Pitani ku nkhani yake

Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kudziwa Bwino Mulungu?

Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kudziwa Bwino Mulungu?

Yankho la m’Baibulo

 Mungadziwe bwino Mulungu mukamaphunzira za iye komanso kuchita zimene amafuna. Mukamachita zimenezi Mulungu “adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:8) Baibulo limanena kuti “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Machitidwe 17:27.

 Zimene zingathandize kuti mudziwe Mulungu

 Muziwerenga Baibulo

  •  Zimene Baibulo limanena: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.”—2 Timoteyo 3:16.

  •  Mfundo yake: Mulungu ndi Mlembi wamkulu wa Baibulo. Iye anachititsa kuti anthu alembe maganizo ake m’Baibulo. Pogwiritsa Baibulo, Mulungu watiuza za moyo umene amafuna kuti tikhale nawo. Watiuzanso makhalidwe ake monga chikondi, chilungamo ndi chifundo.—Ekisodo 34:6; Deuteronomo 32:4.

  •  Zimene mungachite: Muziwerenga Baibulo tsiku lililonse. (Yoswa 1:8) Muziganizira zimene mwawerenga n’kumadzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuphunzirapo chiyani zokhudza Mulungu?’—Salimo 77:12.

     Mwachitsanzo, werengani Yeremiya 29:11, kenako mudzifunse kuti: ‘Kodi Mulungu amandifunira chiyani? Kodi amafuna mtendere kapena mavuto? Nanga kodi amafuna kundichitira nkhanza kapena amandifunira tsogolo labwino?’

 Muziona zimene analenga

  •  Zimene Baibulo limanena: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. . . . [Akuonekera] m’zinthu zimene anapanga.”—Aroma 1:20.

  •  Mfundo yake: Zimene Mulungu analenga zimasonyeza mmene iye alili ngati mmene chithunzi chimene munthu wajambula kapena mashini amene wapanga zingasonyezere mmene munthuyo alili. Mwachitsanzo, ubongo wodabwitsa wa munthu umene ungasunge zinthu zambiri umasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru. Komanso mphamvu ya dzuwa ndi nyenyezi zina imasonyeza kuti Mulungu ndi wamphamvu kwambiri.—Salimo 104:24; Yesaya 40:26.

  •  Zimene mungachite: Muzipeza nthawi yoona komanso yophunzira za chilengedwe. Mukamachita zimenezi, muzidzifunsa kuti, ‘Zinthu zodabwitsa za m’chilengedwe zimasonyeza chiyani zokhudza Mulungu?’ a Koma n’zoona kuti sitingadziwe zonse zokhudza Mulungu poona zimene analenga. Ndiye n’chifukwa chake iye anatipatsa Baibulo.

 Muzigwiritsa ntchito dzina la Mulungu

  •  Zimene Baibulo limanena: “Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa. Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha.”—Salimo 91:14, 15.

  •  Mfundo yake: Mulungu, yemwe dzina lake ndi Yehova, amaganizira kwambiri anthu amene amadziwa dzina lake komanso kuligwiritsa ntchito mwaulemu. b (Salimo 83:18; Malaki 3:16) Potiuza dzina lake, Mulungu wasonyeza kuti amafuna kuti timudziwe. Iye anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.”—Yesaya 42:8.

  •  Zimene mungachite: Muzigwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova polankhula za Mulungu.

 Muzipemphera kwa Yehova

  •  Zimene Baibulo limanena: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.”—Salimo 145:18.

  •  Mfundo yake: Yehova amayandikira anthu amene ali ndi chikhulupiriro ndipo amapemphera kwa iye. Kupemphera ndi mbali ina ya kulambira Mulungu ndipo kumasonyeza kuti timamulemekeza kwambiri.

  •  Zimene mungachite: Muzipemphera kwa Mulungu pafupipafupi. (1 Atesalonika 5:17) Muzimuuza zimene zikukudetsani nkhawa komanso mmene mukumvera mumtima mwanu.—Salimo 62:8. c

 Muzilimbitsa chikhulupiriro chanu mwa Mulungu

  •  Zimene Baibulo limanena: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.”—Aheberi 11:6.

