Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Kodi Kuphunzitsa Ana Ntchito Zapakhomo N’kothandiza Bwanji?

Kodi Kuphunzitsa Ana Ntchito Zapakhomo N’kothandiza Bwanji?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

M’mabanja ena, ana amapatsidwa ntchito zosiyanasiyana zapakhomo ndipo amazigwira bwinobwino osanyinyirika. Pomwe m’mabanja ena, makolo sapatsa ana awo ntchitozi ndipo zimenezi zikupangitsa kuti ana awo asakhale ndi chidwi chogwira ntchito.

Ochita kafukufuku anapeza kuti kumayiko a azungu n’kumene ana ambiri amangokhala manja lende n’kumayembekezera kuti anthu ena awachitire zinthu. Mwachitsanzo, bambo ena dzina lawo a Steven ananena kuti: “Masiku ano, ntchito ya ana imangokhala kuchita masewera apakompyuta, kufufuza zinthu pa intaneti komanso kuonera TV basi.”

Kuphunzitsa ana ntchito zapakhomo kumathandiza kuti pakhomopo pazikhala posamalika. Koma kodi n’zoona kuti kumathandizanso kuti anawo akule bwino? Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Makolo ena sapatsa ana awo ntchito zapakhomo makamaka akaona kuti ali ndi homuweki yambiri komanso akumatanganidwa ndi zinthu zina zomwe amachita akaweruka kusukulu. Komabe, tiyeni tione kuti kuphunzitsa ana ntchito zapakhomo n’kothandiza bwanji.

Kumathandiza kuti mwana azichita zinthu mwanzeru. Nthawi zambiri ana amene amagwira ntchito zapakhomo, zinthu zimawayendera bwino kusukulu. Tikutero chifukwa chakuti mwana akamagwira ntchito zapakhomo amakhala wanzeru komanso sadzikayikira ndipo zimenezi n’zofunika kwambiri pophunzira zinthu.

Kumathandiza kuti mwana azikhala ndi mtima wofuna kuthandiza ena. Anthu ena ananenapo kuti anthu amene amadzipereka kugwira ntchito zosiyanasiyana m’dera lawo, amakhala amene ankakondanso kugwira ntchito zapakhomo ali ana. Zimenezi si zodabwitsa chifukwa kugwira ntchito zapakhomo kumathandiza mwana kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza ena. A Steven omwe tawatchula koyambirira aja ananenanso kuti: “Ngati makolo sapatsa ana awo zochita, anawo amakula ndi kamtima komangofuna kuti munthu wina aziwachitira chilichonse. Choncho amakula ndi maganizo olakwika chifukwa sadziwa udindo wawo komanso sadziwa kufunika kolimbikira ntchito.”

Kumathandiza kuti banja lizigwirizana. Ana omwe amagwira ntchito zapakhomo amamva kuti ndi ofunika komanso amadziwa kuti ali ndi udindo wothandiza nawo zinthu zina m’banja lawo. Koma zimenezi sizingachitike ngati makolo amalephera kupatsa ana awo ntchito zapakhomo poganiza kuti zinthu zina zomwe amachita akaweruka kusukulu, ndiye zofunika kwambiri. Choncho mungadzifunse kuti, ‘Kodi chingachitike n’chiyani ngati mwana wanga amangokhalira kusewera mpira ndi anzake akusukulu koma sapeza nthawi yogwira nafe ntchito zapakhomo?’

ZIMENE MUNGACHITE

Mmera m’poyamba. Anthu ena amanena kuti makolo amafunika kuyamba kuphunzitsa ana awo ntchito zapakhomo, akafika zaka zitatu. Pomwe ena amaona kuti zaka zabwino ndi zaka ziwiri kapena kuchepera pamenepa. Chofunika kudziwa n’choti, ana aang’ono amakonda kugwira ntchito limodzi ndi makolo awo komanso kutsanzira zimene makolowo akuchita.​—Lemba lothandiza: Miyambo 22:6.

Muziwapatsa ntchito zogwirizana ndi msinkhu wawo. Mwachitsanzo, mwana wa zaka zitatu akhoza kuphunzitsidwa kulongedza zidole zake akamaliza kusewera, kupukuta madzi akataika kapena kusankha zovala zofunika kuchapa. Ana okulirapo akhoza kusesa m’nyumba, kutsuka galimoto kapenanso kuphika. Muzidziwa ntchito zimene mwana wanu amachita bwino. Mukamupatsa ntchitozo mudzadabwa kuona kuti wayamba kukonda kwambiri kugwira ntchito zapakhomo.

Muziwasonyeza kuti ntchito zapakhomo n’zofunika kuposa zakusukulu. Zimenezi zimakhala zovuta ngati tsiku lililonse mwana wanu amapatsidwa homuweki yambiri. Komabe buku lina linanena kuti mukamapewa kupatsa mwana wanu ntchito zapakhomo n’cholinga choti azikhoza bwino kusukulu, mumakhala ngati mukumusonyeza kuti ‘ntchito zapakhomozo si zofunika kwenikweni.’ (The Price of Privilege) Monga tanenera kumayambiriro kwa nkhaniyi, ana akamagwira ntchito zapakhomo zimawathandiza kuti asamavutike kuphunzira zinthu. Ndipo zinthu zomwe aphunzira ali aang’ono, zimadzawathandiza akadzakhala ndi banja lawo.​—Lemba lothandiza: Afilipi 1:10.

Muziganizira cholinga chomwe mwawapatsira ntchitoyo osati mmene aigwirira. Nthawi zina mwana wanu angachedwe kumaliza ntchito yomwe mwamupatsa kapenanso mungaone kuti sakuigwira bwino. Zimenezi zikachitika, musamafulumire kumulandira. Cholinga chanu si chakuti mwanayo agwire ntchitoyo ngati munthu wamkulu, koma kumuthandiza kudziwa kuti nayenso ali ndi udindo pa banjalo komanso kuti azisangalala kuti wagwira nawo ntchito inayake.​—Lemba lothandiza: Mlaliki 3:22.

Muziwathandiza kuti asamangoyembekezera kulandira malipiro. Ena amanena kuti kupatsa mwana malipiro, kumamuthandiza kudziwa kuti sikadza kokha. Pomwe ena amanena kuti kupatsa mwana malipiro kumamuchititsa kuti azingoganizira zimene angapeze akagwira ntchitoyo ndipo saona kuti nayenso akhoza kuthandiza nawo banja lawo. Amanenanso kuti kuchita zimenezi n’koopsa chifukwa mwanayo akakhala ndi ndalama amakana kugwira ntchitozo. Choncho makolo akafuna kupatsa mwana wawo mphatso, azichita zimenezi pa nthawi ina, osati pamene amupatsa ntchito inayake.