Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ULOSI WA OKWERA PAMAHATCHI UMATIKHUDZA BWANJI?

Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?

Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?

Anthu ena amaona kuti ulosi wonena za anthu 4 okwera pamahatchi ndi woopsa komanso wosamvetsetseka. Koma dziwani kuti n’zotheka kudziwa tanthauzo la ulosiwu. Baibulo komanso zinthu zimene zikuchitika masiku ano zingatithandize kudziwa zimene wokwera pahatchi aliyense akuimira. Ngakhale kuti ulosiwu ukuimira mavuto amene akuchitika padzikoli, zinthu zina zimene ukuimira, zingakhale nkhani yabwino kwa inuyo ndi banja lanu. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tione zimene wokwera pahatchi aliyense akuimira.

WOKWERA PAHATCHI YOYERA

Ulosiwu umayamba ndi kunena kuti: “Nditayang’ana, ndinaona hatchi yoyera. Wokwerapo wake ananyamula uta. Iye anapatsidwa chisoti chachifumu, ndi kupita kukagonjetsa adani ake ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nawo.”Chivumbulutso 6:2.

Kodi wokwera pahatchi imeneyi akuimira ndani? Buku la Chivumbulutso lomweli lingatithandize kumudziwa chifukwa limasonyeza kuti ndi wakumwamba ndipo limamutchula kuti “Mawu a Mulungu.” (Chivumbulutso 19:11-13) Dzina laudindo lakuti, “Mawu” limanena za Yesu Khristu chifukwa amalankhula m’malo mwa Mulungu. (Yohane 1:1, 14) Iye amatchedwanso “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye” komanso “Wokhulupirika ndi Woona.” (Chivumbulutso 19:16) Choncho Yesu ndi Mfumu ndipo ali ndi mphamvu, koma sagwiritsa ntchito mphamvu zakezo molakwika. Komabe pangakhale mafunso ena.

Mwachitsanzo, kodi ndani anapatsa Yesu mphamvu? (Chivumbulutso 6:2) Mneneri Danieli anaona masomphenya onena za Mesiya. M’masomphenyawo, “Wamasiku Ambiri,” yemwe ndi Yehova, * anapereka “ulamuliro ndi ufumu” kwa “mwana wa munthu.” (Danieli 7:13, 14) Choncho Mulungu Wamphamvuyonse ndi amene anapatsa Yesu mphamvu zoti akhale Mfumu komanso kuti adzapereke chiweruzo. Hatchi yoyera ndi chizindikiro choyenera cha nkhondo yachilungamo yomenyedwa ndi Mwana wa Mulungu chifukwa nthawi zambiri m’Malemba, chinthu choyera chimaimira chilungamo.Chivumbulutso 3:4; 7:9, 13, 14.

Kodi anthuwa anakwera liti pamahatchi? Paja Baibulo limasonyeza kuti wokwera pahatchi yoyamba ndi Yesu, ndipo anakwera pahatchiyi atangoikidwa kukhala Mfumu. (Chivumbulutso 6:2) Ndiye kodi Yesu anaikidwa liti kukhala Mfumu kumwamba? Iye sanakhale Mfumu pamene anaukitsidwa n’kupita kumwamba. Baibulo limasonyeza kuti atapita kumwambako anadikira kaye. (Aheberi 10:12, 13) Yesu anapatsa otsatira ake chizindikiro choti chidzawathandize kudziwa kuti nthawi yodikirayo idzatha liti. Chizindikirocho chinalinso chodzawathandiza kudziwa nthawi imene iye adzayambe kulamulira kumwamba. Anati akadzayamba kulamulira, zinthu zidzaipa kwambiri padzikoli moti padzakhala nkhondo, njala komanso miliri. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11) Nkhondo ya padziko lonse itangoyamba mu 1914, zinadziwikiratu kuti mavuto ambiri ayambika padzikoli. Uku kunali kuyamba kwa nthawi yovuta ndipo Baibulo limatchula nthawi imeneyi kuti “masiku otsiriza.”2 Timoteyo 3:1-5.

