Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula Pafoni

Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula Pafoni

ZOMWE ZIMACHITIKA

Mwina mwamvapo zoti achinyamata ambiri amatumizirana zinthu zolaula pafoni. Mungamade nkhawa kuti, ‘Kodi mwana wanga sakumachita nawo zimenezi?’

Mwina mukufuna mutakambirana nkhani imeneyi ndi mwana wanu, koma kodi mungayambire pati? Tisanayankhe funso limeneli, choyamba muyenera kudziwa chifukwa chimene achinyamata ambiri amatumizirana zinthu zolaula pafoni komanso chifukwa chake nkhaniyi ikukukhudzani. *

ZOMWE ZIMACHITITSA

  • Achinyamata ena amatumiza mameseji a zinthu zolaula pofuna kuti azikopana ndi munthu amene amamufuna.

  • Nthawi zina mtsikana amatha kujambulitsa chithunzi ali maliseche n’kuchitumiza kwa mnyamata chifukwa chakuti mnyamatayo wachita kumunyengerera kuti achite zimenezo.

  • Nthawi zina mnyamata angatumize chithunzi cha mtsikana atavula kwa anthu ambirimbiri pofuna kungosangalatsa anzake. Angachitenso zimenezi ngati chibwenzi chake chatha ndiye akufuna kuchititsa manyazi mtsikanayo.

Wachinyamata amene ali ndi foni akhoza kukumana ndi mavuto ambiri ngati saigwiritsa ntchito bwino. Buku lina linanena kuti: “Kungotumiza meseji kapena chithunzi cholaula kukhoza kusokoneza zinthu zambirimbiri.”—CyberSafe.

Anthu ambiri sadziwa kuti munthu akaika chithunzi pa Intaneti, sangaletse anthu ena kuchiona komanso sangadziwe mmene anthu ena angachigwiritsire ntchito. Mwachitsanzo, apolisi a FBI (Federal Bureau of Investigation) ku America, ananena kuti mtsikana wina wazaka 18 “anadzimangirira atazindikira kuti chithunzi chomwe anadzijambula ali maliseche n’kuchitumiza kwa chibwenzi chake, chatumizidwanso kwa anzake ambiri a kusukulu. Ana ena a sukulu, omwe ankatumiziranso anzawo chithunzichi, ayenera kuti ankamunyoza kapena kumuchititsa manyazi.”

Nthawi zina munthu amatha kuimbidwa mlandu chifukwa chotumiza zinthu zolaula. Mwachitsanzo m’mayiko ena, ana amene atumiza zithunzi zolaula kwa ana anzawo amaimbidwa mlandu ndipo kupolisi amawalemba m’gulu la anthu ogwiririra. Monga kholo, mukhoza kuimbidwanso mlandu ngati simunamuthandize mwana wanuyo kupewa kuchita zimenezi.

 ZIMENE MUNGACHITE

Muzimupatsa malamulo omveka bwino. Ngakhale kuti simungalamulire mwana wanu zimene ayenera kuchita ndi foni yake, mukhoza kumuthandiza pom’patsa malamulo omveka bwino komanso kumuuza chilango chimene angalandire akapanda kutsatira malamulowo. Muyeneranso kudziwa kuti muli ndi udindo wodziwa zimene mwana wanu akuchita ndi foni yake.—Lemba lothandiza: Aefeso 6:1.

Muthandizeni kuti aziganiza bwino. Mwina mukhoza kumufunsa kuti: “Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya zithunzi zimene tingati ndi zolaula. Kodi iweyo ukuganiza kuti zithunzi zolaula ndi zotani? Kodi ukuganiza kuti ndi zithunzi zotani zimene zili zosayenera kutumizirana pafoni? M’mayiko ena mwana akatumiza chithunzi cha mwana mnzake ali maliseche amatha kuimbidwa mlandu, kodi ukuganiza kuti zimenezi n’zolakwika? N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutumizirana zinthu zolaula si kwabwino?” Mwana wanuyo akamayankha muzimumvetsera kuti mudziwe mmene akuonera nkhaniyi, ndipo muthandizeni kuti aziganizira zimene zingachitike ngati atagwiritsa ntchito foni yake molakwika.—Lemba lothandiza: Aheberi 5:14.

Muziganizira zimene zingachitike ngati mutagwiritsa ntchito foni yanu molakwika

Muthandizeni kuganizira zoyenera kuchita. Ngati muli ndi mwana wamkazi mungamufunse kuti: ‘Kodi mtsikana angatani ngati mnyamata akumunyengerera kuti ajambulitse chithunzi ali maliseche n’kumutumizira? Kodi ayenera kuchitadi zimenezi pofuna kuti asamukhumudwitse? Kodi ayenera kukana kutumiza chithunzicho koma n’kumachezabe naye? Kapena ayenera kukamunenera kwa munthu wamkulu?’ Muthandizeni kuganizira zimene ayenera kuchita. Mukhozanso kuchita zimenezi ngati muli ndi mwana wamwamuna.—Lemba lothandiza: Agalatiya 6:7.

Muthandizeni kudziwa ubwino wochita zinthu mwanzeru. Mungamufunse mafunso ngati awa: ‘Kodi umaona kuti kukhala ndi mbiri yabwino n’kofunika? Kodi umafuna kuti anthu azikudziwa kuti ndiwe munthu wotani? Kodi ungamve bwanji ngati utamuchititsa munthu wina manyazi potumiza chithunzi chake chosayenera kwa anthu ena? Nanga ungamve bwanji ngati utamachita zinthu zoyenera?’ Muthandizeni mwana wanu kuti azikhala “ndi chikumbumtima chabwino.”—1 Petulo 3:16.

Muzisonyeza chitsanzo chabwino. Baibulo limanena kuti nzeru yakumwamba ndi yoyera komanso yopanda chinyengo. (Yakobo 3:17) Kodi zimene mumachita zimakhala zoyera komanso zopanda chinyengo? Buku lina linanena kuti: “Makolo ayenera kusonyeza chitsanzo chabwino ndipo sayenera kuona zithunzi kapena kutsegula mawebusaiti omwe anthu ena angawaone kuti ndi olakwika.”—CyberSafe.

^ ndime 5 Zinthu zolaula zimene anthu amatumizirana pafoni zimatha kukhala mameseji, zithunzi kapena mavidiyo. Kuti mudziwe zambiri, pitani pa webusaiti ya jw.org kuti muwerenge nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Zimene Ndiyenera Kudziwa Zokhudza Kutumizirana Zinthu Zolaula.”—Fufuzani pa mawu akuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA.