Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa

Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa

 Bambo wina dzina lake Alexander ananena kuti: “Pamene mwana wathu wamkazi anali ndi zaka 6, tinakambirana naye koyamba nkhani ya mowa. Koma tinadabwa kwambiri kuona kuti akudziwa zambiri zokhudza mowa zomwe sitinkayembekezera.”

 Zimene muyenera kudziwa

 Kukambirana ndi ana anu zokhudza mowa n’kofunika.Musamadikire kuti mwana wanu akule kaye kuti mudzakambirane naye za nkhaniyi. Bambo wina wa ku Russia dzina lake Khamit ananena kuti: “Ndimaona kuti sitinachite bwino kumulekerera mwana wathu osamuuza zokhudza mowa pa nthawi imene anali wamng’ono. Ndinazindikira kuti anali atayamba kale kumwa kwambiri ali ndi zaka 13. Ndinaphunzirapo kanthu koma zinthu zinali zitaipa kale.”

 N’chifukwa chiyani kukambirana ndi mwana za nkhaniyi n’kofunika?

  •   Anzake a kusukulu, otsatsa malonda komanso zimene amaona pa TV zingachititse mwana wanu kusintha mmene amaonera nkhani ya kumwa mowa.

  •   Kafukufuku amene bungwe lina ku United States linachita, anasonyeza kuti pa ana aang’ono 100, pali 11 omwe amamwa mowa.​—U.S. Centers for Disease Control and Prevention.

 Mpake kuti akuluakulu a zaumoyo amanena kuti makolo ayenera kuphunzitsiratu ana awo adakali aang’ono za kuopsa kwa mowa. Tiyeni tione mmene makolo angathandizire ana awo.

 Zimene mungachite

 Muzikhala okonzeka kuyankha mafunso omwe mwana wanu angafunse. Ana amakhala ndi mtima wofuna kudziwa zinthu ndipo akamakula amafunanso kudziwa zambiri. Choncho mumafunika kukonzekereratu mmene mungawayankhire. Mwachitsanzo:

  •   Ngati mwana wanu akufuna kudziwa mmene mowa umamvekera, mungamuuze kuti pali mowa wina umawawasirako pomwe wina umawawa kwambiri.

  •   Ngati mwana wanu akufuna kulawako mowa, mungamuuze kuti mowa si wabwino kwa ana. Mwachitsanzo, n’zoona kuti munthu akamwako mowa amasangalala komanso amamasuka. Koma akaumwa mopitirira malire, amapanga chizungulire, saganiza bwinobwino pochita zinthu ndiponso amachita kapena kulankhula zinthu zomwe kenako amadzanong’oneza nazo bondo.​—Miyambo 23:29-35.

 Muzidziwiratu zokhudza mowa. Baibulo limanena kuti: “Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira.” (Miyambo 13:16) Choncho muyenera kufufuza ndi kudziwiratu mavuto amene amakhalapo munthu akamwa, zimene malamulo a m’dziko lanu amanena pa nkhani ya mowa ndiponso kuchuluka kwa mowa womwe munthu amayenera kumwa. Mukadziwa zimenezi simungavutike kuthandiza mwana wanu.

 Muziyamba ndi inuyo kukambirana ndi mwana wanu zokhudza mowa. Bambo wina wa ku Britain dzina lake Mark ananena kuti: “Mowa umasokoneza kwambiri ana. Tsiku lina ndinafunsa mwana wanga wamwamuna wa zaka 8 kuti afotokozepo maganizo ake ngati kumwa mowa n’kwabwino kapena ayi. Ndinkalankhula naye momasuka ngati kuti tikungocheza ndipo zimenezi zinathandiza kuti nayenso amasuke kunena maganizo ake pa nkhani ya mowa.”

 Ngati nthawi zambiri mumakonda kunena za mavuto amene amakhalapo chifukwa cha mowa, zingathandize ana anu kudziwa kuopsa kwa mowa. Choncho potengera msinkhu wa mwana wanu, mukamakambirana nkhani zofunika pa moyo monga kupewa ngozi pamsewu komanso nkhani zokhudza kugonana, mungakambirane nayenso zokhudza kuopsa kwa mowa.

 Muzikhala chitsanzo chabwino. Ana ali ngati thonje. Thonje likaviikidwa m’madzi, kaya akuda kapena oyera, limayamwa komanso kutengera mtundu wa madziwo. Ochita kafukufuku anapeza kuti nawonso ana amatengera kwambiri zimene makolo awo amakonda kuchita. Izi zikutanthauza kuti ngati inuyo mumaona kuti kumwa mowa ndi njira yokhayo yabwino yochepetsera nkhawa kapena mavuto anu, mwana wanunso amatengera zomwezo. Choncho muzikhala chitsanzo chabwino. Ndipo ngati mumamwa, muziyesetsa kumwa moyenera.

Ana anu amatengera zimene mumachita pa nkhani ya kumwa mowa