Koma kodi n’chifukwa chiyani Yesu atakhala Mfumu mu 1914 zinthu padzikoli zinayamba kuipa kwambiri, m’malo moti ziyambe kuyenda bwino? N’chifukwa chakuti pa nthawiyi Yesu anayamba kulamulira kumwamba, osati padzikoli. Pa nthawiyo kumwamba kunachitika nkhondo. Pa nkhondoyi, Yesu yemwe ndi Mikayeli, anamenyana ndi Satana ndi ziwanda zake ndipo Satana ndi ziwandazo anaponyedwa padzikoli. (Chivumbulutso 12:7-9, 12) Kungoyambira nthawi imeneyo, Satana ndi wokwiya kwambiri chifukwa akudziwa kuti watsala ndi kanthawi kochepa. Posachedwapa Mulungu akwaniritsa chifuniro chake padzikoli ndipo aweruza Satana. (Mateyu 6:10) Tsopano tiyeni tikambirane zokhudza okwera pamahatchi atatu ena aja ndipo tionanso umboni wakuti tilidi ‘m’masiku otsiriza.’ Okwera pamahatchi atatuwa sakuimira munthu. Koma amaimira mavuto amene akuchitika padziko lonse.

WOKWERA PAHATCHI YOFIIRA

“Pamenepo, hatchi ina inatulukira. Imeneyi inali yofiira ngati moto. Wokwerapo wake analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi, kuti anthu aphane. Iye anapatsidwanso lupanga lalikulu.”Chivumbulutso 6:4.

Wokwera pahatchi imeneyi akuimira nkhondo. Onani kuti lembali lanena kuti wokwera pahatchiyu akuchotsa mtendere padziko lonse lapansi, osati m’mayiko owerengeka chabe. Mu 1914, nkhondo ya padziko lonse inayambika ndipo aka kanali koyamba kuti nkhondo yaikulu choncho ichitike. Kenako panayambikanso nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Nkhondoyi inapha anthu ambiri kuposa yoyamba ija. Kafukufuku amasonyeza kuti kungochokera mu 1914, anthu oposa 100 miliyoni aphedwa pa nkhondo. Anthu enanso ambiri anavulala koopsa.

Kodi nkhani ya nkhondo yafika pati masiku ano? Panopa anthu akupanga zida zoopsa kwambiri zoti atati azigwiritse ntchito akhoza kupha anthu onse padzikoli. Choncho ulosi wonena za wokwera pahatchi yofiira ukukwaniritsidwa. Izi zili choncho ngakhale kuti padzikoli pali mabungwe ngati United Nations, omwe amati ntchito yawo n’kukhazikitsa mtendere.

WOKWERA PAHATCHI YAKUDA

“Nditayang’ana, ndinaona hatchi yakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo m’dzanja lake. Kenako ndinamva mawu ngati ochokera pakati pa zamoyo zinayi zija. Mawuwo anali akuti: ‘Kilogalamu imodzi ya tirigu, mtengo wake ukhala dinari imodzi, ndipo makilogalamu atatu a balere, mtengo wake ukhala dinari imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.’”Chivumbulutso 6:5, 6.

Wokwera pahatchi imeneyi akuimira njala. Apa akunena za kukwera mitengo kwa chakudya. Ulosiwu unanena kuti kilogalamu imodzi ya tirigu mtengo wake udzakhala dinari imodzi. M’nthawi ya atumwi, dinari imodzi anali malipiro omwe munthu ankalandira akagwira ntchito tsiku lonse. (Mateyu 20:2) Ulosiwu unasonyezanso kuti ndi ndalama yomweyi, munthu azidzangogula makilogalamu atatu a balele, chomwe ndi chakudya chotsika poyerekeza ndi tirigu. Zimenezi zinasonyeza kuti sizidzakhala zophweka kupeza ndalama zokwanira kugula chakudya chokwana banja lonse. Ulosiwu unatchula za mafuta a maolivi ndi vinyo chifukwa ndi zakudya zomwe anthu pa nthawiyo ankadalira. Izi zinasonyeza kuti m’masiku otsiriza zakudya, ngakhale zimene anthu amadalira, zizidzasowa kwambiri.

