Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Kodi Mungatani Kuti Musamangotengera Zochita za Anzanu?

Kodi Mungatani Kuti Musamangotengera Zochita za Anzanu?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

“Ndili ku pulayimale, anthu ambiri sankakonda kucheza nane, ndipo zimenezi zinkandikwana kwabasi. Choncho nditayamba kuphunzira ku sekondale, ndinasintha khalidwe langa labwino komanso mmene ndinkaonekera. Ndinachita zimenezi chifukwa ndinkafuna kupeza anthu ocheza nawo, moti ndinayamba kumangoterengera zochita za anzanga n’cholinga choti azindikonda.”—Jennifer, wazaka 16. *

Kodi inunso anzanu amakukakamizani kuti muzingochita zofuna zawo? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani kudziwa zoyenera kuchita.

Mukalolera kuchita zoipa zimene anzanu akufuna kuti muchite, mumakhala ngati chidole chifukwa mumangoyendera zimene anzanuwo akufuna. Musalole kuti anzanu azingokusankhirani zochita.—Aroma 6:16.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Munthu akhoza kuyamba kuchita zoipa chifukwa chotengera zochita za anzake.

“Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akorinto 15:33.

“Umatha kudziwa kuti izi n’zolakwika, koma anzako akayamba kukukakamiza kuti uchite zimenezo, umagonja n’kuyamba kuchita zinthu pongofuna kuwasangalatsa.”—Dana.

Munthu amathanso kukakamizidwa ndi mtima wake kuti achite zoipa.

“Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.”—Aroma 7:21.

“Nthawi zambiri ineyo ndimakhalanso ndikufuna kuchita zimene anzanga akukambirana, zomwe zimaoneka kuti ndi zosangalatsa kwambiri kuzichita.”—Diana.

Munthu amakhala wosangalala akakana kuchita zoipa.

“Khalani ndi chikumbumtima chabwino.”—1 Petulo 3:16.

“Poyamba zinkandivuta kuti ndikane kuchita nawo zimene anzanga akuchita poopa kuti azindiona kuti ndine wotsalira. Koma panopa sindichitanso mantha ndi zimenezi chifukwa ndikudziwa zimene ndikuchita. Ndimaona kuti ndimakhala wosangalala kwambiri ndikamadziwa kuti sindinachite chinachake cholakwika.”—Carla.

 ZIMENE MUNGACHITE

Anzanu akamakukakamizani kuti muchite zinazake zoipa, yesani kuchita izi:

Ganizirani zotsatira zake: Dzifunseni kuti, ‘Kodi zingakhale bwanji ngati nditalola kuchita zoipazi kenako n’kugwidwa? Kodi makolo anga adzandiganizira zotani akamva zimenezi? Nanga ineyo ndidzamva bwanji?’—Lemba lothandiza: Agalatiya 6:7.

“Makolo anga amandifunsa funso ngati lakuti, ‘Kodi ukuganiza kuti chingachitike n’chiyani ngati utalola kuchita zoipa zomwe anzako akufuna?’ Amandithandiza kuona kuti kumangotengera zochita za anzanga kungandigwetsere m’mavuto.”—Olivia.

Ganizirani kufunika kwa zomwe mumakhulupirira. Dzifunseni kuti, ‘N’chifukwa chiyani ndimaona kuti kuchita zimenezi kungandibweretsere mavuto ineyo kapena anthu ena?’—Lemba lothandiza: Aheberi 5:14.

“Ndili mwana, anzanga akamandikakamiza kuchita zoipa, ndinkangonena kuti, ayi, kapena ndinkangonena mawu ochepa osonyeza kukana. Koma tsopano ndimafotokoza chifukwa chimene ndikukanira kuchita zimenezo. Panopa ndimadziwa chifukwa chimene ndimakanira kuchita zoipa. Zimene ndimanenazo ndi zimene ineyo ndimakhulupirira, osati zoti munthu wina wachita kundiuza.”—Anita.

Ganizirani mbiri yanu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimafuna kuti ndizidziwika kuti ndine munthu wotani?’ Ndiye ganiziraninso zimene anzanu akufuna kuti muchitezo n’kudzifunsa kuti, ‘Munthu amene akufuna kudziwika ndi mbiri imeneyi angatani atakumana ndi vuto limeneli?’—Lemba lothandiza: 2 Akorinto 13:5.

“Ndimaona kuti ndimachita zoyenera, choncho sindidandaula kwambiri ndi zimene anthu ena anganene zokhudza ineyo. Komanso anthu sasangalala akadziwa kuti zimene munthu akuchita si zochokera pansi pa mtima koma akungochita kuti awasangalatse.”—Alicia.

Muziganizira za m’tsogolo. Achinyamata ena akakhala kusukulu, amatengera zochita za anzawo pofuna kuwasangalatsa. Koma pakangopita zaka zingapo kapenanso miyezi, amaiwalana ndi anzawowo ndipo sadziwa n’komwe kuti ali kuti.

“Ndikayang’ana chithunzi cha kusukulu, sindikumbukira n’komwe mayina a anthu ena amene ndinali nawo m’kalasi imodzi. Koma pa nthawi imene ndinkacheza nawo kusukulu, ndinkaona ngati maganizo awo ndi ofunika kwambiri kuposa kutsatira zimene ndimakhulupirira. Ndimaona kuti ndinkachita zopusa kwambiri.”—Dawn, yemwe panopa ali ndi zaka 22.

Muzikonzekera. Baibulo limati: “Mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.”—Akolose 4:6.

“Makolo anga ankandithandiza ineyo ndi mchemwali wanga kuganizira zimene tingachite titakumana ndi vuto linalake.Izi zinkathandiza kuti tidziwe zochita tikakumanadi ndi vutolo.”—Christine.

^ ndime 4 Tasintha maina ena m’nkhaniyi.