Pitani ku nkhani yake

Kodi Dzikoli Lidzatha?

Kodi Dzikoli Lidzatha?

Yankho la m’Baibulo

 Ayi. Dzikoli silidzatha, kuotchedwa kapena kulowedwa m’malo ndi dziko lina. Baibulo limanena kuti Mulungu analenga dziko lapansili kuti anthu azikhalamo mpaka kalekale.

  •   “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

  •   ‘[Mulungu] anakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.’—Salimo 104:5.

  •   “Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”—Mlaliki 1:4.

  •   “Amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, amene analikhazikitsa mwamphamvu, . . . sanalilenge popanda cholinga, . . . analiumba kuti anthu akhalemo.”—Yesaya 45:18.

Kodi anthu saliwonongeratu dzikoli?

 Mulungu sangalole kuti anthu awonongeretu dzikoli kaya ndi nkhondo kapena mwanjira ina iliyonse. Koma iye adzawononga anthu “amene akuwononga dziko lapansi.” (Chivumbulutso 11:18) Kodi adzachita bwanji zimenezi?

 Mulungu adzachotsa maulamuliro onse a ndale chifukwa alephera kuteteza dzikoli. Pa nthawiyo dziko lonse lapansi lidzayamba kulamuliridwa ndi Ufumu wabwino kwambiri wakumwamba. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Mulungu anasankha Mwana wake Yesu Khristu kuti adzakhale wolamulira mu Ufumu umenewo. (Yesaya 9:6, 7) Pa nthawi yomwe Yesu anali padzikoli, anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zolamulira zinthu za m’chilengedwe. (Maliko 4:35-41) Choncho chifukwa chakuti Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzakwanitsa kulamulira dzikoli komanso chilengedwe. Yesu adzalenganso kapena kukonzanso zinthu zomwe zinaonongeka kuti zikhalenso zatsopano ngati mmene zinalili m’munda wa Edeni.​—Mateyu 19:28; Luka 23:43.

Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti dzikoli lidzaotchedwa ndi moto?

 Ayi siliphunzitsa zimenezo. Anthu amaganiza kuti dzikoli lidzaotchedwa chifukwa chosamvetsa lemba 2 Petulo 3:7 lomwe limati: “Kumwamba kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto.” Tiyeni tikambirane mfundo ziwiri zofunika kwambiri zomwe zingatithandize kumvetsa mawu a palembali. Mfundo zake ndi izi:

  1.   M’Baibulo, mawu akuti “kumwamba,” “dziko lapansi” komanso “moto” amatanthauzanso zinthu zina. Mwachitsanzo pa Genesis 11:1 pamati: “Dziko lonse lapansi linali ndi chilankhulo chimodzi.” Pavesili mawu akuti “dziko . . . lapansi,” akutanthauza anthu.

  2.   Mawu a pa 2 Petulo 3:7, akutithandiza kudziwa tanthauzo la mawu akuti kumwamba, dziko lapansi komanso moto. Mavesi 5 ndi 6 akufotokoza kufanana kwa zomwe zidzachitike kutsogoloku ndi zimene zinachitika pa nthawi ya chigumula cha m’nthawi ya Nowa. “Dziko la pa nthawiyo,” kutanthauza anthu ochita zachiwawa a nthawi imeneyo, ndi amene anawonongedwa koma osati dziko lapansi lenileni. (Genesis 6:11) Mulungu anawononganso “kumwamba” kwa pa nthawiyo kapena kuti olamulira a nthawi imeneyo. Choncho anthu oipa ndi amene anawonongedwa koma osati dzikoli. Nowa ndi banja lake anapulumuka pamene Mulungu ankawononga anthu oipawa ndi chigumula. Koma chigumulacho chitatha, Nowa ndi banja lake anayambanso kukhala padzikoli.​—Genesis 8:15-18.

 Monga mmene zinakhalira ndi chigumula cha madzi, “moto” womwe ukutchulidwa pa 2 Petulo 3:7, udzawononga anthu oipa koma sudzawononga dziko lapansili. Mulungu akutilonjeza “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano” mmene “mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13) “Dziko lapansi latsopano,” kapena kuti nzika zatsopano zomwe zidzakhale padzikoli, zizidzalamuliridwa ndi “kumwamba kwatsopano” komwe ndi ulamuliro watsopano wa Mulungu. Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso.​—Chivumbulutso 21:1-4.