Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Anthu Apitiriza Kuwononga Dzikoli N’kufika Poti Silingakonzedwenso?

Kodi Anthu Apitiriza Kuwononga Dzikoli N’kufika Poti Silingakonzedwenso?

“M’badwo umapita ndipo m’badwo wina umabwera, koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”—MFUMU SOLOMO, YEMWE ANAKHALAKO M’ZAKA ZA M’MA 1000 B.C.E. *

Solomo, yemwe analemba nawo Baibulo, ankaona kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa anthufe ndi dziko lapansili. Anthufe timakhala ndi moyo nthawi yochepa pamene dzikoli lidzakhalako kwamuyaya. Izitu n’zoona chifukwa mibadwo ya anthu yakhala ikutha ina n’kubwera, koma dzikoli silitha ndipo likukwanitsabe kupereka zofunika ku zinthu zamoyo.

Anthu ena amanena kuti kuchokera nthawi imene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inatha, zinthu zasintha kwambiri komanso mofulumira padzikoli. Tikayerekeza ndi mmene zinthu zinalili zaka 70 zapitazo, zinthu zapita patsogolo kwambiri padzikoli pa nkhani ya mayendedwe, njira zolankhulirana komanso zinthu zamakono. Izi zachititsa kuti chuma cha m’mayiko ambiri chiziyenda bwino. Masiku ano anthu ambiri akukhala moyo wapamwamba womwe poyamba sankauganizira n’komwe. Komanso chiwerengero cha anthu padzikoli chawonjezeka kwambiri.

Komatu kusintha kwa zinthu kumeneku kwabweretsa mavuto ankhaninkhani. Anthu akuwononga kwambiri zinthu zachilengedwe moti akapitiriza kuchita zimenezi, dzikoli silidzathanso kupereka bwinobwino zinthu zimene zamoyo zimafunikira. Ndipotu asayansi ena akunena kuti mmene zinthu zilili padzikoli panopa, zikuoneka kuti tayamba kale kukolola zotsatira za zimene anthu akhala akuchita powononga zinthu zachilengedwe.

Baibulo linaneneratu kuti anthu ‘adzawononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Anthu ena akuona kuti nthawi imeneyo ndi inoyi. Kodi anthu apitirizabe kuwononga dzikoli mpaka pati? Kodi kapena lafika kale poti silingakonzedwenso?

 KODI DZIKOLI LAFIKA POTI SILINGAKONZEDWENSO?

Kodi anthu apitirizabe kuwononga dzikoli mpaka kufika poti silingakonzedwenso? Asayansi ena akuona kuti n’zovuta kudziwiratu yankho la funso limeneli. Koma akuda nkhawa kuti mwina kutsogoloku nyengo idzasintha kwambiri ndipo zimenezi zidzabweretsa mavuto osaneneka.

Mwachitsanzo, tiyeni tione mmene kusintha kwa nyengo kwakhudzira madzi oundana amene ali pamwamba pa nyanja ya Antarctic. Chifukwa cha kutentha kwa padziko lonse, madziwa ayamba kusungunuka ndipo anthu ena akukhulupirira kuti kutenthaku kukapitirira, madziwa asungunuka n’kufika poti sangamaundanenso. Madzi oundanawa, omwe amakhala pamwamba pa nyanja, amathandiza kuti kutentha kwa dzuwa kusamalowe m’nyanja. Koma chifukwa choti madziwa ayamba kusungunuka, kutentha kwa dzuwa kukumalowa m’nyanja. Zimenezi zikuchititsa kuti madzi a m’nyanjayi azitentha. Kutentha kwa madziwa kumapangitsa kuti madzi oundana apitirize kusungunuka. Madziwa akasungunuka, zimakhala zovuta kuti aundanenso. Zimenezi zimapangitsa kuti madzi a m’nyanja awonjezeke ndipo zingabweretse mavuto monga kusefukira kwa madzi.

