Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 2

“Anayenda Ndi Mulungu Woona”

“Anayenda Ndi Mulungu Woona”

1, 2. Kodi Nowa ndi banja lake ankagwira ntchito iti, nanga ankakumana ndi mavuto otani?

YEREKEZERANI kuti mukuona Nowa atakhala pamtengo waukulu ndipo akupumula. Akudziongola kwinaku akuyang’ana chingalawa chimene akupanga. Pakumveka fungo la phula komanso phokoso la anthu akukhoma chingalawa. Iye akuona ana ake atatanganidwa ndi kucheka matabwa. Tsopano patha zaka zambiri kuchokera pamene ntchitoyi inayamba ndipo mkazi wake, ana ake komanso akazi a ana akewo akhala akugwira ntchitoyi mwakhama. Komabe padakali ntchito yambiri yoti igwiridwe.

2 Anthu a m’dera lawo ankaona Nowa ndi banja lake ngati opusa. Pamene Nowa ndi banja lake ankagwira ntchito yomanga chingalawayi, anthu ankaseka kwambiri zoti kudzabwera chigumula chimene chidzachitike padziko lonse. Ngakhale kuti Nowa ankawachenjeza kuti kudzabwera chigumula, ankaona kuti zimenezo sizingachitike. Iwo ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani Nowa ndi banja lake ankawononga nthawi ndi mphamvu zawo pachabe. Koma Yehova Mulungu sankaona motero.

3. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati Nowa anayenda ndi Mulungu?

3 Mawu a Mulungu amati: “Nowa anayenda ndi Mulungu woona.” (Werengani Genesis 6:9.) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Sizikutanthauza kuti Mulungu ankayendadi ndi Nowa padziko lapansili kapena kuti Nowa anapita kumwamba n’kumakayenda ndi Mulungu. Koma zikutanthauza kuti Nowa ankamvera Mulungu komanso ankamukonda kwambiri moti zinali ngati iye ndi Mulunguyo akuyenda limodzi ngati mabwenzi. Patapita zaka zambiri, Baibulo linanena za Nowa kuti: “Mwa chikhulupiriro [chake], anatsutsa dziko.” (Aheb. 11:7) Kodi Nowa anatsutsa bwanji dziko ndi chikhulupiriro chake? Nanga ifeyo tingaphunzirepo chiyani?

Anali Wokhulupirika Ngakhale Kuti Ankakhala Pakati pa Anthu Oipa

4, 5. M’nthawi ya Nowa, kodi n’chiyani chinachititsa kuti dziko liipireipire?

4 Nowa ankakhala m’dziko lomwe linkaipiraipira. Dzikoli linaipa kuyambira nthawi ya Inoki, yemwe anali abambo awo a agogo ake a Nowa. Inoki anali munthu wolungama ndipo nayenso anayenda ndi Mulungu. Iye analosera za chiweruzo chimene chidzafikire anthu osaopa Mulungu. Koma pomafika m’nthawi ya Nowa dziko linali litaipa kwambiri. Ndipotu Yehova ankaona kuti dziko lawonongeka chifukwa linali litadzaza ndi chiwawa. (Gen. 5:22; 6:11; Yuda 14, 15) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti zinthu ziipe choncho?

5 Angelo ena ndi amene anayambitsa mavutowa. Mngelo wina anali atapandukira kale Yehova n’kukhala Satana Mdyerekezi. Iye ananamizira Mulungu ndipo ananyengerera Adamu ndi Hava kuti nawonso achimwire Mulungu. M’nthawi ya Nowa angelo ena anapandukira ulamuliro wolungama wa Yehova. Iwo anasiya malo awo kumwamba n’kuvala matupi a anthu, ndipo anabwera padziko lapansili n’kutenga akazi okongola kuti akhale akazi awo. Angelo opandukawa ankachititsa kuti anthu azichita makhalidwe oipa.—Gen. 6:1, 2; Yuda 6, 7.

6. Kodi Anefili anachititsa kuti zinthu zikhale bwanji padzikoli, nanga Yehova anaganiza zochita chiyani?

6 Komanso angelo amenewa anabereka ziphona zomwe zinali zamphamvu kwambiri komanso zazitali. Baibulo limatchula ziphona zimenezi kuti Anefili, dzina lomwe limatanthauza “Ogwetsa.” Anefiliwa ankachitira nkhanza anthu ndipo anachititsa kuti anthu akhale achiwawa komanso asamaope Mulungu. N’zosadabwitsa kuti Mlengi ankaona kuti “kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.” Choncho Yehova anaganiza zowononga dziko loipali m’kati mwa zaka 120.—Werengani Genesis 6:3-5.

7. Kodi Nowa ndi mkazi wake anafunika kuteteza ana awo ku mavuto ati amene ankachitika m’nthawi yawo?

7 Taganizani mmene zinalili zovuta kukhala ndi banja labwino pa nthawi imeneyo. Komabe Nowa anayesetsa kukhala ndi banja labwino. Anapeza mkazi wabwino ndipo ali ndi zaka 500 mkazi wakeyo anamuberekera ana aamuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti. * Iye ndi mkazi wake anafunika kuteteza ana awowo kuti asatengere makhalidwe oipa. Ana sachedwa kutengera makhalidwe oipa a anthu amphamvu komanso “otchuka” ndipo Anefili anali anthu otero. Ngakhale kuti palibe chimene Nowa ndi mkazi wake akanachita kuti ana awowa asamamve zinthu zokhudza Anefili, iwo anayesetsa kuwaphunzitsa zoti Yehova Mulungu amadana ndi zoipa. Anathandizanso anawo kuona kuti Yehova amadana ndi chiwawa komanso kupanduka komwe kunali m’dzikolo.—Gen. 6:6.

Nowa ndi mkazi wake anafunika kuteteza ana awo kuti asatengere makhalidwe oipa

8. Kodi makolo angatengere bwanji chitsanzo cha Nowa ndi mkazi wake?

8 Makolo angamvetse mmene zinalili zovuta kwa Nowa ndi mkazi wake kulera ana chifukwa masiku anonso m’dzikoli chiwawa ndi mtima wosamvera zili ponseponse. M’mizinda yambiri mumapezeka magulu a achinyamata olowerera. Ndiponso zosangalatsa zambiri za ana zimalimbikitsa makhalidwe amenewa. Koma makolo anzeru amayesetsa kuphunzitsa ana awo kuti Yehova ndi Mulungu wamtendere ndipo posachedwapa adzawononga dziko loipali. (Sal. 11:5; 37:10, 11) Choncho, n’zotheka kuphunzitsa ana kuti asatengere makhalidwe oipa a m’dzikoli. Nowa ndi mkazi wake anakwanitsa kulera bwino ana awo. Ana awowo anakula ndi makhalidwe abwino ndipo anakwatira akazi amene nawonso ankatumikira Yehova Mulungu.

“Udzipangire Chingalawa”

9, 10. (a) Kodi Yehova analamula Nowa kuchita chiyani? (b) Kodi Yehova anauza Nowa chiyani zokhudza kapangidwe ka chingalawa komanso chifukwa chake anafunika kupanga chingalawacho?

9 Tsiku lina Yehova analankhula ndi Nowa ndipo anamuuza kuti akufuna kuwononga anthu oipa. Analamula Nowa kuti: “Udzipangire chingalawa cha mtengo wa mnjale.”—Gen. 6:14.

10 Anthu ena amanena kuti chingalawa chimenechi chinali sitima yapamadzi koma zimenezi si zoona. Chingalawachi chinkaoneka mosiyana kwambiri ndi mmene sitima zimaonekera chifukwa chinkaoneka ngati chibokosi chachikulu. Yehova anauza Nowa mwatsatanetsatane kukula ndi kapangidwe ka chingalawachi ndipo anamuuza kuti achimate phula mkati ndi kunja komwe. Anamuuzanso chifukwa chake anafunika kupanga chingalawachi. Yehova anati: “Ndidzabweretsa chigumula chamadzi padziko lapansi. . . . Chilichonse cha m’dziko lapansi chidzafa.” Yehova anauzanso Nowa kuti: “Iweyo udzalowe m’chingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.” Nowa anafunikanso kudzalowetsa nyama za mitundu yonse m’chingalawamo. Yehova ananena kuti anthu ndi nyama zimene zidzakhale m’chingalawamo ndi zomwe zidzapulumuke Chigumula.—Gen. 6:17-20.

Nowa ndi banja lake anagwira ntchito mogwirizana kuti akwaniritse zimene Mulungu anawalamula

11, 12. Kodi Nowa anauzidwa kuti agwire ntchito yaikulu iti, nanga anatani atauzidwa zimenezi?

11 Pamenepatu Nowa anali ndi ntchito yaikulu kwabasi. Chingalawachi chinali chachikulu kwambiri. Chinayenera kukhala chachitali mamita 133 m’litali, mamita 22 m’lifupi ndipo kutalika kwake kuyambira pansi mpaka m’mwamba chinayenera kukhala mamita 13. Kodi Nowa anakana ntchitoyi kapena kudandaula kuti ndi yovuta kwambiri mwinanso kuganiza zoisintha mwina ndi mwina kuti isamuvute? Ayi, chifukwa Baibulo limati: “Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.”—Gen. 6:22.

12 Ntchitoyi inatenga zaka zambiri, mwina zaka 40 kapena 50. Iwo anafunika kugwetsa mitengo, kuinyamula komanso kuidula moyenerera n’kuilumikiza. Chingalawachi chinafunika kukhala ndi nyumba zosanjikiza zitatu, zipinda komanso khomo. Chiyeneranso kuti chinali ndi mawindo m’mwamba ndiponso denga lake linali lotsetsereka kuti madzi asamalowe mkati.—Gen. 6:14-16.

13. Kodi Nowa ankagwiranso ntchito ina iti yomwe inali yovuta kuposa kumanga chingalawa, nanga anthu ankatani Nowa akamagwira ntchitoyi?

13 Pamene zaka zinkapita komanso pomwe ntchito yomanga chingalawa inkayenda bwino, Nowa ayenera kuti ankasangalala kuona kuti banja lake likugwira ntchitoyi mwakhama. Koma panalinso ntchito ina yovuta kuposa imeneyi, imene Nowa ndi banja lake ankagwira. Baibulo limanena kuti Nowa anali “mlaliki wa chilungamo.” (Werengani 2 Petulo 2:5.) Choncho iye ankatsogolera pa ntchito yochenjeza anthu oipa za chiwonongeko. Kodi anthuwo anatani atamva chenjezoli? Patapita zaka zambiri, Yesu Khristu ananena kuti anthu pa nthawiyo “ananyalanyaza zimene zinali kuchitika.” Iye ananena kuti anthuwo anali otanganidwa ndi kudya, kumwa komanso kukwatira ndi kukwatiwa, moti sanamvere zimene Nowa ankawauza. (Mat. 24:37-39) N’zosakayikitsa kuti anthu ambiri ankanyoza Nowa ndi banja lake mwinanso kuwaopseza kumene. Iwo ayeneranso kuti ankachita zinthu zofuna kulepheretsa ntchito yomanga chingalawa.

Ngakhale kuti panali umboni wakuti Mulungu ankadalitsa Nowa, anthu anapitirizabe kumunyoza komanso kunyalanyaza uthenga umene ankalengeza

14. Kodi mabanja achikhristu angaphunzire chiyani kwa Nowa ndi banja lake?

14 Komabe Nowa ndi banja lake sanagwe ulesi. Ngakhale kuti anthu ambiri ankangoganizira zofuna zawo moti ankaona ntchito yomanga chingalawa ngati yopanda pake komanso kungotaya nthawi, Nowa anapitirizabe kugwira ntchitoyi mokhulupirika. Mabanja achikhristu angaphunzire zambiri pa chikhulupiriro cha Nowa ndi banja lake. Ndipotu Baibulo limati tili ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Tim. 3:1) Yesu analosera kuti anthu a nthawi yathu ino azidzachita zofanana ndi zimene anthu ankachita pa nthawi yomwe Nowa ankamanga chingalawa. Choncho Akhristufe tikamalalikira uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu, anthu n’kumakana, kutinyoza kapena kutizunza, tizikumbukira Nowa. Ifeyo si oyamba kukumana ndi mavuto oterewa.

