Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 23

Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka

Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka

1. Pa moyo wake wonse, kodi ndi nthawi iti imene Petulo ayenera kuti anakhumudwa kwambiri?

PA MOYO wake wonse, Petulo ayenera kuti ankakumbukirabe mmene zinamupwetekera mumtima pa nthawi ina pamene anaphana maso ndi Yesu. Kodi pa nthawiyi iye anaona kuti Yesu wakhumudwa kapena wamukwiyira chifukwa cha zimene wachita? Sitikudziwa, chifukwa mawu a Mulungu amangonena kuti: “Ambuye anacheuka ndi kuyang’ana Petulo.” (Luka 22:61) Yesu anali ataneneratu kuti Petulo adzamukana. Koma Petulo ananena kuti sangachite zimenezi. Choncho pa nthawiyi, Yesu atamuyang’ana, Petulo anadziwa kuti walakwa kwambiri. Ndipo anazindikira kuti wachita zimene ankanena kuti sangachite zija. Zimenezi zinam’khumudwitsa kwambiri ndipo ayenera kuti anali asanakhumudwepo chonchi pa moyo wake.

2. Kodi Petulo anafunika kuphunzira mfundo iti, nanga nkhani yake ingatithandize bwanji?

2 Komabe, sikuti Petulo analibiretu chiyembekezo. Chifukwa choti Petulo anali munthu wachikhulupiriro, anali ndi mwayi wokhululukidwa zimene anachitazo komanso kuphunzira kwa Yesu mfundo ina yofunika kwambiri yokhudza kukhululuka. Tonsefe tikufunika kuphunzira mfundo imeneyi. Tiyeni tikambirane zimene Petulo anakumana nazo zomwe zinachititsa kuti aphunzire mfundo imeneyi.

Panali Zambiri Zoti Aphunzire

3, 4. (a) Kodi Petulo anafunsa Yesu funso liti, ndipo ayenera kuti anali ndi maganizo otani pofunsa funsoli? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti Petulo anali ndi maganizo omwe anthu ambiri pa nthawiyo anali nawo?

3 Petulo ali mumzinda wa kwawo wa Kaperenao, kutatsala pafupifupi miyezi 6 kuti zimenezi zichitike, anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, kodi m’bale wanga angandichimwire kangati ndipo ine n’kumukhululukira? Mpaka nthawi 7 kodi?” Pamenepa mwina Petulo ankaganiza kuti kukhululukira munthu ka 7 ndiye kuti wamukhululukira kokwanira chifukwa nthawi imeneyo atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa kuti munthu azikhululukira mnzake katatu kokha basi. Koma Yesu anamuyankha kuti: “Osati nthawi 7 zokha ayi, koma, mpaka nthawi 77.”—Mat. 18:21, 22.

4 Kodi Yesu ankatanthauza kuti Petulo azilemba nthawi iliyonse imene munthu wamulakwira? Ayi. Yesu ponena kuti munthu azikhululukira mnzake ka 77, osati ka 7 kokha ngati mmene Petulo ankaganizira, ankatanthauza kuti kukhululuka kulibe malire. (1 Akor. 13:4, 5) Yesu anasonyeza kuti Petulo anatengera mtima wosakhululukira ena womwe unali wofala kwambiri nthawi imeneyo. Anthu amene anali ndi maganizo amenewa ankakumbukira nthawi iliyonse imene mnzawo wawalakwira. Iwo ankachita zimenezi ngati kuti analemba penapake mofanana ndi mmene wokongoza ndalama ankachitira polemba ngongole zimene ena atenga. Komabe, Mulungu amafuna kuti tizikhululukira ena mopanda malire.Werengani  1 Yohane 1:7-9.

5. kodi ndi nthawi iti pamene tingadziwe kuti kukhululuka n’kofunika kwambiri?

5 Petulo sanatsutse zimene Yesu ananenazo. Koma kodi mfundo imene Yesu anam’phunzitsayi inamufika pa mtima? Nthawi zambiri timazindikira kuti kukhululuka n’kofunika ifeyo tikalakwa kwambiri ndipo tikufunitsitsa kuti ena atikhululukire. Choncho, tiyeni tionenso zimene zinachitika Yesu atatsala pang’ono kuphedwa. Pa nthawi yovutayi, panali zinthu zingapo zimene Petulo analakwitsa zomwe zinafunika kuti Mbuye wake amukhululukire.

