Pitani ku nkhani yake

Kodi Ulosi wa M’Baibulo Umatiuza Zotani pa Nkhani ya Chaka cha 1914?

Kodi Ulosi wa M’Baibulo Umatiuza Zotani pa Nkhani ya Chaka cha 1914?

Yankho la m’Baibulo

 Maulosi a m’Baibulo amasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba m’chaka cha 1914. Ulosi wopezeka m’buku la Danieli chaputala 4 umasonyeza bwino nkhani imeneyi.

 Tione ulosiwu mwachidule. Mulungu anachititsa kuti Nebukadinezara, yemwe anali mfumu ya ku Babulo alote maloto aulosi okhudza mtengo wautali kwambiri umene unagwetsedwa. Chitsa chake sichinaloledwe kuphuka mpaka patadutsa “nthawi zokwanira 7” kuti chidzayambenso kuphuka.​—Danieli 4:​1, 10-​16.

 Kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwu. Mtengo waukuluwo unkaimira Mfumu Nebukadinezara. (Danieli 4:​20-22) Mophiphiritsira mfumuyi ‘inagwetsedwa’ pamene inasiya kulamulira ufumu wake kwa zaka 7 chifukwa chakuti inachita misala. (Danieli 4:​25) Mulungu atathetsa matenda akewo, anakhalanso mfumu ndipo anavomereza kuti Mulungu ndiyedi woyenera kulamulira.​—Danieli 4:​34-36.

 Umboni wosonyeza kuti ulosiwu unayenera kudzakwaniritsidwa m’njira inanso yaikulu. Cholinga chachikulu cha ulosiwu chinali chakuti “anthu adziwe kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso adziwe kuti iye akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa ndipo amaika ngakhale munthu wonyozeka kwambiri kuti azilamulira.” (Danieli 4:17) Kodi lembali likusonyeza kuti Mulungu ankafuna kupereka ulamuliro umenewu kwa Nebukadinezara yemwe anali wonyada? Ayi ndithu. Zili choncho chifukwa chakuti poyambirira Mulungu anaonetsa mfumuyi maloto osonyeza kuti palibe wolamulira wina aliyense wandale kuphatikizapo Nebukadinezarayo amene adzakwanitse zimene Mulungu amafuna. M’malomwake Mulungu “adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.”​—Danieli 2:31-44.

 Kale Mulungu anakhazikitsa ufumu wa Aisiraeli womwe unkaimira ulamuliro waMulunguyo padziko lapansi. Mulungu analola kuti ufumuwu ‘uwonongedwe’ chifukwa olamulira ake anasiya kuchita zinthu mokhulupirika. Kenako iye analosera kuti adzapereka ufumuwu kwa munthu “amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga.” (Ezekieli 21:25-​27) Baibulo limasonyeza kuti Yesu Khristu ndi amene anali woyenerera mwalamulo kulandira ufumu umenewu. (Luka 1:​ 30-​33) Mosiyana kwambiri ndi Nebukadinezara, Yesu anali “wodzichepetsa” mogwirizana ndi zimene zinaloseredwa.​—Mateyu 11:29.

 Kodi mtengo wotchulidwa mu Danieli chaputala 4 ukuimira chiyani? M’Baibulo, nthawi zina mitengo imaimira ulamuliro. (Ezekieli 17:22-​24; 31:​ 2-5) Pa kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosi wotchulidwa mu Danieli chaputala 4, mtengo waukulu umene unanenedwa m’chaputalachi ukuimira ulamuliro wa Mulungu.

 Kodi kudulidwa kwa mtengowo kumatanthauza chiyani? Monga mmene kudulidwa kwa mtengo wa mu ulosiwu kunaimira kuimitsidwa kwa ulamuliro wa Nebukadinezara, nawonso ulamuliro wa Mulungu padziko lapansi pano unaimitsidwa. Zimenezi zinachitika pamene Nebukadinezara anagonjetsa mzinda wa Yerusalemu kumene mafumu a Isiraeli ankakhala “pampando wachifumu wa Yehova,” monga oimira ulamuliro wake.​—1 Mbiri 29:23.

 Kodi “nthawi zokwanira 7” zikuimira chiyani? “Nthawi zokwanira 7” zimenezi zimaimira nthawi imene Mulungu analola kuti mitundu ya anthu izilamulira padziko lapansi popanda kusokonezedwa ndi ulamuliro uliwonse umene Mulunguyo anakhazikitsa. Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti “nthawi zokwanira 7” zimenezi zinayamba mu October 607 B.C.E., pamene Yerusalemu anawonongedwa ndi Ababulo. a​—2 Mafumu 25:​ 1, 8-​10.

 Kodi “nthawi zokwanira 7” ndi nyengo yaitali bwanji? Nthawi imeneyi ndi yosiyana ndi zaka 7 zenizeni zopezeka mu nkhani ya Nebukadinezara. Yesu ananena mawu otithandiza kudziwa nthawi imeneyi pamene anati, “Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu [yemwe ankaimira ulamuliro wa Mulungu], kufikira nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo zitakwanira.” (Luka 21:24) “Nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina,” yomwe ndi nthawi imene Mulungu analola kuti ‘mitundu ya anthu ipondeponde’ ulamuliro wake, ndi yofanana ndi “nthawi zokwanira 7” zotchulidwa mu Danieli chaputala 4. Izitu zikusonyeza kuti “nthawi zokwanira 7” zinali zisanathe ngakhale pamene Yesu anali padziko lapansi.

 Baibulo limatithandiza kudziwa kutalika kwa ulosi wa “nthawi zokwanira 7” umenewu. Limanena kuti “nthawi” zitatu ndi hafu zikuimira masiku 1,260. Choncho tinganene kuti “nthawi zokwanira 7” zikufanana ndi masiku 2,520 omwe ndi kuwirikiza kawiri masiku 1,260. (Chivumbulutso 12:​ 6, 14) Potsatira kuwerengera zaka kwa maulosi a m’Baibulo, komwe ‘tsiku limodzi limaimira chaka chimodzi’ ndiye kuti masiku 2,520 akuimira zaka 2,520. Choncho “nthawi zokwanira 7” kapena kuti zaka 2,520 zinatha mu October 1914.​—Numeri 14:34; Ezekieli 4:6.

a Kuti mudziwe mwatsatanetsatane chifukwa chimene chaka cha 607 B.C.E chimagwiritsidwa ntchito, werengani nkhani izi; “Kodi Yerusalemu Wakale Anawonongedwa Liti?-Gawo 1” tsamba 26-​31 mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2011, komanso nkhani yakuti, “Kodi Yerusalemu Wakale Anawonongedwa Liti?-Gawo 2” tsamba 22-​28 mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2011.