Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Muziphunzitsa Ana Anu Kukhala ndi Mtima Woyamikira

Muziphunzitsa Ana Anu Kukhala ndi Mtima Woyamikira

 Ochita kafukufuku anapeza kuti anthu omwe ali ndi mtima woyamikira, amakhala osangalala, athanzi, amakhala bwino ndi anzawo komanso amapirira akakumana ndi mavuto. Wochita kafukufuku wina dzina lake Robert A. Emmons ananena kuti kukhala ndi mtima woyamikira “kumateteza munthu kuti asakhale ndi makhalidwe oipa ngati nsanje, kusunga zifukwa, umbombo komanso ukali.” a

 Kodi ana amapindula bwanji akakhala ndi mtima woyamikira? Kafukufuku wina amene anachitika kwa zaka 4 pa achinyamata okwana 700, anapeza kuti achinyamata omwe anali ndi mtima woyamikira, analibe maganizo ofuna kubera mayeso, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuledzera kapena kukhala ndi maganizo aliwonse ofuna kuvulaza anthu ena.

  •   Mwana akamaona kuti zinthuzo ndi zake ndi kale amakhala wosayamika. Ana ambiri akapatsidwa zinthu zabwino, amaona kuti amayenera kale kupatsidwa zinthuzo. Munthu akamaona zinthu zomwe wapatsidwa kukhala ngati malipiro, osati monga mphatso, zimakhala zovuta kuti athokoze.

     Masiku ano anthu ambiri ali ndi maganizo amenewa. Mayi wina dzina lake Katherine ananena kuti: “Dzikoli limaphunzitsa kuti munthu ayenera kupeza chilichonse chomwe akufuna.” Mayiyu ananenanso kuti, “Ofalitsa nkhani amafalitsa zithunzi za zinthu zosiyanasiyana kudzera m’magazini, pa TV komanso pa intaneti ndipo amalimbikitsa anthu kuti agule zinthuzo chifukwa akuyenera kukhala nazo.”

  •   Mwana angaphunzire kukhala woyamikira adakali wamng’ono. Mayi wina dzina lake Kaye anati, “Ana savuta kuwaphunzitsa. Kuphunzitsa mwana makhalidwe abwino adakali wamng’ono, kuti ngati kuimikira mbewu timitengo kuti ikule mowongoka.”

Mmene mungaphunzitsire mwana wanu kukhala ndi mtima woyamikira

  •   Muphunzitseni zomwe anganene. Ngakhale ana aang’ono akhoza kuphunzira kunena kuti zikomo, munthu wina akawapatsa chinthu kapena kuwachitira zabwino. Akamakula, amakhala ndi mtima woyamikira anthu ena chifukwa cha zomwe awachitira.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”—Akolose 3:15.

     “Kamdzukulu kathu kazaka zitatu kamakonda kuthokoza ponena kuti ‘zikomo.’ Komanso amapempha zinthu mwaulemu osati ngati kuti akulamula. Anaphunzira zimenezi kwa makolo ake. Zochita zawo komanso zomwe amalankhula, zamuphunzitsa kuti nayenso aziyamikira anthu ena.”—Jeffrey.

  •   Muziwaphunzitsa zomwe angachite. Munthu wina akadzapatsa ana anu mphatso, mudzawaphunzitse mmene angadzalembere meseji yothokoza. Chinanso n’chakuti, mukamapatsa ana anu ntchito zapakhomo, amamvetsa kuti pamakhala ntchito yaikulu kuti chilichonse pakhomo chiziyenda bwino.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.

     “Ana athu awiri amatithandiza kuphika komanso kugwira ntchito zapakhomo. Zimenezi zimawathandiza kumvetsa kukula kwa ntchito yomwe makolofe timakhala nayo komanso kuyamikira zomwe timachita.”—Beverly.

  •   Aphunzitseni khalidwe labwino. Tingayerekezere mtima woyamikira ndi mbewu yomwe yadzalidwa mudothi lomwe ndi mtima wodzichepetsa. Munthu wodzichepetsa amadziwa kuti zinthu zimamuyendera bwino akamalola kuti anthu ena amuthandize. Zimenezi zimamuchititsa kuti azithokoza anthu omwe amuthandizawo.

     Mfundo ya m’Baibulo: ‘Modzichepetsa, muziona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.’—Afilipi 2:3, 4.

     “Nthawi ina tikamadya chakudya chamadzulo, timakhala ndi ‘nthawi yoyamikirana.’ Aliyense amapatsidwa mpata woti afotokoze zinthu zomwe akuyamikira. Zimenezi zimathandiza kuti aliyense aziganizira zinthu zabwino ndi zolimbikitsa osati zongokomera iyeyo.”—Tamara.

 Zomwe mungachite: Muziwapatsa chitsanzo. Ana angaphunzire mosavuta kukhala oyamikira akamakumvani mukuyamikira anthu ena komanso mukamawayamikira pa zomwe achita.

a Kuchokera m’buku lakuti Thanks! How Practicing Gratitude Can Make You Happier.