Panali Zambiri Zoti Amukhululukire

6. Kodi Petulo anatani pamene Yesu ankasambitsa mapazi a atumwi ake, koma kodi Yesu anatani Petulo atachita zimenezi?

6 Usiku woti Yesu aphedwa mawa lake unali nthawi yapadera kwambiri chifukwa anali ndi zambiri zoti aphunzitse atumwi ake. Chinthu china chimene anafunika kuwaphunzitsa ndi kufunika kokhala wodzichepetsa. Yesu anapereka chitsanzo pa nkhani imeneyi pomwe anadzichepetsa n’kusambitsa mapazi a atumwi akewo, ntchito imene nthawi zambiri inali ya akapolo. Poyamba Petulo anadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi ndipo anakana kuti amusambitse mapazi. Kenako, iye anauza Yesu kuti asangomusambitsa mapazi okha koma amusambitsenso manja ndi mutu womwe. Yesu sanam’psere mtima Petulo koma anamufotokozera bwinobwino tanthauzo la zimene ankachitazo.—Yoh. 13:1-17.

7, 8. (a) Kodi Petulo anachitanso zinthu zina ziti zimene zikanachititsa Yesu kupsa mtima? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali munthu wokoma mtima ndiponso wokhululuka?

7 Komabe patangopita nthawi pang’ono, atumwiwo anachitanso zinthu zina zimene zinakam’psetsa mtima Yesu. Iwo anasonyeza mtima wodzikuza ndipo anayamba kukangana kuti wamkulu ndani. N’zosakayikitsa kuti nayenso Petulo ankakangana nawo pa nkhani yochititsa manyaziyi. Ngakhale zinali choncho, Yesu anawalangiza mwachifundo ndipo anawayamikira kuti anachita bwino pokhalabe okhulupirika kwa iye monga Mbuye wawo. Komabe, iye analosera kuti atumwi akewo adzamuthawa. Petulo anayankha kuti sangamusiye Yesu ngakhale atawopsezedwa kuti aphedwa. Koma Yesu analosera kuti usiku womwewo Petulo akana Mbuye wake katatu, tambala asanalire kawiri. Komabe, Petulo anatsutsa zimenezi ndipo anachita kunena modzitama kuti iye adzakhala wokhulupirika kwambiri kuposa atumwi ena onsewo.—Mat. 26:31-35; Maliko 14:27-31; Luka 22:24-28; Yoh. 13:36-38.

8 Kodi Yesu anam’psera mtima? Ayi, ndipo pa nthawi yovuta yonseyi, Yesu anapitirizabe kuona zinthu zabwino zokha mwa atumwi ake opanda ungwirowo. Yesu ankadziwa kuti Petulo amulakwira, komabe ananena kuti: “Ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe. Chotero iwenso, ukabwerera, ukalimbikitse abale ako.” (Luka 22:32) Choncho, Yesu anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Petulo adzazindikira kulakwa kwake ndipo adzayambiranso kutumikira mokhulupirika. Zimenezi zikusonyezeratu kuti Yesu anali munthu wokoma mtima ndiponso wokhululuka.

9, 10. (a) Kodi Petulo analakwitsa chiyani ali m’munda wa Getsemane? (b) Kodi zimene Petulo ankalakwitsa zimatikumbutsa chiyani?

9 Patapita nthawi, Yesu ndi atumwi ali m’munda wa Getsemane, Petulo analakwitsanso zinthu zingapo ndipo anafunika kulangizidwa. Yesu anapita kokapemphera ndipo anauza Petuloyo, komanso Yakobo ndi Yohane kuti akhale maso. Pa nthawiyi, Yesu ankavutika maganizo ndipo anafunika kulimbikitsidwa, koma Petulo ndi atumwi enawo anagona tulo kangapo konse. Yesu ananena mawu osonyeza kuti ankawamvetsa komanso kuti anawakhululukira. Iye anati: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”—Maliko 14:32-41.

