Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 21

Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira

Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira

1-3. Kodi ndi zinthu ziti zimene Petulo anaona Yesu akuchita, nanga anakumana ndi zotani usiku wa tsiku limenelo?

PETULO anapalasa ngalawa mwamphamvu m’nyanja ya Galileya ngakhale kuti kunja kunali mdima. Atayang’ana chakum’mawa, n’kuona kuti kukuoneka mbuu anaganiza kuti kunja kwayamba kucha. Apa n’kuti msana ndiponso mapewa ake zikumupweteka chifukwa chopalasa ngalawayo kwanthawi yaitali. Tsitsi lake linali lili petupetu chifukwa cha chimphepo chomwenso chinkachititsa mafunde panyanjayo. Analinso atanyowa ndi mafundewo koma anapitirizabe kupalasa.

2 Pa nthawiyi n’kuti Petulo ndi anzake atam’siya Yesu ali yekha kumtunda. Pa tsikuli, iwo anaona Yesu akudyetsa khamu la anthu ndi nsomba ziwiri ndiponso mikate isanu yokha. Yesu atachita zimenezi, anthuwo anafuna kumugwira kuti amulonge ufumu, koma iye anakana chifukwa sankafuna kulowerera nawo ndale. Komanso anayesetsa kuthandiza otsatira ake kuti asamalowerere ndale. Pofuna kuzemba gulu la anthulo, Yesu anauza ophunzira ake kuti akwere ngalawa n’kupita tsidya lina la nyanjayo. Ndipo iye anakwera m’phiri yekhayekha kukapemphera.—Maliko 6:35-45; werengani Yohane 6:14-17.

3 Pa nthawi imene ophunzirawa ankanyamuka, mwezi unali uli pamwamba koma tsopano unali utayamba kulowa. Ngakhale zinali choncho, iwo anali atangoyenda kamtunda kochepa chifukwa cha mafunde. Zinali zovuta kuti ophunzirawa azimvana chifukwa cha mphepo, mafunde ndiponso chifukwa chotanganidwa ndi kupalasa. N’kutheka kuti pa nthawiyi Petulo ankaganizira zinthu zambiri zimene zinachitika pa moyo wake.

Petulo anali ataphunzira zambiri pa zaka ziwiri zimene anakhala wotsatira wa Yesu koma panalinso zambiri zoti aphunzire

4.N’chifukwa chiyani tingati Petulo ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe?

4 Panali patatha zaka zoposa ziwiri kuchokera pamene Petulo anakhala wotsatira wa Yesu wa ku Nazarete. Iye anali ataphunzira zambiri koma panalinso zambiri zoti aphunzire. Mwachitsanzo, Petulo ankalephera kuchita zinthu zina chifukwa cha mantha komanso anali ndi vuto lokayikira. Komabe ankayesetsa kuthana ndi mavuto akewa ndipo ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa tonsefe. Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Petulo.

“Ifetu Tapeza Mesiya”

5, 6. Kodi Petulo ankagwira ntchito yanji?

5 Petulo ankakumbukirabe tsiku limene anakumana ndi Yesu. Andireya, yemwe anali mchimwene wake, anamuuza uthenga wochititsa chidwi wakuti: “Ifetu tapeza Mesiya.” Ichi chinali chiyambi choti Petulo adziwane ndi Yesu.—Yoh. 1:41.

6 Petulo ankakhala ku Kaperenao, mzinda womwe unali mphepete mwa nyanja ya Galileya. Iye ndi Andireya ankagwira ntchito ya usodzi pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane, omwe anali ana a Zebedayo. Petulo anali ndi mkazi ndipo ankakhalanso ndi apongozi ake aakazi ndiponso Andireya. Kuti msodzi athe kusamalira banja lalikulu chonchi, ankafunika kugwira ntchito mwakhama. Pogwira ntchitoyi, asodzi ankachezera usiku wonse. Iwo ankagawana magulu awiri ndipo gulu lililonse linkakwera m’ngalawa yake. Kenako ankaponya khoka m’nyanja n’kuyamba kulikoka kuti akokolole nsomba zonse zimene zili pamalopo. Kukacha, ankakhala ndi chintchito chachikulu chifukwa ankafunika kusankha nsombazo, kuziika m’magulu, kenako n’kuzigulitsa. Ankafunikanso kutsuka ndiponso kusoka makoka amene ang’ambika.