ANTHU AKUWONONGA KWAMBIRI ZINTHU ZACHILENGEDWE

Anthu akhala akuyesa njira zosiyanasiyana kuti athetse vuto la kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe. Njira imodzi imene akugwiritsa ntchito ndi kulimbikitsa anthu kuti azigwiritsa ntchito zinthu zachilengedwe moyenera. Kodi zimenezi zathandizadi?

Ayi, chifukwa anthu akupitirizabe kuwononga zinthu zachilengedwe. Anthu akugwiritsa ntchito kwambiri zinthu zachilengedwe kuposa zimene dzikoli limabwezeretsa. Katswiri wina wa zinthu zachilengedwe ananena kuti: “Kunena zoona, sitikudziwa zimene tingachite kuti zinthu zachilengedwe zibwerere m’chimake.” Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

Komatu Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu, yemwe ndi Mlengi wa zinthu zonse, sadzalola kuti anthu awononge dzikoli n’kufika poti silingakonzedwenso. Lemba la Salimo 115:16 limati: “Dziko lapansi [Mulungu] analipereka kwa ana a anthu.” Izi zikusonyeza kuti dziko lapansili ndi ‘mphatso yabwino’ imene Atate wathu wakumwamba anatipatsa. (Yakobo 1:17) Kodi n’zotheka kuti Mulungu atipatse mphatso imene ingangogwira ntchito kwa kanthawi kenako n’kuwonongeka? N’zosatheka. Izi zikusonyeza kuti dzikoli silidzawonongeka n’kufika poti silingakonzedwenso.

 CHOLINGA CHA MULUNGU CHOKHUDZA DZIKO LAPANSILI

Buku la Genesis, lomwe ndi loyambirira m’Baibulo, limafotokoza mwatsatanetsatane mmene Mulungu analengera dzikoli. Limati poyamba dzikoli linali “lopanda maonekedwe enieni ndiponso lopanda kanthu. Panali madzi akuya kwambiri ndipo pamwamba pake panali mdima wokhawokha.” (Genesis 1:2) Vesili likusonyeza kuti “madzi,” omwe ndi ofunika kwambiri ku zamoyo, analipo padzikoli. Kenako Mulungu anati: “Pakhale kuwala.” (Genesis 1:3) Zimenezi zikusonyeza kuti kuwala kwa dzuwa kunadutsa mlengalenga n’kufika padzikoli zomwe zinapangitsa kuti padzikoli paziwala. Kenako Baibulo limanena kuti panakhala mtunda ndi nyanja. (Genesis 1:9, 10) Izi zitachitika, panamera ‘udzu, zomera zobala mbewu komanso mitengo yobala zipatso.’ (Genesis 1:12) Pa nthawiyi Mulungu anakonza zinthu zothandiza kuti padzikoli pakhale zamoyo. Mwachitsanzo, anakonza zoti zomera zizitha kupanga chakudya pogwiritsa ntchito dzuwa ndi madzi. Kodi cholinga cha Mulungu chinali chiyani pochita zonsezi?

Yankho la funso limeneli tikulipeza pa zimene mneneri Yesaya anafotokoza zokhudza Mulungu. Iye ananena kuti Mulungu ndi “amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, amene analikhazikitsa mwamphamvu, amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Apatu n’zoonekeratu kuti cholinga cha Mulungu n’choti padzikoli pazikhala anthu mpaka kalekale.

N’zomvetsa chisoni kuti anthu akhala akugwiritsa ntchito molakwika mphatso imeneyi ndipo akuiwononga. Koma zimenezi sizinasinthe cholinga cha Mulungu. Baibulo limanena kuti: “Mulungu si munthu, woti anganene mabodza, si mwana wa munthu, woti angadzimve kuti ali ndi mlandu. Kodi ananenapo kanthu koma osachita, analankhulapo kanthu kodi koma osakwaniritsa?” (Numeri 23:19) Mulungu sangalekerere kuti anthu awononge dzikoli mpaka kufika poti silingakonzedwenso. Ndipotu posachedwapa ‘awononga amene akuwononga dziko lapansi.’—Chivumbulutso 11:18.

