?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

“Ndili ndi anzanga awiri, koma nthawi zina amakonda kuchitira limodzi zinthu zina, ine osandiuza. Nthawi zambiri ndimamva kuti anali limodzi kwinakwake ndipo anasangalala kwambiri. Tsiku lina ndinaimbira foni mnzanga winayo pa nthawi yomwe anali kwa mnzakeyo. Munthu wina ndiye anayankha foniyo ndipo ndinkawamva chapansipansi anzangawo akucheza komanso kuseka. Nditamva zimenezi, zinangowonjezera vuto langa loona kuti ndili ndekha ndipo ndikusowa wocheza naye.”—Maria. *

Kodi nanunso nthawi zina mumaona kuti mulibe wocheza naye? Kodi mumasirira anzanu akamachitira limodzi zinthu zina n’kumasangalala? Ngati ndi choncho, dziwani kuti m’Baibulo muli malangizo omwe angakuthandizeni. Komabe choyamba muyenera kudziwa zinthu zingapo zokhudza vuto losowa wocheza naye.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Pafupifupi aliyense nthawi zina amaona kuti alibe wocheza naye. Ngakhalenso anthu ena otchuka, nthawi zina amaona kuti akusowa wocheza naye kapena woti angamachitire naye limodzi zinthu zina n’kumasangalala. Kodi n’chiyani chimachititsa zimenezi? N’chifukwa choti kukhala ndi anzako ambiri pakokha sikuthetsa vutoli. Nkhani imagona poti, kodi anzakowo ndi mabwenzi apamtima oti umatha kuuzana nawo zakukhosi komanso kuchitira limodzi zinthu zosangalatsa? Munthu wotchuka, nthawi zambiri pomwe ali pamakhalanso anthu ambiri. Koma n’kutheka kuti munthu wotereyu alibe anzake apamtima, choncho angathe kumasowa wocheza naye.

Kusowa ocheza nawo kungasokoneze thanzi lanu. Zotsatira za kafukufuku wina zinasonyeza kuti anthu amene nthawi zambiri amangokhala okhaokha, akhoza kumwalira msanga poyerekeza ndi anthu amene amacheza ndi kusangalala ndi anzawo. Kafukufukuyu anasonyezanso kuti vuto losowa ocheza nawo ndi loopsa ku thanzi la munthu “kuposa vuto lokhala wonenepa kwambiri.” Komanso “kusowa ocheza nawo kumasokoneza thanzi la munthu mofanana ndi mmene zimakhalira ndi munthu yemwe amasuta ndudu 15 pa tsiku.”

Kusowa ocheza nawo kungachititse kuti muyambe kucheza ndi anthu olakwika. Vutoli lingachititse kuti muyambe kucheza ndi aliyense amene angapezeke. Mnyamata wina, dzina lake Alan, anati: “Mukamaona kuti mumangokhala nokhanokha ndipo mumasowa wocheza naye, mungayambe kucheza ndi aliyense amene wasonyeza zoti akufuna kuti mukhale mnzake. Mungamaganize kuti: ‘Kuli bwino kucheza ndi aliyense amene wapezeka kusiyana ndi kukhala wopanda wocheza naye.’ Zimenezi zingakugwetsereni m’mavuto.”

Si nthawi zonse pamene zipangizo zamakono zingathetse vuto losowa wocheza naye. Mtsikana wina, dzina lake Natalie, anati: “Ukhoza kulembera anthu ambiri maimelo kapena mameseji, koma n’kumaonabe kuti ukusowa wocheza naye.” Mtsikana wina, dzina lake Tyler amaonanso choncho. Iye anati: “Kulemberana mameseji kuli ngati kudya tizakudya totolatola monga mabisiketi kapena maswiti. Koma kukhala ndi munthu n’kumacheza naye kapena kuchitira naye limodzi zosangalatsa, kuli ngati kudya chakudya monga nsima kapena mpunga. Tizakudya totolatola ndi tabwino, komabe kuti ukhute umafunika chakudya chogwira pamimba.”

ZIMENE MUNGACHITE

Musafulumire kuganiza kuti anzanu akukusalani. Tiyerekeze kuti mwaona zithunzi za anzanu, zomwe anajambulitsa ali kuphwando linalake koma inuyo sanakuitaneni kuphwandolo. Popeza simukudziwa zonse zomwe zinachititsa kuti asakuitaneni, si bwino kufulumira kuganiza kuti ayamba kukusalani. M’malomwake, yesani kuganizira zinthu zabwino, zomwe mwina zinachititsa kuti asakuitaneni. Choncho vuto loona kuti ulibe wocheza naye likhoza kukula kapena kuchepa, malinga ndi mmene ukuonera zinthu.—Lemba lothandiza: Miyambo 15:15.

Musamakokomeze vuto lanu. Mukayamba kuona kuti mukusowa ocheza nawo, mungaganize kuti: ‘Kukakhala zosangalatsa, anthu sandiitana. Kapena mungaganize kuti, ‘Anthu safuna kucheza nane.’ Maganizo okokomeza amenewa angangochititsa kuti vuto lanu loona kuti mumasowa wocheza naye likule. Zikatere mumayamba kudzipatula chifukwa mumaona ngati anthu samakukondani. Komatu, kudzipatula kungangowonjezera vuto lanu.—Lemba lothandiza: Miyambo 18:1.

Muzichezanso ndi anthu aakulu kuposa inuyo. M’Baibulo muli nkhani ya Davide, yemwe ali mnyamata anadziwana ndi Yonatani. Yonatani anali wamkulu kwambiri poyerekeza ndi Davide chifukwa ankasiyana zaka 30. Koma ngakhale zinali chonchi, Davide ndi Yonatani anayamba kugwirizana moti anakhala mabwenzi apamtima. (1 Samueli 18:1) Izi zikusonyeza kuti nanunso mungathe kukhala ndi anzanu aakulu kuposa inuyo. Mtsikana wina, wazaka 21 dzina lake Kiara, anati: “Ndimaona kuti kukhala ndi anzako aakulu kuli ndi ubwino wake. Ineyo ndili ndi anzanga aakulu kwambiri kuyerekeza ndi ineyo. Anzangawa amandithandiza chifukwa amadziwa zambiri komanso ndi odalirika.”—Lemba lothandiza: Yobu 12:12.

Dziwani kuti kukhala pawekha kuli ndi ubwino wake. Anthu ena akangokhala paokha, amayamba kuona kuti akusowa wocheza naye. Koma nthawi zina kukhala pawekha kuli ndi bwino wake. Mwachitsanzo, Yesu ankakonda kucheza ndi anthu komanso kuchita nawo zinthu zosangalatsa. Koma ankadziwanso ubwino wokhala yekha. (Mateyu 14:23; Maliko 1:35) Inunso mukakhala nokha, muziona kuti mungathe kugwiritsa ntchito nthawi imeneyo kuganizira zinthu zimene Mulungu wakuchitirani. Zimenezi zingathandizenso kuti anthu ena ayambe kufuna kuti mukhale mnzawo.—Miyambo 13:20.

^ ndime 4 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.