10 Posakhalitsa, panafika chigulu cha anthu chitanyamula zounikira, malupanga ndi zibonga. Imeneyi inali nthawi yofunika kuchita zinthu mosamala komanso mwanzeru. Koma Petulo anachita zinthu mopupuluma ndipo anatenga lupanga n’kudula nalo khutu la munthu wina dzina lake Makasi, yemwe anali wantchito wa mkulu wa ansembe. Koma Yesu anadzudzula Petulo mwachikondi n’kupoletsa balalo, kenako anafotokoza mfundo yofunika kwambiri pa nkhani yopewa zachiwawa, ndipo ndi imene Akhristu amatsatira mpaka pano. (Mat. 26:47-55; Luka 22:47-51; Yoh. 18:10, 11) Pofika pa nthawiyi, Petulo anali atachita zinthu zambirimbiri zofunika kuti Mbuye wake amukhululukire. Zimenezi zikutikumbutsa mfundo yakuti tonsefe timachimwa nthawi zambiri. (Werengani Yakobo 3:2.) Timalakwitsa tsiku lililonse ndipo timafuna kuti Mulungu azitikhululukira. Komabe usiku umenewu Petulo analakwitsanso zinthu zina zambiri.

Chimene Petulo Analakwitsa Kwambiri

11, 12. (a) Kodi Petulo anasonyeza bwanji kulimba mtima Yesu atamangidwa? (b) Kodi zimene Petulo anachita zinasiyana bwanji ndi zimene ananena poyamba?

11 Yesu anauza gulu la anthulo kuti ngati akufuna iyeyo, asiye atumwi ake kuti azipita. Petulo ankangoyang’ana mothedwa nzeru pamene gululo linkamanga Yesu. Kenako anathawa ngati mmene anachitira atumwi enawo.

12 Petulo ndi Yohane atathawa, ayenera kuti anakaima pafupi ndi nyumba ya Anasi, yemwe poyamba anali mkulu wa ansembe, ndipo kumeneku n’kumene anayambira kumuzenga Yesu mlandu. Pomwe Yesu ankachoka naye kumeneko, Petulo ndi Yohane ankatsatira “chapatali ndithu.” (Mat. 26:58; Yoh. 18:12, 13) Zimenezi zikusonyeza kuti Petulo sanali wamantha chifukwa panafunika kulimba mtima kuti munthu azitsatira Yesu pa nthawiyi. Gululo linali ndi zida ndipo Petulo anali atapalamula kale povulaza mmodzi wa anthu omwe anali pagululo. Komabe zimene Petulo anachitazi zinali zosiyana ndi zimene ananena zija. Paja iye ananena kuti adzakhalabe wokhulupirika ndipo adzalolera kufa ndi Mbuye wakeyo ngati pangafunike kutero.—Maliko 14:31.

13. Kodi njira yabwino yotsatirira Yesu ndi iti?

13 Mofanana ndi Petulo, anthu ambiri masiku ano amatsatiranso Khristu “chapatali ndithu.” Safuna kuti anthu adziwe zoti ndi otsatira a Khristu. Komabe monga Petulo ananenera nthawi ina, njira yabwino yotsatirira Khristu ndi kuchita zonse zimene iye anaphunzitsa ndiponso kutsatira chitsanzo chake pa zinthu zonse mosaopa kanthu.—Werengani 1 Petulo 2:21.

14. Kodi Petulo ankachita chiyani pa nthawi imene Yesu ankazengedwa mlandu?

14 Petulo anatsatirabe mochenjera gulu limene linagwira Yesu lija mpaka anafika pachipata cha nyumba ina yaikulu kwambiri ya ku Yerusalemu. Nyumbayi inali ya Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe wolemera komanso wolemekezeka kwambiri. Nthawi zambiri nyumba zotere zinkakhala ndi bwalo mkati mwake, ndipo kutsogolo kwake kunkakhala chipata. Petulo anafika pachipatapo koma anakanizidwa kulowa. Kenako Yohane, yemwe pa nthawiyi anali atalowa kale, anabwera n’kudzapempha mtsikana yemwe anali mlonda wapachipatapo kuti amulole Petulo kuti alowe. Zikuoneka kuti Petulo atalowa sanakakhale limodzi ndi Yohane komanso sanakalowe m’nyumba mmene munali Yesu kuti akakhale pafupi ndi Mbuye wake. Iye anakhala pabwalo ndi akapolo ndi antchito ena omwe ankaotha moto n’kumaona mboni zabodza zikulowa ndi kutuluka m’nyumba momwe ankazengera mlanduwo.—Maliko 14:54-57; Yoh. 18:15, 16, 18.

15, 16. Fotokozani mmene ulosi wa Yesu wonena kuti Petulo adzamukana katatu unakwaniritsidwira.

15 Chifukwa cha kuwala kwa motowo, mtsikana amene analola kuti Petulo alowe uja anayamba kumuona bwinobwino ndipo anamuzindikira. Kenako ananena kuti: “Inunso munali ndi Yesu wa ku Galileyayu!” Petulo anadzidzimuka ndi mawu amenewa ndipo anakana zoti akudziwa Yesu, mpaka ananena kuti sakudziwa zimene mtsikanayo akunena. Kenako anachoka n’kukaima pafupi ndi chipata pofuna kuti anthu asamuzindikire. Koma mtsikana wina anamuzindikiranso ndipo ananena mawu angati amene mtsikana woyamba uja ananena. Iye anati: “Bambo awa anali limodzi ndi Yesu Mnazaretiyu.” Koma Petulo anakanitsitsa ndipo analumbira kuti: “Ndithudi munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” (Mat. 26:69-72; Maliko 14:66-68) Mwina Petulo atakana Yesu kachiwirika m’pamene anamva kulira kwa tambala. Koma anasokonezeka maganizo ndi zimene zinkachitikazi moti sanakumbukire ulosi umene Yesu ananena uja.

16 Petulo anayesetsabe kuti anthu asamuzindikire koma patangopita nthawi pang’ono, gulu lina la anthu lomwe linali m’bwalomo linafika pafupi ndi pomwe iye anali. Mmodzi wa anthuwo anali m’bale wake wa Makasi, kapolo amene Petulo anamudula khutu uja. Munthuyo anauza Petulo kuti: “Ndinakuona iwe m’munda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” Koma Petulo anakana kwamtuwagalu kuti zimenezi si zoona. Choncho iye analumbira, ndipo n’kutheka kuti ananena kuti tsoka limugwere ngati akunama. Aka kanali kachitatu kuti Petulo akane Yesu. Atangomaliza kulankhula, tambala analira ndipo kameneka kanali kachiwiri Petulo kumva tambala akulira usiku umenewu.—Yoh. 18:26, 27; Maliko 14:71, 72.

“Ambuye anacheuka ndi kuyang’ana Petulo”

17, 18. (a) Kodi Petulo anatani atazindikira kuti walakwira kwambiri Mbuye wake? (b) Kodi Petulo ayenera kuti ankaganiza chiyani?

17 Pa nthawiyi, Yesu anali atatuluka naye n’kufika pakhonde la nyumbayo pomwe ankatha kuona bwinobwino bwalo la nyumbayo. Monga tafotokozera kumayambiriro kwa nkhaniyi, nthawi imeneyi ndi imene Yesu anaphana maso ndi Petulo. Petulo anazindikira kuti walakwira kwambiri Mbuye wakeyu. Choncho anachoka pabwalopo ali ndi chisoni kwambiri ndipo ankangoyenda m’misewu ya mumzindawo. Komabe ankatha kuona njira chifukwa kunja kunali mwezi. Pa nthawiyi m’maso mwake munali mutalengeza misozi ndipo kenako anayamba kulira kwambiri chifukwa chopwetekedwa mtima.—Maliko 14:72; Luka 22:61, 62.

18 Munthu akazindikira kuti walakwa kwambiri, amaganiza kuti sakhululukidwa ndipo mwina ndi mmenenso Petulo ankaganizira. Koma kodi Yesu anamukhululukira Petulo?

Kodi Petulo Anachita Tchimo Losakhululukidwa?

19. Kodi Petulo anamva bwanji chifukwa cha zimene anachita, ndipo tikudziwa bwanji kuti iye sanafooke chifukwa cha zimenezi?

19 Petulo ayenera kuti anakhumudwa kwambiri kutacha n’kumva zimene zamuchitikira Yesu. Ayenera kuti anadziimba mlandu kwambiri atazindikira kuti Yesu anafa madzulo a tsiku limenelo, atazunzidwa kwa maola ambiri. Petulo ayeneranso kuti zinkamuwawa kwambiri akaganizira kuti anathandizira nawo kuti Mbuye wake amve kupweteka kwambiri pa tsiku lake lomaliza kukhala ndi moyo padziko lapansi monga munthu. Ngakhale kuti Petulo anali ndi chisoni kwambiri chonchi, sanafooke. Tikudziwa zimenezi chifukwa pasanapite nthawi yaitali, anayamba kusonkhana ndi atumwi anzake. (Luka 24:33) N’zosakayikitsa kuti atumwi onse anali ndi chisoni kwambiri chifukwa cha zimene anachita usiku wovuta umenewu, komabe anayesetsa kulimbikitsana.

20. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Petulo anachita?