Kodi palidi umboni woti kuchokera mu 1914, hatchi yakuda ndi wokwerapo wake ikuthamanga kwambiri? Inde. M’zaka za m’ma 1900, anthu pafupifupi 70 miliyoni anafa chifukwa cha njala. Lipoti lina linanena kuti “anthu 805 miliyoni anavutika ndi njala kwa nthawi yaitali pakati pa zaka za 2012 ndi 2014. Apa ndiye kuti munthu mmodzi pa anthu 9 alionse padzikoli ankavutika ndi njala.” Lipoti linanso linati: “Chiwerengero cha anthu amene amafa ndi njala chaka chilichonse n’chokwera kuposa cha onse amene amafa ndi Edzi, malungo komanso TB.” Choncho, ngakhale kuti anthu akuyesetsa kuthetsa njala, ulosi wonena za hatchi yakuda ndi wokwerapo wake ukukwaniritsidwa.

WOKWERA PAHATCHI YOTUWA

“Nditayang’ana, ndinaona hatchi yotuwa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa. Ndipo Manda anali kumutsatira pafupi kwambiri. Iwo anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi lupanga lalitali, njala, mliri wakupha, ndi zilombo za padziko lapansi.”Chivumbulutso 6:8.

Wokwera pahatchi ya 4 akuimira imfa yobwera chifukwa cha miliri komanso zinthu zina. Pasanapite nthawi yaitali kuchokera mu 1914, matenda a chimfine cha ku Spain anapha anthu mamiliyoni ambiri. N’kutheka kuti anthu okwana 500 miliyoni anadwala matendawa. Apa ndiye kuti munthu mmodzi pa anthu atatu alionse anagwidwa ndi matendawa.

Komatu ichi chinali chiyambi chabe. Akatswiri amati m’zaka za m’ma 1900 anthu enanso mamiliyoni ambiri anafa ndi matenda a nthomba. Panopa anthu ambiri akumwalira chifukwa cha Edzi, TB komanso malungo ngakhale kuti asayansi akuyesetsa kupeza njira zothetsera matendawa.

Monga taonera, nkhondo, njala komanso miliri zikupha anthu ambiri. Tingati Manda amalandira anthu ophedwawa ndipo zimangooneka ngati palibe chiyembekezo chilichonse choti zinthu zidzakhala bwino.

POSACHEDWAPA MAVUTO ONSE ADZATHA

Mavuto amene ali padzikoli atha posachedwapa. Musaiwale kuti mu 1914 Yesu ‘anapita kukagonjetsa’ adani ake ndipo anaponyera Satana padzikoli. Komabe sikuti pa nthawiyi iye anamaliza kugonjetsa adani ake onse. (Chivumbulutso 6:2; 12:9, 12) Posachedwapa, pa Aramagedo, Yesu adzachititsa kuti Satana asamavutitsenso anthu komanso adzawononga onse amene amachita zoipa. (Chivumbulutso 20:1-3) Iye adzathetsa nkhondo, njala ndi miliri. Choncho tingati okwera pamahatchi atatu ena aja, sadzakhalakonso. Kuwonjezera pamenepa, Yesu adzakonza zonse zomwe zawonongeka chifukwa cha zimenezi. Koma kodi adzachita bwanji zimenezi? Taonani zimene Baibulo limalonjeza.

Nkhondo idzatha ndipo padziko lonse padzakhala mtendere. Yehova ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Adzathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo adzatentha magaleta pamoto.’ (Salimo 46:9) Anthu omvera “adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”Salimo 37:11.

Njala idzatha chifukwa padziko lonse padzakhala chakudya chamwanaalirenji. “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”Salimo 72:16.

Posachedwapa Yesu adzathetsa mavuto onse obwera chifukwa cha okwera pamahatchi atatu ena aja

Miliri ndi imfa zidzatha ndipo anthu adzakhala ndi moyo wathanzi komanso wamuyaya. Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”Chivumbulutso 21:4.

Pamene Yesu anali padzikoli anachita zinthu zimene zinasonyeza zomwe adzachite akadzayamba kulamulira dzikoli. Ankalimbikitsa anthu kuti azikhala mwamtendere, anadyetsa anthu ambiri mozizwitsa, anachiritsa odwala komanso anaukitsa akufa.Mateyu 12:15; 14:19-21; 26:52; Yohane 11:43, 44.

A Mboni za Yehova angagwiritse ntchito Baibulo pokuthandizani kuti mudziwe zimene mungachite kuti inunso mudzakhalepo pa nthawi imene malonjezo amenewa adzakwaniritsidwe. Kodi mungakonde kudziwa zambiri?

^ ndime 7 Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.