Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Mwana Wanu Wachinyamata Akachita Zinthu Zokuchititsani Kusiya Kumukhulupirira

Mwana Wanu Wachinyamata Akachita Zinthu Zokuchititsani Kusiya Kumukhulupirira

 Achinyamata ena amabwera pakhomo mochedwa. Ena amanamiza makolo, mwina powauza mabodza kapena kuchoka pakhomo mozemba kupita kokacheza ndi anzawo. Kodi mungatani ngati mwana wanu wachinyamata wachita zinthu zokuchititsani kuti musiye kumukhulupirira?

 Kodi mwana wanga wapanduka?

 N’kutheka kuti sanapanduke. Baibulo limati: “Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana,” ndipo achinyamata nthawi zambiri amachita zinthu zosonyeza kuti mawu amenewa ndi oona. (Miyambo 22:15) Pankhani imeneyi, Dr. Laurence Steinberg anati: “Achinyamata nthawi zina amachita zinthu zopupuluma komanso zopusa. Choncho muyembekezere kuti nthawi zina azilakwitsa zinthu.” a

 Bwanji ngati wandinamiza?

 Musafulumire kuganiza kuti mwana wanu wachinyamata waganiza zoti asamakumvereni. Kafukufuku wasonyeza kuti achinyamata amadera nkhawa zimene makolo awo amawaganizira, ngakhale azioneka ngati sizimawakhudza. Ngakhale kuti mwana wanuyo sangasonyeze momwe akumvera, zoona zake n’zakuti mwina wakhumudwa ndi zimene wachitazo ndipo akudandaula kuti wakukhumudwitsani.

Munthu akavulala n’kuthyoka fupa, limabwereranso m’malo mwake akalandira chithandizo. Mofananamo ngati mwana walakwitsa zinazake, n’zotheka kukonzanso zinthu ndipo mungayambenso kumukhulupirira

 Kodi wolakwa ndani?

  •    Kodi ndi anzake amene akumuchititsa? Baibulo limati: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Zoonadi, achinyamata amatengera kwambiri zimene anzawo amachita. Komanso pali zinthu zina zimene zingawasokoneze, monga kucheza ndi anzawo pa intaneti, komanso anthu otsatsa malonda. Ndipotu achinyamata amakhala kuti sakudziwa zambiri pamoyo. Zinthu zonsezi zimawapangitsa kuti asamasankhe bwino zochita nthawi zina. Komabe, kuti iwo adzakhale achikulire odalirika, akuyenera kuvomereza zotsatirapo za zochita zawo.

  •    Kodi wolakwa ndine kapena? Nthawi zina mungaganize kuti mwina mumakhwimitsa kwambiri zinthu, n’chifukwa chake mwana wanuyo wayamba khalidwe loipa. Kapena mungaganize kuti mumamulekerera komanso mumamupatsa ufulu wochuluka kwambiri. M’malo moganizira kwambiri zimene inuyo munachita zomwe zabweretsa vutolo, ndi bwino kuganizira zimene mungachite kuti muthetse vutolo.

 Kodi ndingathandize bwanji mwana wanga wachinyamata kuchita zinthu zoti ndiyambenso kumukhulupirira?

  •   Musachite zinthu mopsa mtima. N’zachidziwikire kuti mwana wanuyo akuyembekezera kuti mupsa mtima. Ndiye bwanji osachita zinthu zosiyanako? Kambiranani mofatsa ndi mwana wanuyo kuti mudziwe chimene chinamuchititsa kuti apange zimene wapangazo. Kodi amafuna kudziwa zinazake? Kapena amaboweka? Kapena amasowa wocheza naye? Kodi alibe anzake? Zifukwa zonsezi sizingalungamitse zolakwa zimene anapangazo, koma zingakuthandizeni inuyo pamodzi ndi mwana wanuyo kumvetsa bwino chimene chinamuchititsa.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.”—Yakobo 1:19..

  •   Thandizani mwana wanu kuganizira mofatsa zimene zinachitikazo. Mufunseni kuti, Kodi waphunzirapo chiyani pa zimene zachitikazi? Utakumananso ndi zangati zomwezi, kodi ungapange bwanji zinthu mosiyana? Mafunso ngati amenewa angathandize wachinyamatayo kuphunzira mmene ayenera kuganizira asanachite zinthu.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Dzudzula, tsutsa, dandaulira. Chita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri.”—2 Timoteyo 4:2.

  •   Muthandizeni kuona kuti zochita zake zili ndi zotsatirapo zake. Zilizonse zimene mungamuletse kuchita zizikhala zogwirizanadi ndi zomwe walakwitsa n’cholinga choti zimuthandize kuphunzirapo kanthu. Mwachitsanzo, ngati mwana wanu wachita zinthu zoti musiye kumukhulupirira poyendetsa galimoto yanu asanakupempheni, mukhoza kumuikira malire a nthawi yomwe ayenera kumayendetsa galimotoyo mpaka pamene mungaone kuti wasintha.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”Agalatiya 6:7.

  •   Muthandizeni kudziwa zimene angachite kuti ayambirenso kuchita zinthu zoti muzimukhulupirira. N’zoona kuti zingatenge nthawi yaitali. Komabe, mwana wanu akufunika kudziwa kuti n’zotheka kuyambiranso kuchita zinthu zoti muzimukhulupirira ngakhale kuti zingathe nthawi. Onetsetsani kuti akutha kuzindikira kuti ndinu wokonzeka kuyambiranso kumukhulupirira. Ngati mwangomusiya, mwanayo angayambe kuona kuti sangathenso kukonza zinthu kuti muzimukhulupirira ndipo akhoza kugwa mphwayi.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Inu abambo, musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”—Akolose 3:21.

a Kuchokera m’buku lakuti You and Your Adolescent.