Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Ndingatani Ngati Mwana Wanga Akumaboweka?

Ndingatani Ngati Mwana Wanga Akumaboweka?

 Mwana wanu ali pakhomo ndipo akusowa zochita. Kenako akukuuzani kuti: “Ndaboweka!” Musanamuyatsire TV kuti azionera makatuni kapenanso kumupatsa magemu oti azisewera, taganizirani kaye mfundo izi:

Zomwe makolo ena apeza zokhudza ana amene amaboweka

  •   Kuthera nthawi yaitali pa zosangalatsa kungawonjezere vuto la kuboweka. Bambo wina dzina lake Robert anati: “Ana ena amaboweka ngati sakuonera TV kapena kusewera magemu. Ana oterewa amaona kuti kuchita zinthu zina sikungawathandize kukhala osangalala.”

     Mkazi wake Barbara anavomereza mfundoyi ndipo anati: “Munthu amafunika kuganiza komanso kuchita khama. Koma nthawi zambiri zotsatira za zinthu zomwe wachita sizioneka nthawi yomweyo. Choncho zimenezi ndi zobowa kwa ana amene amathera nthawi yambiri poonera TV ndiponso kusewera magemu.”

  •   Kuthera nthawi yaitali pamalo ochezera a pa intaneti kungachititse kuti munthu ayambe kudziona molakwika. Munthu amene amangokhalira kuona zithunzi ndi mavidiyo a zinthu zimene anzake akuchita angayambe kuona kuti moyo wake ndi wosafunika. Mtsikana wina dzina lake Beth anati: “N’zosavuta kuyamba kuganiza kuti, ‘Anzanga onse akunjoya pomwe ine ndikungokhala pakhomo.’”

     Kuwonjezera pamenepa, munthu akamathera nthawi yaitali pamalo ochezera a pa intaneti, mapeto ake amaona kuti palibe chomwe wachita ndipo amangobowekabe. Mnyamata wina dzina lake Chris anati: “Ukakhala pa intaneti umaoneka kuti uli bize ndithu koma pamapeto pake umaona kuti palibe cholozeka chomwe wachita.”

  •  Kuboweka kungathandize munthu kuchita zinthu zina. Mayi wina dzina lake Katherine ananena kuti kuboweka kumathandiza kuti ana akhale ndi luso lopanga zinthu zina. Mwachitsanzo, iye anati: “Mwana angagwiritse ntchito katoni popanga mosungira zinthu, galimoto, boti kapena sitima. Angapangenso kanyumba pogwiritsa ntchito bulangete ndi mipando.”

     Pa zifukwa zabwino, katswiri wina wa zamaganizo dzina lake Sherry Turkle anafotokoza kuti kuboweka ndi “mwayi wogwiritsa ntchito luso lanu.” a Choncho, kuboweka pakokha sivuto. Ndipotu buku lina linati: “Munthu akamanyamula zinthu zolemera n’cholinga chofuna kulimbitsa thupi amakhala ndi minofu yamphamvu. N’chimodzimodzinso ndi kuboweka, munthu akaboweka amakhala ndi mwayi woganizira mmene angagwiritse ntchito luso lake.”—Disconnected.

 Mfundo yofunika kwambiri: Ana anu akamaboweka musamaone kuti ndi vuto koma muziona kuti ndi mwayi wowathandiza kukhala ndi luso lochita zinthu zina.

Zomwe mungachite ngati ana anu amaboweka

  •   Ngati n’zotheka, muzilola ana anu kuti azisewera panja. Barbara yemwe tamutchula kale uja anati: “Munthu akamawothera dzuwa komanso kupitidwa mphepo panja, zimathandiza kuti asamaboweke. Kusewera panja kunathandiza ana athu kuti atseguke m’mutu n’kuyamba kuganizira zinthu zina zomwe angamachite.”

     Mfundo ya m’Baibulo: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . Nthawi yolira ndi nthawi yoseka . . . ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.”—Mlaliki 3:1, 4.

     Zoti muganizire: Kodi ndingathandize bwanji ana anga kuti azipeza mipata yosewera panja? Ngati sizingatheke kusewera panja, kodi pali zinthu zinanso ziti zimene angamachite ali m’nyumba?

  •   Muzithandiza ana anu kuti aziganizira anthu ena. Mayi wina dzina lake Lillian anati: “Mungatchetche kapena kusesa pakhomo la anzanu enaake achikulire, kuwaphikira chakudya kapenanso kungopita kunyumba kwawo kukawaona. Munthu amasangalala kwambiri akamathandiza ena.”

     Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto, ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.”—Miyambo 11:25.

     Zoti muganizire: Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azikhala osangalala chifukwa chothandiza ena?

  •   Muzisonyeza chitsanzo chabwino. Zimene mumanena zokhudza moyo wanu watsiku ndi tsiku zingakhudze ana anu. Mayi wina dzina lake Sarah anati: “Tikamangokhalira kuuza ana athu zinthu zodetsa nkhawa zomwe zikuchitika pa moyo wathu, zimawapangitsa kuti aziboweka. Koma tikamanena zinthu zabwino, timawathandiza kuti nawonso aziona zinthu moyenera.”

     Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.”—Miyambo 15:15.

     Zoti muganizire: Kodi ana anga amaona kuti ndimakonda kulankhula zinthu zotani? Kodi amaona kuti ndimakonda kuchita chiyani ndikaboweka?

 Zimene zingakuthandizeni: Thandizani ana anu kuganizira zinthu zosiyanasiyana zomwe angamachite. Mayi wina dzina lake Allison anati: “Tinakonza kabokosi komwe aliyense m’banja lathu amaponyamo kapepala kamene walembapo maganizo ake.”

a Kuchokera m’buku la Chingelezi lakuti, Reclaiming Conversation.