Pitani ku nkhani yake

Kodi Chisautso Chachikulu N’chiyani?

Kodi Chisautso Chachikulu N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Chisautso chachikulu ndi nthawi imene padziko padzakhala mavuto aakulu kwambiri omwe sanachitikepo. Baibulo linaneneratu kuti chisautsochi chidzachitika mu “masiku otsiriza” kapena kuti mu “nthawi yamapeto.” (2 Timoteyo 3:1; Danieli 12:4) Ndipo chidzakhala “chisautso chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu analenga kudzafika nthawi imeneyo, ndipo sichidzachitikanso.”—Maliko 13:19; Danieli 12:1; Mateyu 24:21, 22.

Zimene zidzachitike pachisautso chachikulu

  •   Chipembedzo chonyenga chidzawonongedwa. Chipembedzo chonyenga chidzawonongedwa modzidzimutsa komanso mofulumira kwambiri. (Chivumbulutso 17:1, 5; 18:9, 10, 21) Bungwe la United Nations lomwe limaimira magulu amphamvu a ndale, ndi limene lidzawononge chipembedzo chonyenga pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu.​—Chivumbulutso 17:3, 15-18. a

  •   Chipembedzo choona chidzaukiridwa. Ezekieli anaona masomphenya onena za “Gogi wa kudziko la Magogi” yemwe amaimira mgwirizano wa mayiko. Gogi wa kudziko la Magogiyu adzayesa kuwononga anthu amene amalambira Yehova m’njira yovomerezeka. Komabe, Mulungu adzateteza atumiki ake kuti asawonongedwe.—Ezekieli 38:1, 2, 9-12, 18-23.

  •   Anthu oipa adzawonongedwa. Yesu adzaweruza anthu onse ndipo “adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi.” (Mateyu 25:31-33) Iye adzaweruza anthuwa potengera zomwe aliyense ankachitira “abale” ake omwe akalamulire limodzi naye kumwamba.​—Mateyu 25:34-46.

  •   Anthu Odzalamulira ndi Yesu adzasonkhanitsidwa. Anthu okhulupirika omwe anasankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu adzamaliza utumiki wawo wapadziko lapansi ndipo adzaukitsidwa n’kupita kumwamba.​—Mateyu 24:31; 1 Akorinto 15:50-53; 1 Atesalonika 4:15-17.

  •   Nkhondo ya Aramagedo. “Nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” yomwe idzachitike imatchedwanso “tsiku la Yehova.” (Chivumbulutso 16:14, 16; Yesaya 13:9; 2 Petulo 3:12) Pa nthawiyi, anthu omwe Khristu adzawaweruze kuti ndi oipa adzawonongedwa. (Zefaniya 1:18; 2 Atesalonika 1:6-10) Enanso omwe adzaphedwe pankhondoyi ndi magulu andale apadziko lonse omwe Baibulo limanena kuti ndi chilombo cha mitu 7.​—Chivumbulutso 19:19-21.

Zimene zidzachitike pambuyo pa chisautso chachikulu

  •   Satana ndi ziwanda zake adzamangidwa. Yesu yemwe ndi Mngelo wamkulu adzaponya Satana ndi ziwanda zake “m’phompho,” ndipo adzakhala ngati wafa. (Chivumbulutso 20:1-3) M’phomphomo, Satana adzakhala ngati ali kundende, choncho sadzatha kusocheretsa anthu.​—Chivumbulutso 20:7.

  •   Ulamuliro wa zaka 1000 udzayamba. Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira ndipo udzalamulira kwa zaka 1000. Ufumuwu udzabweretsa madalitso ambiri kwa anthu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:4, 6) Chisautso chachikulu chikadzatha, “khamu lalikulu la anthu” osawerengeka omwe ‘adzatuluke m’chisautso chachikulu,’ kapena kuti kupulumuka adzayamba kulamuliridwa ndi ufumuwu kwa zaka 1000 padziko lapansi.​—Chivumbulutso 7:9, 14; Salimo 37:9-11.

a Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti chipembedzo chonyenga chimaimira Babulo Wamkulu kapena kuti “hule lalikulu.” (Chivumbulutso 17:1, 5) Chilombo chofiira kwambiri chomwe chidzawononge Babulo Wamkulu chikuimira bungwe la mgwirizano wa mayiko lomwe cholinga chake ndi kukhazikitsa mtendere padziko lonse. Chilombochi chitaonekera koyamba chinkadziwika kuti League of Nations ndipo panopa chimadziwika ndi dzina loti United Nations.