  •  Mfundo yake: Kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu, tiyenera kumukhulupirira. Koma mogwirizana ndi Baibulo, kumukhulupirira kumatanthauza zambiri osati kungokhulupirira kuti aliko. Kumatanthauzanso kuti timamudalira ndi mtima wonse komanso kudalira malonjezo ndi mfundo zake. Popanda kukhulupirira munthu, sitingakhale naye pa ubwenzi wabwino.

  •  Zimene mungachite: Munthu sangakhulupirire zinthu zimene sakuzidziwa. (Aroma 10:17) Choncho muyenera kuphunzira Baibulo kuti mudziwe chifukwa chake mungamakhulupirire Mulungu komanso malangizo ake. A Mboni za Yehova angakonde kumaphunzira nanu Baibulo. d

 Muzichita zimene zimasangalatsa Mulungu

  •  WZimene Baibulo limanena: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.”—1 Yohane 5:3.

  •  Mfundo yake: Yehova amakonda anthu amene amasonyeza kuti amamukonda poyesetsa kumvera malamulo ake.

  •  Zimene mungachite: Mukamaphunzira Baibulo, onani zimene Mulungu amakonda komanso zimene sakonda. Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndiyenera kusintha zinthu ziti n’cholinga choti ndizisangalatsa Mulungu?’—1 Atesalonika 4:1.

 Muzitsatira malangizo a Mulungu kuti muone kuti azikusamalirani

  •  Zimene Baibulo limanena: “Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.”—Salimo 34:8.

  •  Mfundo yake: Mulungu amatipempha kuti tione kuti iye ndi wabwino. Mukaona kuti Mulungu akukusonyezani chikondi komanso kukusamalirani mudzafuna kukhala naye pa ubwenzi wabwino.

  •  Zimene mungachite: Mukamawerenga Baibulo, muzitsatira malangizo a Mulungu kuti mupeze madalitso ambiri. (Yesaya 48:17, 18) Mungachitenso bwino kuona zitsanzo za anthu omwe anathandizidwa ndi Mulungu kuti athetse mavuto, asinthe zinthu pa moyo wawo ndi wa banja lawo komanso anapeza chimwemwe chenicheni. e

 Maganizo olakwika okhudza kudziwa Mulungu

 Maganizo olakwika: Mulungu ndi wamphamvu komanso wapamwamba kwambiri moti sangafune kukhala nafe pa ubwenzi.

 Zoona zake: Ngakhale kuti Mulungu ndi wamphamvu komanso wapamwamba kwambiri m’chilengedwe chonse, amatipempha kuti tikhale naye pa ubwenzi. M’Baibulo muli zitsanzo za amuna ndi akazi ambiri amene anali anzake apamtima a Mulungu.—Machitidwe 13:22; Yakobo 2:23.

 Maganizo olakwika: Sitingamudziwe Mulungu chifukwa ndi wosamvetsetseka.

 Zoona zake: Zinthu zina zokhudza Mulungu n’zovuta kumvetsa monga mfundo yakuti Mulungu ndi Mzimu wosaoneka. Komabe tingamudziwe. Baibulo limanena kuti tiyenera kumudziwa kuti tidzapeze moyo wosatha. (Yohane 17:3) Baibulo limafotokoza Mulungu m’njira imene tingamvetse kuti tidziwe makhalidwe ake, mfundo zake komanso cholinga chake chokhudza anthufe ndiponso dzikoli. (Yesaya 45:18, 19; 1 Timoteyo 2:4) Ndipo ngati mmene tatchulira kale, Baibulo limatiuzanso dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Choncho tingadziwe Mulungu komanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.—Yakobo 4:8.

a Kuti mudziwe zinthu zam’chilengedwe zomwe zimasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru, onani nkhani za mutu wakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?

b Anthu ambiri amaona kuti dzina la Yehova limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Potiuza dzina lake, tinganene kuti Mulungu akutiuza kuti: ‘Ndidzachititsa kuti cholinga changa chikwaniritsidwe. Nthawi zonse ndimachita zimene ndimanena.’

d Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji?

e Onani nkhani za mutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu.”