ANTHU ADZAKHALABE PADZIKOLI MPAKA KALEKALE

Pa ulaliki wa paphiri, Yesu ananena kuti: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Pa ulalikiwu, Yesu anatchulanso njira imene Mulungu adzagwiritse ntchito pokonza dzikoli. Anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” Izi zikusonyeza kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu  kapena kuti boma lake pokwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi.—Mateyu 6:10.

Ponena za mmene Ufumuwu udzasinthire zinthu, Mulungu anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu adzalenga dziko lina kuti lilowe m’malo mwa dziko lapansili? Ayi, chifukwa Mulungu analenga bwinobwino zinthu zonse za padzikoli. M’malomwake, iye adzawononga anthu amene ‘akuwononga dzikoli.’ Anthu amenewa akuphatikizapo maboma amene akulamulira masiku ano. Mabomawa adzalowedwa m’malo ndi “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Kumwamba kwatsopano kukuimira Ufumu wa Mulungu ndipo dziko lapansi latsopano likuimira anthu omvera Mulungu amene adzakhale padzikoli. Anthu amenewa azidzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 21:1.

Kuti dzikoli libwerere m’chimake, Mulungu adzakonza zinthu zachilengedwe kuti ziyambenso kugwira ntchito bwinobwino ngati poyamba. Ponena za zimene Mulungu adzachite, munthu wina amene analemba nawo Baibulo ananena kuti: “Inu mwatembenukira dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zochuluka, mwalilemeretsa kwambiri.” Mulungu akadzachita zimenezi, dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Padzikoli pazidzapezeka zakudya za mwanaalirenji komanso nyengo idzakhala yabwino. Kuwonjezera pamenepa, Mulungu adzadalitsa dzikoli.—Salimo 65:9-13.

Mlembi wa Mohandas Gandhi, dzina lake Pyarelal, analemba zimene Gandhi yemwe anali mtsogoleri wa zachipembedzo ku India ananena. Iye anati: “Dzikoli limapereka zinthu zoti zikhoza kukwanira munthu wina aliyense. Koma chifukwa choti anthu ndi adyera, zinthuzi sizikwanira aliyense.” Ufumu wa Mulungu udzathandiza anthu kusiya mtima wadyera womwe umapangitsa kuti aziwononga zinthu zachilengedwe. Mneneri Yesaya analosera kuti Ufumu umenewu ukadzayamba kulamulira, anthu ‘sazidzavulazana kapena kuwononga’ dzikoli. (Yesaya 11:9) Panopa, anthu mamiliyoni ambiri a m’mayiko ndi zikhalidwe zosiyanasiyana ayamba kale kuphunzira zimene Mulungu amafuna. Anthuwa akuphunzitsidwa kuti azikonda Mulungu ndi anthu, kuti aziyamikira ndi kusamalira zinthu zachilengedwe zimene Mulungu anatipatsa komanso kuchita zinthu zothandizira kuti chifuniro cha Mlengi chikwaniritsidwe. Zimene akuphunzirazi zidzawathandiza kuti azidzakhala mosangalala dzikoli likadzakhala paradaiso.—Mlaliki 12:13; Mateyu 22:37-39; Akolose 3:15.

Mulungu sadzalola kuti dzikoli, lomwe analipanga bwino kwambiri, liwonongedwe n’kufika poti silingakonzedwenso

Nkhani yokhudza mmene Mulungu analengera zinthu yopezeka m’buku la Genesis, imamaliza ndi mawu akuti: “Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.” (Genesis 1:31) Mulungu sadzalola kuti dzikoli, lomwe analipanga bwino kwambiri, liwonongedwe n’kufika poti silingakonzedwenso. N’zolimbikitsa kudziwa kuti iye adzakwaniritsa cholinga chake choti padzikoli pakhale anthu mpaka kalekale. Iye analonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Kodi inuyo mukufuna kukhala m’gulu la “olungama,” amene adzakhala padzikoli kwamuyaya?

^ ndime 3 Mawuwa achokera m’Baibulo pa Mlaliki 1:4.