7. Kodi Petulo anamva zotani zokhudza Yesu, nanga n’chifukwa chiyani nkhaniyi inali yosangalatsa?

7 Baibulo limanena kuti poyamba, Andireya anali wophunzira wa Yohane M’batizi. N’zosakayikitsa kuti Petulo ankamvetsera mwachidwi mchimwene wakeyu akamamuuza zimene Yohane ankalalikira. Tsiku lina Andireya anaona Yohane akuloza Yesu n’kunena kuti: “Onani, Mwanawankhosa wa Mulungu!” Nthawi yomweyo Andireya anakhala wotsatira wa Yesu ndipo anakauza Petulo mosangalala nkhani yabwino yakuti Mesiya wafika. (Yoh. 1:35-40) Pa nthawiyi n’kuti patatha zaka 4,000 kuchokera pamene anthu anapandukira Mulungu m’munda wa Edene ndipo Yehova Mulungu analonjeza kuti kudzabwera munthu wapadera amene adzathandize anthu kukhala ndi chiyembekezo chenicheni. (Gen. 3:15) Andireya anali atakumana ndi Mpulumutsi ameneyu, yemwe anali Mesiya. Choncho, nayenso Petulo anathamanga kukakumana ndi Yesu.

8. Kodi dzina limene Yesu anapereka kwa Petulo limatanthauza chiyani, nanga n’chifukwa chiyani anthu ena amaona kuti dzinali n’losayenera kwa Petulo?

8 Poyamba, Petulo ankadziwika ndi dzina lakuti Simoni. Koma atakumana ndi Yesu, Yesuyo anamuyang’ana n’kumuuza kuti: “‘Iwe ndiwe Simoni mwana wa Yohane, udzatchedwa Kefa’ (dzina limene kumasulira kwake ndi Petulo).” (Yoh. 1:42) Dzina lakuti “Kefa” limatanthauza “mwala” kapena “thanthwe.” Zikuoneka kuti mawu a Yesu amenewa anali ulosi. Iye anaona kuti m’tsogolo Petulo angathe kudzakhala thanthwe, kutanthauza kuti angadzakhale munthu wodalirika komanso wolimbikitsa otsatira a Khristu. Koma kodi Petulo ankadzionanso choncho? N’zokayikitsa. Ndipo anthu ena masiku ano amene amawerenga Mauthenga Abwino, saona kuti Petulo anali munthu wodalirika kwenikweni. Ena amati anali munthu wokayikakayika ndiponso wosachedwa kusintha maganizo.

9. Kodi Yehova ndi Mwana wake amaganizira kwambiri za chiyani, nanga n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti iwo angapeze zabwino mwa ife?

9 N’zoona kuti Petulo ankalakwitsa zinthu zina ndipo Yesu ankadziwa zimenezo. Koma mofanana ndi Atate wake, Yehova, nthawi zonse Yesu ankaganizira kwambiri zomwe anthu amachita bwino. Ndipo Yesu anaona kuti Petulo anali ndi makhalidwe abwino, choncho ankafuna kumuthandiza kuti akulitse makhalidwewo. Masiku anonso, Yehova ndi Mwana wake amaona zabwino mwa ife. Mwina tingakayikire zoti Yehova ndi Yesu angapeze zabwino mwa ife. Koma sitiyenera kukayikira zimenezi. Mofanana ndi Petulo, tikufunika kusonyeza kuti tikufunitsitsa kuti Yehova atiphunzitse ndiponso kutiumba.—Werengani 1 Yohane 3:19, 20.

“Usachite Mantha”

10. Kodi Petulo anaona zinthu ziti, komabe kodi anachita chiyani pambuyo pake?

10 Zikuoneka kuti Petulo anapita ndi Yesu pa maulendo ake ena okalalikira kumadera ena. Choncho, n’kutheka kuti anaona chozizwitsa choyamba cha Yesu, chosandutsa madzi kukhala vinyo, paphwando la ukwati ku Kana. Koma chofunika kwambiri n’choti Petulo anamva ulaliki wa Yesu umene unkathandiza anthu kukhala ndi chiyembekezo. Ulalikiwu unali wonena za Ufumu wa Mulungu. Koma ngakhale kuti anaona zonsezi, iye anasiya kuyenda ndi Yesu n’kukapitiriza ntchito yake ya usodzi. Komabe patatha miyezi ingapo, Petulo anakumananso ndi Yesu ndipo nthawi imeneyi Yesu anamupempha kuti akhale wotsatira wake.

11, 12. (a) Kodi Petulo anagwira ntchito yotani usiku wonse? (b) Kodi Petulo ayenera kuti ankaganizira mafunso ati pamene ankamvetsera ulaliki wa Yesu?

11 Petulo ndi anzake anali atagwira ntchito usiku wonse koma osapha nsomba ngakhale imodzi. Popeza Petulo ankaidziwa bwino ntchitoyi, ayenera kuti anayesa njira zosiyanasiyana kuti aphe nsomba. Ayenera kuti anayesetsa kuponya maukonde m’malo onse amene ankaganiza kuti mungapezeke nsomba zambiri. Zikatere, n’kutheka kuti asodzi ankalakalaka atangolowa m’madzimo kuti akasake pamene nsomba zaunjikana kapenanso kupeza njira yozikusira muukondewo. Mwinanso Petulo pa nthawiyi ankaganiza zimenezi. Ngati Petulo anali ndi maganizo amenewa, ndiye kuti anangomuwonjezera nkhawa imene anali nayo. Petulo sankagwira nsomba n’cholinga chongofuna kusangalala, koma ankachita zimenezi n’cholinga choti azipeza ndalama zosamalira banja lake. Komabe, pa nthawiyi anatuluka m’nyanjamo ali chimanjamanja. Ngakhale zinali choncho, iye anafunika kutsukabe makokawo. N’chifukwa chake Yesu anam’peza ali wotanganidwa.

Petulo sanatope kumvetsera ulaliki wa Yesu wonena za Ufumu wa Mulungu ndipo imeneyi ndiye inali mfundo yaikulu ya zimene Yesu ankalalikira

12 Yesu anazunguliridwa ndi chikhamu cha anthu omwe ankamvetsera mwachidwi zimene ankaphunzitsa. Chifukwa cha gulu la anthulo, Yesu analowa m’ngalawa ya Petulo, n’kumuuza kuti aisunthire m’madzi pang’ono. Kenako Yesu anayamba kuphunzitsa anthuwo ndipo aliyense anayamba kumumva bwinobwino. Mofanana ndi anthu ena onse omwe anali kumtunda, Petulo ankamvetsera mwachidwi kwambiri. Iye sanatope kumvetsera ulaliki wa Yesu wonena za Ufumu wa Mulungu ndipo imeneyi ndiye inali mfundo yaikulu ya zimene Yesu ankalalikira. N’kutheka kuti Petulo ankaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kugwira ntchito yolalikira uthenga umenewu limodzi ndi Khristu. Koma kodi akanachita bwino kuyamba ntchito imeneyi? Nanga ndani akanamasamalira banja lake? Mwina Petulo anakumbukiranso kuti anali atagwira ntchito usiku wonse koma sanaphe kanthu.—Luka 5:1-3.

13, 14. Kodi Yesu anachitira Petulo chozizwitsa chotani, nanga Petuloyo anatani?

13 Yesu atamaliza kulankhula, anauza Petulo kuti: “Palasira kwakuya, ndipo muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” Koma Petulo anakayikira kwambiri, ndipo anauza Yesu kuti: “Mlangizi, ife tagwira ntchito usiku wonse koma osapha kanthu. Koma popeza mwanena ndinu, ndiponya maukondewa.” N’zosakayikitsa kuti Petulo sankafuna n’komwe kuponyeranso maukondewo m’madzi, makamaka chifukwa choti pa nthawiyi nsomba sizikhala zikudya. Komabe iye anamvera mawu a Yesu, ndipo n’kutheka kuti anakodola anzake omwe anali m’ngalawa ina kuti amutsatire.—Luka 5:4, 5.

14 Pokoka maukondewo, Petulo anadabwa kumva kuti akulemera. Iye anakoka kwambiri ndipo posakhalitsa anangoona nsomba zambirimbiri zikuphiriphitha mu ukondemo. Mwamsanga, iye anakodola anzake omwe anali m’ngalawa ina aja kuti adzamuthandize. Atabwera, anaona kuti nsombazo sizikwana m’ngalawa imodzi. Iwo anaika nsombazo m’ngalawa zonsezo ndipo ngalawazo zinadzaza kwambiri. Ngalawazo zinayamba kumira chifukwa cha kulemera kwa nsombazo. Petulo anadabwa kwambiri ndi zimenezi. Iye anali ataona Khristu akuchita zozizwitsa kwa anthu ena, koma chozizwitsa chimenechi chinali chapadera, chifukwa chinakhudza kwambiri iyeyo. Mosiyana ndi Petuloyo, Yesu ankatha ngakhale kulamula nsomba kuti zilowe mu ukonde. Zimenezi zinamuchititsa mantha kwambiri Petulo ndipo anagwada n’kuuza Yesu kuti: “Ambuye, chokani pali ine pano, chifukwa ndine munthu wochimwa.” Iye ankaona kuti si woyenera kuyandikana ndi munthu amene ankasonyeza mphamvu za Mulungu m’njira imeneyi.—Werengani Luka 5:6-9.

“Ambuye, . . . ndine munthu wochimwa”

15. Kodi Yesu anathandiza bwanji Petulo kudziwa kuti panalibe chifukwa choti azikayikirira komanso kuchita mantha?

15 Mokoma mtima, Yesu anamuuza kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.” (Luka 5:10, 11) Panalibe chifukwa choti Petulo akayikire kapena kuchita mantha. Petulo sanafunike kuda nkhawa kuti ndani azisamalira banja lake ngati iye atasiya ntchito yake ya usodzi. Ndipo sanafunikenso kuopa kuti anali ndi zofooka ndiponso kuti panali zinthu zimene sangathe kuchita. Iye ankatumikira Mulungu amene ‘amakhululuka ndi mtima wonse.’ (Yes. 55:7) Yesu anali ndi ntchito yaikulu yoti achite, ndipo ntchito imeneyi inali yokhudza tsogolo la anthu onse. Choncho, Yehova akanatha kumupatsa Petulo zinthu zofunika pa moyo wake, kuti azitha kusamalira banja lake kwinaku akugwira ntchito yolalikira.—Mat. 6:33.

16. Kodi Petulo, Yakobo ndi Yohane anatani Yesu atawaitana kuti akhale otsatira ake, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti anasankha bwino?

16 Nthawi yomweyo, Petulo anamvera mawu a Yesu ngati mmene anachitiranso Yakobo ndi Yohane. Baibulo limanena kuti: “Ngalawazo anafika nazo kumtunda, ndipo iwo anasiya chilichonse ndi kumutsatira.” (Luka 5:11) Petulo anakhulupirira Yesu komanso Mulungu. Apatu Petulo anasankha bwino kwambiri. Masiku anonso, Akhristu amene salola mantha ndiponso kukayikira kuwalepheretsa kutumikira Mulungu, amasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro. Ndipotu iwo salakwitsa kuchita zimenezi.—Sal. 22:4, 5.

“N’chifukwa Chiyani Wakayikira?”

17. Kodi Petulo ankakumbukira zinthu ziti zimene anaona Yesu akuchita?

17 Patatha zaka ziwiri kuchokera pamene Petulo anakumana ndi Yesu, usiku wina kunja kuli chimphepo, iye anapalasa ngalawa panyanja ya Galileya monga mmene tafotokozera kumayambiriro kwa nkhani ino. N’zoona kuti sitingadziwe kuti pa nthawiyi iye ankaganiza chiyani. Koma panali zambiri zoti aziganizire. Yesu anali atangochiritsa apongozi aakazi a Petulo ndiponso anali atalalikira ulaliki wake wa paphiri. Komanso, Yesu anali atasonyeza kambirimbiri kuti anali wosankhidwa wa Yehova ndiponso Mesiya, polalikira ndiponso pochita zozizwitsa. Pa nthawiyi, n’kutheka kuti Petulo sankachitanso mantha kwambiri komanso kukayikira ngati mmene ankachitira poyamba. Ndipotu Yesu anali atasankha Petuloyo kuti akhale mmodzi wa atumwi ake 12. Koma zimene tione m’ndime zotsatirazi, zikusonyeza kuti Petulo anali asanasiyiretu kukayikira ndiponso kuchita mantha.

18, 19. (a) Fotokozani zimene Petulo anaona panyanja ya Galileya. (b) Kodi Yesu anatani Petulo atamupempha kuti nayenso ayende panyanja?

18 Usiku umenewu, pa ulonda wachinayi womwe unkayamba 3 koloko m’mawa mpaka nthawi yotuluka dzuwa, Petulo anadzidzimuka ataona chinthu china ndipo anasiya kupalasa ngalawayo n’kukhala tsonga. Chinthucho chimabwera kuchokera kumene kumachokera mafunde. Popeza kunja kunali mwezi, kodi mwina Petulo ankangoona kuwala komwe kunkaonekera pamafundewo? Ayi, chifukwa chinthucho chinkaoneka kuti chaimirira. Anali munthu amene ankayenda pamwamba pa madzipo. Munthuyo atayandikira pafupi, anaoneka kuti akubwera kutsogolo kwenikweni kwa ngalawayo. Choncho, ophunzirawo anachita mantha ndipo anaganiza kuti ndi mzukwa. Koma munthuyo anati: “Limbani mtima, ndine. Musachite mantha.” Munthuyo anali Yesu.—Mat. 14:25-28.

