Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAGWIRIZANA NDI ZOTI ANTHU AZIMENYA NKHONDO?

Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo Masiku Ano?

Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo Masiku Ano?

Masiku ano anthu ambiri amaponderezedwa ndipo amapempha Mulungu kuti awathandize, koma zimangokhala ngati akulimbikira mtunda wopanda madzi. Kodi Mulungu amamvetsera anthu akamamupempha kuti awathandize? Kodi amathandiza anthu amene akumenya nkhondo n’cholinga choti asiye kuponderezedwa?

Aramagedo idzakhala mapeto a nkhondo zonse

Choyamba muyenera kudziwa kuti Mulungu sasangalala anthu akamavutika ndipo analonjeza kuti adzathetsa mavuto onse amene anthu akukumana nawo. (Salimo 72:13, 14) Mulungu anatilonjeza kuti: “Amene panopo mukuvutika mudzapeza mpumulo.” Ndiye kodi zimenezi zidzachitika liti? Baibulo limati zidzachitika “pa nthawi imene Ambuye Yesu adzaonekere kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake . . . Adzabwezera chilango kwa anthu osadziwa Mulungu ndi kwa anthu osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:7, 8) Zimenezi zidzachitika mtsogolomu pa nthawi imene Baibulo limanena kuti ‘tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,’ kapena kuti Aramagedo.—Chivumbulutso 16:14, 16.

Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu Khristu komanso angelo amphamvu kuti achotse anthu onse oipa ndipo sikudzakhalanso kuponderezana.—Yesaya 11:4; Chivumbulutso 19:11-16.

Tsopano taona kuti maganizo a Mulungu sanasinthe pa nkhani ya nkhondo. Amaonabe kuti nkhondo ndi njira yabwino yochotsera anthu oipa komanso yopulumutsira anthu ake kuti asamaponderezedwe. Taonanso kuti Mulungu ndi yemwe amasankha woti amenye nkhondo komanso nthawi yoyenera kumenya nkhondoyo. Monga taonera kale, Mulungu wasankha Mwana wake Yesu Khristu kuti adzamenye nkhondo yomwe idzathetse zoipa zonse komanso kuponderezedwa. Choncho masiku ano Mulungu sathandiza anthu akamamenya nkhondo ngakhale atamachita zimenezi pa zifukwa zimene akuona kuti n’zomveka.

Kuti timvetse chifukwa chake Mulungu sawathandiza, tiyerekeze chonchi: Bambo wina ali ndi ana awiri. Tsiku lina bamboyu atachokapo, anawo akuyamba kumenyana. Kenako akusiya kaye kumenyanako ndipo akuimbira foni bambo awo n’kuwauza zomwe zachitika. Mwana wina akuuza bambowo kuti anayambitsa ndewu ndi mnzakeyo, pomwe winayo akunena kuti anachita zimenezi chifukwa mnzakeyo anachita kumuputa dala. Mwana aliyense akuganiza kuti bambo akewo amuikira kumbuyo. Komabe bamboyo atamva zimene anawo afotokoza, akuwauza kuti asamenyanenso ndipo akuwauzanso kuti adzakambirane nkhaniyo akabwera. Anawo akusiyadi kumenyana, koma kenako akuyambiranso. Bamboyo atabwera akupeza ndewu ili mkati ndipo akupereka chilango kwa ana onsewo chifukwa sanamumvere.

Masiku anonso anthu akamamenyana pa nkhondo, amapempha Mulungu kuti awathandize. Komatu Mulungu sathandiza aliyense pa nkhondo zimenezi. Ndipo mofanana ndi zimene bambo wa m’chitsanzo chija anachita, Mulungu amatiuza kudzera m’Baibulo kuti: “Musabwezere choipa pa choipa.” (Aroma 12:17, 19) Ndipotu Mulungu safuna kuti tizimenya nkhondo, koma amafuna kuti tidikire kufikira nthawi imene adzathetse mavutowa pa Aramagedo. (Salimo 37:7) Bambo uja anakhumudwa kwambiri ataona kuti ana akewo sanamumvere. Mulungunso amakhumudwa kwambiri akamaona anthu akulephera kuugwira mtima n’kumamenyana ndi anzawo. Choncho, pa Aramagedo, Mulungu adzathetsa mavuto onse amene amachititsa kuti anthu azimenyana ndipo ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’ (Salimo 46:9; Yesaya 34:2) Ndiyetu Aramagedo idzakhala mapeto a nkhondo zonse.

Ufumu wa Mulungu udzathandiza kuti nkhondo zonse zithe. Yesu anatchula za Ufumu umenewu m’pemphero lake lomwe anthu ambiri amalidziwa. Iye anati: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumuwu udzathetsa nkhondo ndipo udzawononganso anthu onse oipa amene amayambitsa nkhondozo. * (Salimo 37:9, 10, 14, 15) Chimenechi n’chifukwa chake otsatira a Yesu samenya nkhondo, koma amayembekezera kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzakonze zinthu.—2 Petulo 3:13.

Koma kodi patenga nthawi yaitali bwanji kuti Mulungu adzachotse anthu oipa komanso kuti adzathetse mavutowa? Pali maulosi ambiri amene Baibulo linaneneratu, amene akukwaniritsidwa masiku ano. Zimenezi zikusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’ * (2 Timoteyo 3:1-5) Posachedwapa Ufumu wa Mulungu uchotsa anthu oipa komanso uthetsa mavutowa pa nkhondo ya Aramagedo.

Monga taonera m’nkhaniyi, anthu “osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu,” adzawonongedwa pa Aramagedo. (2 Atesalonika 1:8) Koma kumbukiraninso kuti Mulungu sasangalala anthu akamafa, kuphatikizapo anthu oipa. (Ezekieli 33:11) Popeza Mulungu “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe” pa nkhondoyi, iye akufuna kuti uthenga wabwino wonena za Ambuye Yesu, ‘ulalikidwe padziko lonse lapansi kumene kuli anthu’ mapeto asanafike. (2 Petulo 3:8, 9; Mateyu 24:14; 1 Timoteyo 2:3, 4) Choncho ntchito yolalikira imene a Mboni za Yehova amachita padziko lonse, ikuthandiza kuti anthu adziwe Mulungu komanso kuti azichita zimene amafuna. Zimenezi zidzathandiza kuti adzapulumuke n’kulowa m’dziko limene Mulungu watikonzera. Pa nthawi imeneyo nkhondo idzakhala mbiri yakale.

^ ndime 9 Ufumu wa Mulungu udzathetsanso imfa. Mungawerenge nkhani yakuti ”Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” m’magazini ino, yomwe ikusonyeza kuti Mulungu adzaukitsa anthu ambirimbiri amene anamwalira, kuphatikizapo amene anaphedwa pa nkhondo.

^ ndime 10 Kuti mudziwe zambiri zokhudza masiku otsiriza, onani mutu 9 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova.