Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Mmene Mungathandizire Ana Anu Akamalephera Zinazake

Mmene Mungathandizire Ana Anu Akamalephera Zinazake

 Nthawi zina ana anu akhoza kukhumudwa chifukwa cholephera kuchita zinthu zina kapenanso kulakwa kusukulu. Ndiye kodi mungawathandize bwanji kuti zinthu ziyambe kuwayendera bwino?

 Zimene muyenera kudziwa

 Tonse timalephera zinthu zina. Baibulo limanena kuti “tonsefe timapunthwa.” (Yakobo 3:2) Nawonso ana amalephera kuchita zinthu zina. Komabe, mwana akalakwitsa zinazake zimamuthandiza kuti aphunzire mmene angamathetsere mavuto. Ana sabadwa ndi luso lothetsera mavuto, amachita kuphunzira. Mayi wina dzina lake Laura ananena kuti: “Ine ndi mwamuna wanga timaona kuti ana akalakwitsa zinazake ndi bwino kuwasiya kuti adziwe zoyenera kuchita kuti akonze zinthu, m’malo moti azichita zinthu ngati kuti sanalakwitse chilichonse. Izi zimawathandiza kuti azitha kupirira ngati zinthu zitavuta.”

 Ana ambiri amadandaula kwambiri akalephera zinazake. Ana ena sadziwa zoyenera kuchita akalakwitsa zinthu chifukwa choti makolo awo amakonda kuwaikira kumbuyo. Mwachitsanzo, mwana akalakwa kusukulu, makolo ena amafulumira kuimba mlandu mphunzitsi wake. Ndiponso ngati mwana wayambana ndi mnzake, makolo ake amathamangira kuloza chala mnzakeyo.

 Ndiyeno funso ndi lakuti, ngati makolo amaikira kumbuyo ana awo komanso sawauza mavuto omwe angakumane nawo, kodi anawo angaphunzire bwanji kuvomereza akalakwitsa zinazake?

 Zimene mungachite

  •   Muzithandiza ana anu kudziwa kuti zimene amachita zimakhala ndi zotsatirapo zake.

     Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—Agalatiya 6:7.

     Ana amafunika kudziwa kuti zonse zimene timachita zimakhala ndi zotsatirapo zake. Tikawononga chinthu, pamafunika nthawi komanso ndalama kuti chikonzedwenso. Ndipo zilizonse zimene talakwitsa zimakhala ndi mavuto ake. Amafunika kudziwa kuti ngati atathandizira kuchita zinazake zolakwika, ndiye kuti zotsatirapo zake ziwakhudzanso iwowo. Choncho, ana anu akalakwitsa zinthu musamaimbe mlandu anthu ena kapena kupeza zifukwa zowaikira kumbuyo. Muzilola kuti akumane ndi zotsatirapo za zomwe achitazo mogwirizana ndi msinkhu wawo. Komabe mwanayo azitha kumvetsa kugwirizana kwa zomwe walakwitsa ndi zotsatirapo zake.

  •   Muzithandiza ana anu kudziwa zoyenera kuchita zinthu zikalakwika.

     Lemba lothandiza: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.”—Miyambo 24:16.

     Kulakwitsa zinthu n’kopweteka, koma si mapeto a zonse. Choncho muzithandiza ana anu kuti aziganizira kwambiri zopeza njira yokonzera zomwe alakwitsazo m’malo moti azingokhalira kudandaula. Mwachitsanzo, ngati mwana wanu walakwa mayeso kusukulu, muzimulimbikitsa kuti aziwerenga kwambiri n’cholinga choti adzakhoze ulendo wotsatira. (Miyambo 20:4) Ngati mwana wanu wasemphana maganizo ndi mnzake, muthandizeni kudziwa zomwe angachite kuti athetse nkhaniyo mwamtendere, ngakhale kuti wolakwa si iyeyo.—Aroma 12:18; 2 Timoteyo 2:24.

  •   Muziphunzitsa ana anu kuti asamadzione ngati ofunika kwambiri kuposa ena.

     Lemba lothandiza: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.”—Aroma 12:3.

     Mwana wanu akachita bwino pa zinthu zina, si nzeru kumupangitsa kuganiza kuti ndi wofunika kwambiri kuposa wina aliyense. Ndipotu ngakhale ana anzeru kwambiri kusukulu, samakhoza bwino nthawi zonse. Ana amenenso amasewera bwino masewera enaake, samawina nthawi zonse. Ana odzichepetsa samavutika kupeza njira yothetsera vuto akalakwitsa zinazake.

     Baibulo limanena kuti mayesero akhoza kutithandiza kukhala olimba komanso opirira. (Yakobo 1:2-4) Choncho ngakhale kuti ana amakhumudwa akalakwitsa kapena kulephera zinazake, muziwathandiza kuti asamabise zomwe zachitikazo komanso kuti asamadzione kuti ndi olephera.

     Kuphunzitsa ana kuti akhale opirira n’chimodzimodzi ndi kuwaphunzitsa luso linalake. Pamafunika nthawi yokwanira komanso khama. Koma anawo akakula zimadzawathandiza kuti azitha kupirira akakumana ndi mavuto. Buku lina limanena kuti: “Achinyamata amene amakwanitsa kupirira akapanikizika, safulumira kuchita zinthu zomwe zingawaike m’mavuto. Zinthu zimawayenderabe bwino ngakhale atakumana ndi zomwe samaziyembekezera.” Ndipotu mwana akakhala wopirira, zimadzamuthandiza akadzakula.—Letting Go With Love and Confidence.

 Zimene zingakuthandizeni: Muzikhala chitsanzo kwa ana anu. Muzikumbukira kuti mmene inuyo mumachitira zinthu mukakumana ndi zinthu zokhumudwitsa, zingathandizenso anawo kudziwa zimene angachite ngati atakumana ndi zoterozo.