20 Apa titha kuona kuti Petulo anaganiza bwino kwambiri. Mtumiki wa Mulungu akachita tchimo lalikulu, ayenera kuyesetsa kudzukanso m’malo momangoganizira kukula kwa tchimo lakelo. (Werengani Miyambo 24:16.) Petulo anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chenicheni posonkhana ndi atumwi anzake ngakhale kuti anakhumudwa kwambiri. Munthu akakhumudwa kwambiri kapena akachita tchimo, akhoza kuganiza zosiya kusonkhana ndi Akhristu anzake, koma zimenezi n’zosathandiza. (Miy. 18:1) Chinthu chanzeru ndi kupitirizabe kusonkhana ndi atumiki anzathu, kuti tipezenso mphamvu mwauzimu.—Aheb. 10:24, 25.

21. Kodi Petulo anamva nkhani yotani atasonkhana ndi abale ake?

21 Petulo ali kunyumba kumene anasonkhana ndi abale akewo, anamva zoti thupi la Yesu lasowa m’manda momwe analiika ngakhale kuti khomo la mandawo linatsekedwa bwinobwino. Choncho, Petulo ndi Yohane anathamangira kumandako. Yohane, amene mwina anali wocheperapo poyerekeza ndi Petulo, ndi amene anayambirira kufika pamandapo. Iye anapezadi mandawo ali wotsegula koma anachita mantha kulowamo. Koma Petulo atafika, sanachite mantha. Ngakhale kuti anali ali wefuwefu, anangofikira kulowa m’mandamo ndipo anapeza kuti Yesu mulibe.—Yoh. 20:3-9.

22. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Petulo asiye kuda nkhawa ndiponso kukayika?

22 Kodi Petulo anakhulupirira kuti Yesu waukitsidwa? Poyamba sanakhulupirire ngakhale kuti akazi ena okhulupirika anamuuza kuti auzidwa ndi angelo zoti akauze anthu kuti Yesu wauka kwa akufa. (Luka 23:55, 56; 24:1-11) Koma pofika madzulo a tsiku limenelo, Petulo anali atasiya kuda nkhawa ndiponso kukayika. Yesu anali ali ndi moyo monga mngelo wamphamvu ndipo anaonekera kwa atumwi ake onse. Koma asanaonekere kwa atumwi ake onsewo anaonekera kaye kwa Petulo. Tsiku limenelo atumwiwo ananena kuti: “N’zoonadi, Ambuye wauka kwa akufa ndipo waonekera kwa Simoni!” (Luka 24:34) Komanso mtumwi Paulo nthawi ina analemba za tsiku lapadera limene Yesu “anaonekera kwa Kefa, kenako kwa atumwi 12 aja.” (1 Akor. 15:5) Kefa ndi Simoni ndi mayina ena a Petulo. Choncho zikuoneka kuti Yesu anaonekera kwa Petulo ali yekha.

Petulo analakwitsa zinthu zambiri zofunika kuti Mbuye wake amukhululukire. Nafenso timalakwitsa tsiku lililonse ndipo timafuna kuti Mulungu azitikhululukira

23. N’chifukwa chiyani Akhristu amene achita tchimo ayenera kukumbukira nkhani ya Petulo?

23 Baibulo silinena zimene Yesu ndi Petulo anakambirana pa nthawiyo. Koma tingathe kuona kuti Petulo anasangalala kwambiri kuona Mbuye wake amene ankamukonda kwambiri ataukitsidwa. Anasangalalanso kukhala ndi mwayi womuuza Yesu kuti anamva chisoni kwambiri ndi zimene anachita zija komanso kumuuza kuti walapa. Pa nthawiyi Petulo ankalakalaka kuti Mbuye wakeyo amukhululukire. Ndipo sitingakayikire kuti Yesu anamukhululukiradi ndi mtima wonse. Mkhristu amene wachimwa ayenera kukumbukira nkhani ya Petulo. Tikachimwa, tisamaganize kuti Mulungu sangatikhululukire. Yesu anasonyeza bwino kwambiri kuti Atate wake “amakhululuka ndi mtima wonse.”—Yes. 55:7.

Umboni Wina Wosonyeza Kuti Yesu Anakhululukira Petulo

24, 25. (a) Fotokozani zimene zinachitika Petulo atapita kukapha nsomba m’nyanja ya Galileya. (b) Kodi Petulo anatani kutacha, Yesu atachita chozizwitsa?