“Lowa M’chingalawacho”

15. Kodi ndi achibale ati a Nowa amene anamwalira Nowayo atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 600?

15 Patapita nthawi, chingalawa chija chinayamba kuoneka kuti chikutha. Nowa atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 600, achibale ake ena anamwalira. Lameki, yemwe anali bambo ake a Nowa, anamwalira. * Patangopita zaka zisanu, Metusela, yemwe anali agogo ake a Nowa nayenso anamwalira ali ndi zaka 969. Baibulo limasonyeza kuti Metusela ndi amene anakhala ndi moyo zaka zambiri pa anthu onse. (Gen. 5:27) Metusela ndi Lameki anakhalapo pa nthawi imene Adamu anali ndi moyo.

16, 17. (a) Nowa ali ndi zaka 600, kodi Mulungu anamuuza chiyani? (b) Fotokozani zinthu zosaiwalika zimene Nowa ndi banja lake anaona.

16 Nowa ali ndi zaka 600, Yehova Mulungu anamuuza kuti: “Lowa m’chingalawacho, iwe ndi banja lako.” Anamuuzanso kuti alowetse nyama za mitundu yonse m’chingalawa. Anamuuza kuti pa mtundu uliwonse wa nyama zimene zinkagwiritsidwa ntchito popereka nsembe, alowetse nyama zokwana 7, yamphongo ndi yaikazi yake. Pa nyama zosaperekedwa nsembe anamuuza kuti alowetse ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.—Gen. 7:1-3.

17 Ziyenera kuti zinali zochititsa chidwi kuona nyama zambirimbiri zikulowa m’chingalawa. Panali nyama zoyenda, zokwawa, zouluka komanso zodumpha. Nyamazi zinali zosiyanasiyana, zina zinali zazikulu, zina zazing’ono, zina zofatsa ndipo zina zolusa. Koma sikuti Nowa anavutika kulowetsa nyamazi m’chingalawamo chifukwa Baibulo limati “zinalowa . . . m’chingalawa mmene munali Nowa.”—Gen. 7:9.

18, 19. (a) Kodi tingayankhe bwanji zimene anthu otsutsa Baibulo amanena pa nkhani yoti Nowa analowetsa nyama m’chingalawa? (b) Kodi njira imene Yehova anapulumutsira nyama imasonyeza bwanji nzeru zake?

18 Anthu ena otsutsa Baibulo amanena kuti zimenezi sizingatheke. Iwo amati n’zosatheka kuti nyama zonsezi zikhale mwamtendere m’chingalawa. Koma taganizirani mfundo iyi: Kodi n’zovuta kwa Mlengi yemwe ndi wamphamvu m’chilengedwe chonse kupangitsa nyama zimene analenga kuti zikhale mwamtendere ngati mmene iye akufunira? Kumbukirani kuti pa nthawi ina Yehova Mulungu analekanitsa Nyanja Yofiira komanso anaimitsa dzuwa kuti kusade. Ndiye kodi iye sangathe kuchita zimene zinatchulidwa m’nkhani ya Nowayi? N’zodziwikiratu kuti Yehova angathe kuchita zimenezi ndipo n’zimene anachitadi.

19 N’zoona kuti Mulungu akanatha kusankha njira ina yoti apulumutsire nyamazi. Koma iye anasankha kupulumutsa nyama mwa njira imeneyi n’cholinga chofuna kutikumbutsa ntchito imene iye anapatsa anthu yosamalira nyama. (Gen. 1:28) Makolo ambiri masiku ano amagwiritsa ntchito nkhani ya Nowa kuphunzitsa ana awo kuti Yehova amaona kuti moyo wa nyama ndi wofunika komanso kuti anthu ndi ofunika kwambiri.

