Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA

Kodi Tiyambe Kukhala Limodzi Tisanakwatirane?

Kodi Tiyambe Kukhala Limodzi Tisanakwatirane?

 Anthu ambiri amayamba kukhala limodzi asanakwatirane. Ena amachita zimenezi poganiza kuti ziwathandiza kudziwa ngati ali oyenerana komanso amaganiza kuti kuchita zimenezi kungawathandize kuti adzakhale ndi banja losangalala. Kodi ndi nzeru kuyamba kukhala limodzi musanakwatirane?

Munkhaniyi muli

 Kodi Baibulo limanena zotani?

  •   Baibulo silivomereza kuti anthu azigonana asanakwatirane. Mwachitsanzo, limati: “Muzipewa chiwerewere.” (1 Atesalonika 4:3; 1 Akorinto 6:18) Zimenezi zikuphatikizapo kugonana kwa mwamuna ndi mkazi amene akukhala limodzi ngakhale ali ndi cholinga chodzakwatirana. a Mfundo za m’Baibulozi zimateteza anthu kuti apewe kukhala ndi mimba asanakwatirane komanso mavuto ena amene amabwera chifukwa choyamba kukhala limodzi asanakwatirane.

  •   Mulungu ndi amene anayambitsa banja. Pa nthawi imene ankayambitsa banja loyamba, ananena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa mkazi wake ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Ngati mwamuna ndi mkazi akwatirana kaye movomerezeka asanayambe kukhala limodzi, zimathandiza kuti banja lawo likhale lolimba komanso kuti azikondana kwambiri.

 Kodi kukhala limodzi musanakwatirane kungakuthandizeni kukonzekera moyo wa m’banja?

 Ena amaganiza choncho. Amaganiza kuti amaphunzira zambiri akamathandizana kugwira ntchito zapakhomo komanso akamaona mmene mnzawo akuchitira zinthu. Komabe, anthu amafunika kuchita kaye mgwirizano wa ukwati kuti banja lawo likhale losangalala.

 N’chiyani chingathandize mwamuna ndi mkazi kuti apitirize kukhala limodzi kwa moyo wawo wonse, kaya pa nthawi yabwino kapena yovuta? Sikuti ayenera “kuyeserera kaye kukhala limodzi” kenako n’kusiyana akaona kuti sakuyenererana. M’malomwake, aliyense ayenera kuyesetsa kumachita zinthu mogwirizana ndi mnzake komanso kupezera limodzi njira zothetsera mavuto alionse amene angakumane nawo.

 Mfundo yofunika kwambiri: M’malo mokonzekera kudzakhala ndi banja labwino, anthu amene amasankha kukhala limodzi asanakwatirane, amakhala akukonzekera kudzapatukana.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”​—Agalatiya 6:7.

 Kodi kukhala limodzi kungakuthandizeni kuti musamawononge ndalama?

 Ena amaona kuti n’zimene zingawathandize. Pakafukufuku wina amene anachitika ndi bungwe lina (Pew Research Center) la ku United States, panapezeka kuti pa anthu 10 alionse amene ankakhala limodzi asanakwatirane, anthu 4 ankachita zimenezi chifukwa choganiza kuti ziwathandiza kuti asawononge ndalama. Komabe, pambuyo pokhala limodzi kwa nthawi ndithu, ambiri ananena kuti sanakonzekere kukwatirana chifukwa cha mavuto okhudzana ndi ndalama.

 Kukhala limodzi anthu asanakwatirane kumabweretsanso mavuto ena makamaka kwa mkazi. Mwachitsanzo, chibwenzi chikatha, azimayi ndi amene amakhala ndi udindo wolera ana.

 Mfundo yofunika kwambiri: Mavuto amene amabwera chifukwa chokhalira limodzi anthu asanakwatirane amakhala aakulu kuposa ubwino umene anthu amayembekezera.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, Amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.”​—Yesaya 48:17.

 Kodi kukhala limodzi kungakuthandizeni kuti mupewe kukwatirana ndi munthu wolakwika?

 Anthu ena amanena kuti zimenezi n’zothandiza. Komabe, buku lina linanena kuti, “Nthawi zambiri anthu amene amakhala limodzi asanakwatirane samazindikira kuti kuchita zimenezi kungawachititse kuti avutike kuthetsa chibwenzi.” N’chifukwa chiyani zimenezi zili choncho? Anthu ena amadzazindikira kuti sakumvana ngakhale pang’ono. Koma amangokhalabe limodzi chabe chifukwa choti pali zinthu zina zimene akhala akuchitira limodzi monga kusamalira chiweto, kusainira mapepala a nyumba, kapenanso ngati akuyembekezera mwana. Bukuli lija linanenanso kuti, “Anthu ena omwe akanatha kuthetsa chibwenzi amangokwatirana chifukwa choti angozolowera b ndipo akuona kuti bola kungopitiriza kukhala limodzi.”​—Fighting for Your Marriage

 Mfundo yofunika kwambiri: M’malo mokuthandizani kusankha munthu woyenerera, kukhala limodzi musanakwatirane kungachititse kuti muvutike kuthetsa chibwenzi ndi munthu woti si woyenerera.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala, koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto.”​—Miyambo 22:3.

 Kodi mungasankhe njira ina yabwino?

 Mungatani kuti mupewe mavuto amene amabwera chifukwa chokhala limodzi musanakwatirane? Nanga n’chiyani chingakuthandizeni kudzakhala ndi banja labwino? Muziyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza ukwati. Yesetsani kudziwana bwino ndi munthu amene mukuyembekezera kudzakwatirana naye musanayambe kukhala limodzi. Anthu amasankha bwino munthu woti adzakwatirane naye poganizira zinthu zofunika monga mfundo za makhalidwe zimene amayendera komanso zimene amakhulupirira osati chifukwa chongokopeka kuti mungasangalale kumagonana naye.

 M’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni kukhala ndi banja losangalala komanso lolimba. c Mwachitsanzo, muli mfundo zomwe zingakuthandizeni . . .

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza nkhani zimenezi, onani gawo lakuti “Anthu Okwatirana Komanso Mabanja” pa jw.org.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi othandiza pophunzitsa.”​—2 Timoteyo 3:16.

b Kuchokera munkhani yakuti, “Sliding Versus Deciding: Inertia and the Premarital Cohabitation Effect,” by Scott M. Stanley, Galena Kline Rhoades ndi Howard J. Markman, yomwe inatulutsidwa m’buku Family Relations.

c Mu zikhalidwe zina, makolo ndi amene amasankhira ana awo munthu woti akwatirane naye. Ngati zili choncho, Baibulo lingathandize makolo kudziwa makhalidwe amene afunika kuona mwa munthu woti akwatirane ndi mwana wawo.