19 Petulo anayankha kuti: “Ambuye, ngati ndinudi, ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” Apa iye anasonyeza kulimba mtima. Pochita chidwi kuti Yesu akuyenda pamadzi, Petulo anafuna kuti nayenso ayende pamadzipo kupita kumene kunali Yesu n’cholinga choti chikhulupiriro chake chilimbe. Choncho mokoma mtima Yesu anamuitana. Petulo anatsika m’ngalawayo n’kuyamba kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. Tangoganizirani mmene Petulo anamvera ataona kuti waima bwinobwino pamwamba pa madziwo. Ayenera kuti anadabwa kwambiri kuona kuti zikuthekadi kuyenda pamadzipo. Koma posapita nthawi, iye anayamba kukayikira ndiponso kuchita mantha.—Werengani Mateyu 14:29.

“Ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha”

20. (a) Kodi Petulo anayamba kuganizira chiyani ndipo zotsatira zake zinali zotani? (b) Pofuna kumuthandiza Petulo kuona kufunika kokhala ndi chikhulupiriro, kodi Yesu anam’funsa funso liti?

20 Maganizo onse a Petulo anayenera kukhala pa Yesu chifukwa Yesuyo, mwa mphamvu ya Yehova, ndi amene anamuthandiza kuyenda panyanjapo. Ndipo Yesu anachita zimenezi chifukwa choti Petulo anasonyeza chikhulupiriro. Komabe, Petulo anayamba kuganizira zinthu zina. Timawerenga kuti: “Ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha.” Iye ayenera anayamba kuganiza kuti amira n’kufera m’nyanjayo. Mantha akewo atakula, chikhulupiriro chake chinayamba kuchepa. Munthu amene anatchedwa Thanthwe uja, anayamba kumira chifukwa chosowa chikhulupiriro. Ngakhale kuti Petulo ankatha kusambira, pa nthawiyi anadziwa kuti kusambira sikungam’pulumutse. Iye anakuwa kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!” Yesu anam’gwira dzanja n’kumuvuula m’madzimo. Kenako, ali pamadzi pomwepo, Yesu anamufunsa funso lomuthandiza kuona kufunika kokhala ndi chikhulupiriro. Iye anati: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”—Mat. 14:30, 31.

21. Kodi kukayikira n’koopsa motani, ndipo tingatani kuti tipewe mtima umenewu?

21 Mawu amene Yesu ananena akuti ‘kukayikira’ anali oyenereradi chifukwa kukayikira kungamusokoneze munthu pa zimene akufuna kupanga. Mtima wokayikira ndi woipa kwambiri chifukwa tikaulekerera ungawononge chikhulupiriro chathu. Choncho, tiyenera kuyesetsa kupewa mtima umenewu. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kuganizira zinthu zoyenera chifukwa kumangoganizira zinthu zimene zikutidetsa nkhawa, kutikhumudwitsa ndiponso zimene zingatilepheretse kuchita bwino utumiki wathu, kungachititse kuti tipitirizebe kukayikira. Koma chikhulupiriro chathu chingalimbe ngati titamaganizira kwambiri zimene Yehova ndi Mwana wake anachita, zimene akuchita panopa komanso zimene adzachitire anthu omvera m’tsogolo.

22. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha Petulo?

22 Petulo akupita ndi Yesu kukakwera ngalawayo, anaona kuti chimphepo chija chatha ndipo panyanja ponsepo pali bata. Petulo ndi ophunzira anzakewo anauza Yesu kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” (Mat. 14:33) Kunja kutayamba kucha, Petulo ayenera kuti anasangalala kwambiri. Iye anaphunzira kuti sayenera kulola mtima wokayikira ndiponso mantha kumulepheretsa kukhulupirira Yehova ndi Yesu. N’zoona kuti Petulo anali asanakhale Mkhristu wolimba ngati thanthwe, mogwirizana ndi zimene Yesu ananena. Komabe, iye nthawi zonse ankayesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chake. Kodi inunso mwatsimikiza mtima kuchita zimenezi? Ndiyetu muyenera kutsanzira chikhulupiriro cha Petulo.