Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Simupita Kunkhondo?

N’chifukwa Chiyani Simupita Kunkhondo?

A Mboni za Yehova sapita kunkhondo chifukwa cha zifukwa zotsatirazi:

  1. Timamvera Mulungu. Baibulo limati atumiki a Mulungu “adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,” ndiponso kuti “sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.

  2. Timamvera Yesu. Pa nthawi ina, Yesu anauza mtumwi Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Apa Yesu anasonyeza kuti otsatira ake sayenera kumenya nkhondo.

    Ophunzira a Yesu amamvera lamulo limene Yesuyo anawapatsa lakuti asakhale “mbali ya dziko,” kutanthauza kuti asamalowerere ngakhale pang’ono m’nkhani zandale kapena nkhondo. (Yohane 17:16) A Mboni za Yehova sachita zionetsero potsutsana ndi magulu amene asankha kumenya nkhondo ndiponso salimbana ndi anthu amene asankha kulowa usilikali.

  3. Timakonda ena. Yesu analamula ophunzira ake kuti ‘azikondana.’ (Yohane 13:34, 35) Choncho ophunzirawo anapanga ubale wapadziko lonse ndipo palibe amene angatenge zida n’kuyamba kuchita nkhondo ndi m’bale wake kapena mlongo wake.—1 Yohane 3:10-12.

  4. Timatsanzira Akhristu oyambirira. Buku lina linati: “Otsatira a Yesu oyambirira ankakana kupita kunkhondo chifukwa . . . ankadziwa kuti kumenya nkhondo n’kosagwirizana ndi chikondi chimene Yesu anawasonyeza komanso zimene anawaphunzitsa kuti azikonda ngakhale adani awo.” (Encyclopedia of Religion and War) Ponena za ophunzira a Yesu oyambirirawa, katswiri wina wa ku Germany, wamaphunziro a Baibulo, dzina lake Peter Meinhold anati: “Zinali zosatheka kuti munthu akhale Mkhristu pa nthawi imodzimodziyo n’kukhalanso msilikali.”

Ndife nzika zodalirika

A Mboni za Yehova ndi nzika zothandiza kwambiri m’dera limene akukhala ndipo si anthu amene angaopseze chitetezo cha mayiko amene akukhala. Timalemekeza olamulira, potsatira malamulo a m’Baibulo awo:

  • “Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.”—Aroma 13:1.

  • “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”—Mateyu 22:21.

Choncho timamvera malamulo, timapereka misonkho ndiponso timagwirizana ndi zimene boma likuchita pofuna kuthandiza anthu ake.