24 Yesu anauza atumwi ake kuti apite ku Galileya kuti akakumane nayenso. Atafika kumeneko, Petulo anaganiza zokapha nsomba m’nyanja ya Galileya ndipo anapita ndi anzake angapo. Zaka zingapo m’mbuyomo, Petulo ankagwira ntchito yake ya usodzi m’nyanja yomweyi. Phokoso la ngalawa, mafunde, ndiponso ntchito yokoka khoka, sizinali zachilendo kwa iye. Koma usiku umenewo iwo sanaphe kanthu.—Mat. 26:32; Yoh. 21:1-3.

Petulo analumphira m’nyanja n’kusambira kupita kumtunda

 

25 Komabe, kunja kukucha, munthu wina amene anali kugombe anawaitana n’kuwauza kuti aponye ukonde wawo mbali ina ya ngalawayo. Iwo anachitadi zimenezi ndipo anapha nsomba 153. Petulo anazindikira kuti munthuyo ndi Yesu ndipo analumphira m’nyanja n’kusambira kupita kumtunda. Ophunzira enawonso atafika kumtundako, Yesu anawapatsa nsomba zowotcha pamakala. Komabe maganizo ake anali pa Petulo.—Yoh. 21:4-14.

26, 27. (a) Kodi Yesu anapatsa Petulo mwayi wotani? (b) Kodi Yesu anachita chiyani posonyeza kuti anakhululukira Petulo ndi mtima wonse?

26 Yesu anafunsa Petulo ngati amakonda Mbuye wakeyo “koposa izi.” Ponena mawu amenewa ayenera kuti ankaloza nsombazo. Ankafuna kudziwa ngati Petulo ankakonda kwambiri ntchito yosodza kuposa mmene ankakondera iyeyo. Yesu anafunsa Petulo funso limeneli katatu ngati mmenenso Petuloyo anakanira Mbuye wakeyo katatu. Iye anachita zimenezi pofuna kupatsa Petulo mwayi wotsimikizira pamaso pa atumwi enawo kuti amamukonda. Petulo atayankha kuti amakonda Yesu, anamuuza njira imene angasonyezere chikondi chimenechi. Iye anayenera kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba ndiponso kuphunzitsa ndi kusamalira nkhosa za Khristu, zomwe ndi atumiki ake okhulupirika.—Luka 22:32; Yoh. 21:15-17.

27 Apa Yesu anasonyeza kuti Petulo anali adakali munthu wofunika kwambiri kwa iye komanso kwa Atate wake. Yesu ankaona kuti Petulo angagwire ntchito yofunika kwambiri mumpingo motsogoleredwa ndi Khristu. Umenewutu ndi umboni wamphamvu wakuti Yesu anakhululukira Petulo ndi mtima wonse. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinamulimbikitsa kwambiri Petulo.

28. Kodi Petulo anachita zinthu ziti zogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake?

28 Petulo anachita utumiki wake mokhulupirika kwa zaka zambiri. Iye analimbikitsa atumiki anzake monga mmene Yesu anamulamulira madzulo a tsiku limene anafa. Petulo anagwira ntchito moleza mtima komanso mokoma mtima poweta ndiponso podyetsa otsatira a Khristu. Munthu ameneyu, wodziwikanso kuti Simoni, anachitadi zinthu mogwirizana ndi dzina limene Yesu anam’patsa lakuti Petulo kapena kuti Thanthwe. Iye anakhala wodalirika, wolimba ndiponso wolimbikitsa ena kuchita zabwino mumpingo. Umboni wa zimenezi timaupeza m’makalata awiri amene Petulo analemba omwe ndi mbali ya Baibulo. Makalata amenewa amasonyezanso kuti Petulo sanaiwale phunziro lofunika kwambiri limene anaphunzira kwa Yesu lokhudza kukhululuka.—Werengani 1 Petulo 3:8, 9; 4:8.

29. Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Petulo komanso chifundo cha Yesu?

29 Nafenso tiyenera kuphunzirapo kanthu pa chitsanzo cha Petulo. Kodi tsiku lililonse timapempha Mulungu kuti atikhululukire zimene tamuchimwira? Ndiyeno kodi timakhulupirira kuti watikhululukiradi ndipo sakutionanso ngati munthu wochimwa? Nanga kodi ifenso timakhululukira anzathu? Ngati timachita zimenezi, ndiye kuti timatsanzira chikhulupiriro cha Petulo ndiponso chifundo cha Mbuye wake.