Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Phunzitsani Ana Anu Kuti Akhale Odziletsa

Phunzitsani Ana Anu Kuti Akhale Odziletsa

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekeze kuti mwana wanu wazaka 6 sadziletsa ngakhale pang’ono. Akaona chimene chimamusangalatsa amafuna kuti mumupatse pompopompo. Akakwiya, amakalipa koopsa. Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi ana onse amatere, kapena wangayu ali ndi vuto? Kodi adzasintha yekha m’tsogolo kapena ndiyambepo kumuphunzitsa kuti akhale wodziletsa?’

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Anthu ambiri masiku ano ndi osadziletsa. Katswiri wina analemba kuti: “Masiku ano, ana ndi akulu omwe sadziletsa akafuna kuchita chilichonse. Anthu ambiri, ngakhale amene amafuna kuthandiza anzawo, amalimbikitsa mtima wosadziletsa.” *

Muyambe kuwaphunzitsa ali aang’ono. Anthu ena ochita kafukufuku anatenga kagulu ka ana azaka 4 n’kupereka switi imodzi kwa aliyense. Ndiyeno anawauza kuti akadya nthawi yomweyo, adzangodya imodzi yokhayo koma akadikira pang’ono adzawapatsa switi ina. Akatswiriwo anapeza kuti anawo atamaliza sukulu, amene anali odziletsa kuyambira pa nthawi imene anali ndi zaka 4 anali anthu olongosoka ndipo ankakhoza bwino koma amene sankadziletsa zinthu sizinawayendere bwino.

Ngati simuwaphunzitsa pamakhala mavuto aakulu. Ochita kafukufukuwo anapeza kuti zimene zimachitika pa moyo wa mwana zimakhudza kaganizidwe kake. Katswiri wina analemba kuti: “Ngati tilekerera ana, osawaphunzitsa kudikira ndiponso kupirira, n’kumangowapatsa chilichonse pa nthawi imene afuna, anawo amakhala opanda khalidwe.” *

ZIMENE MUNGACHITE

Inuyo mukhale chitsanzo chabwino. Kodi inuyo mumatani pa nkhani yodziletsa? Tiyerekeze kuti muli pamzere wodikira zinazake, kodi mwana wanu amakuonani mukukwiya kapena kulowerera anzanu? Nanga mukamacheza ndi anzanu, kodi amakuonani mukuwadula mawu? Dr Kindlon analembanso kuti: “Ifeyo tikakhala odziletsa ana athu amatengera chitsanzo chathu.”—Mfundo ya m’Baibulo: Aroma 12:9.

Azidziwa kuti zimene amachita zimakhala ndi zotsatirapo. Malinga ndi misinkhu yawo, muziwathandiza kudziwa ubwino wodziletsa ndiponso mavuto amene amabwera chifukwa chosadziletsa. Mwachitsanzo, mwana wanu akakwiya chifukwa cha zimene mnzake wachita, muzimuuza kuti aziyamba wadzifunsa kuti: ‘Kodi ndikabwezera zinthu ziyenda kapena ayi?’ Mwina angachite bwino kuwerenga kaye 1 mpaka 10 asanachite chilichonse podikira kuti mtima wake ukhale m’malo. Apo ayi, mwina ndi bwino kungochokapo.—Mfundo ya m’Baibulo: Agalatiya 6:7.

Muziwalimbikitsa. Ana anu akamadziletsa muziwayamikira. Muziwauza kuti kudziletsa n’kovuta ndipo munthu akakwanitsa ndiye kuti ndi wanzeru. Paja Baibulo limati: “Munthu wosaugwira mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa, n’kuusiya wopanda mpanda.” (Miyambo 25:28) Koma limanenanso kuti: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.”—Miyambo 16:32.

Muziyeserera. Muzichita nawo timasewero tokhudza mayesero amene angakumane nawo. Muziyeserera kuchita zinthu zosiyanasiyana zimene munthu angasankhe akakumana ndi mayeserowo. Kenako muzikambirana ngati zimene wina wasankha kuchita n’zoyenera kapena zolakwika. Muzisinthasintha zochita pa masewerowo kuti ana azisangalala nazo. Cholinga chanu chizikhala kuthandiza anawo kukhala odziletsa osati kumangochita zimene zabwera m’mutu mwawo.—Mfundo ya m’Baibulo: Miyambo 29:11.

Khalani oleza mtima. Baibulo limanena kuti: “Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.” (Miyambo 22:15) Choncho musaganize kuti mwana wanu angasinthe lero ndi lero. Buku lina lothandiza kuphunzitsa ana limanena kuti nkhani imeneyi imatheka mwapang’onopang’ono ndipo pamafunika khama. Koma pali ubwino wambiri. Mwachitsanzo, mwana amene waphunzitsidwa kudziletsa adzatha kupewa kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kuchita chiwerewere.

^ ndime 6 Mawuwa analemba ndi Dr.  David Walsh, m’buku lakuti: No: Why Kids—of All Ages—Need to Hear It and Ways Parents Can Say It.

^ ndime 8 Mawuwa analemba ndi Dr. Dan Kindlon m’buku lakuti Too Much of a Good Thing—Raising Children of Character in an Indulgent Age.