20. Kodi mukuganiza kuti Nowa ndi banja lake anatanganidwa bwanji kutatsala masiku 7 kuti Chigumula chichitike?

20 Kenako Yehova anauza Nowa kuti Chigumula chibwera pakatha masiku 7. Banjali liyenera kuti linatanganidwa kwambiri litamva zimenezi. Tangoganizani chintchito chimene chinalipo cholowetsa nyama zonse ndiponso chakudya chake komanso kulowetsa katundu wa banja lonse. Mkazi wa Nowa komanso akazi a Semu, Hamu ndi Yafeti ayenera kuti anatanganidwa kwambiri ndi kukonza mkati mwa chingalawamo kuti mukhale malo abwino.

21, 22. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa ndi zimene anthu a m’nthawi ya Nowa ankachita? (b) Kodi n’chiyani chinachitikira anthu amene ankanyoza Nowa ndi banja lake?

21 Kodi anthu pa nthawiyi ankachita chiyani? Iwo anapitirizabe ‘kunyalanyaza’ ngakhale kuti panali umboni wonse wosonyeza kuti Yehova akudalitsa zimene Nowa ankachita. Anthuwo anaona ndithu nyama zikulowa m’chingalawa koma sanachite chilichonse. Koma zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Anthu masiku ano amanyalanyazanso umboni woonekeratu wosonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Mogwirizana ndi zimene mtumwi Petulo analosera, anthu onyodola amanyoza anthu amene amatsatira chenjezo la Mulungu. (Werengani 2 Petulo 3:3-6.) Koma tikudziwa kuti Nowa ndi anthu a m’banja lake ankanyozedwanso.

22 Kodi anthu onyozawo chinawachitikira n’chiyani? Baibulo limanena kuti Nowa ndi banja lake atalowa m’chingalawa limodzi ndi nyama, “Yehova anatseka chitseko.” Ngati anthu onyozawo anali pafupi, ayenera kuti anadabwa kwambiri ndi zimenezi. Apo ayi, ndiye kuti anadabwa ataona kuti chimvula chayamba kugwa. Chimvulachi chinapitirizabe kugwa mpaka madzi anasefukira padziko lonse mogwirizana ndi mmene Yehova ananenera.—Gen. 7:16-21.

23. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova sanasangalale ndi imfa ya anthu oipa a m’nthawi ya Nowa? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha Nowa?

23 Kodi Yehova anasangalala ndi imfa ya anthu oipawo? Ayi ndithu. (Ezek. 33:11) Iye anawapatsa mwayi woti asiye makhalidwe awo oipa. Koma kodi iwo akanatha kusiya makhalidwe oipa n’kuyamba kusangalatsa Mulungu? Zimene Nowa anachita zimayankha funso limeneli. Nowa anayenda ndi Yehova komanso kumumvera pa zinthu zonse ndipo izi zikusonyeza kuti zinali zotheka kupulumuka. Apa tingati Nowa anatsutsa dziko chifukwa anasonyeza kuti n’zotheka kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Chikhulupiriro chake chinapangitsa kuti iye ndi banja lake apulumuke. Ngati nanunso mutatsanzira chikhulupiriro cha Nowa, zingathandize kuti inuyo ndi banja lanu mudzapulumuke. Mofanana ndi Nowa, nanunso mukhoza kuyenda ndi Yehova Mulungu monga Bwenzi lanu. Ndipotu ubwenzi umenewu ukhoza kukhala mpaka kalekale.

^ ndime 7 Pa nthawi imeneyo anthu ankakhala zaka zambirimbiri kuposa masiku ano. Ziyenera kuti zinali choncho chifukwa panali pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Adamu ndi Hava anakhala opanda ungwiro.

^ ndime 15 Lameki anapatsa mwana wake dzina loti Nowa lomwe limatanthauza “Mpumulo” kapena “Chitonthozo.” Iye analoseranso kuti Nowa adzakwaniritsa tanthauzo la dzina lake pothandiza kuti temberero la nthaka lichotsedwe. (Gen. 5:28, 29) Koma Lameki anamwalira ulosi umenewu usanakwaniritsidwe. N’kutheka kuti mayi ake a Nowa, azichimwene ake komanso azichemwali ake anafa ndi Chigumula.