Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 15

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

1-3. (a) N’chifukwa chiyani Esitere ayenera kuti ankachita mantha pamene ankapita kukaonana ndi mwamuna wake? (b) Kodi tikambirana mafunso ati okhudza Esitere?

ESITERE anayesetsa kudzilimbitsa mtima pamene ankalowa m’bwalo la nyumba ya mfumu ku Susani. Kulowa m’nyumba imeneyi siinali nkhani yamasewera. Nyumbayi inali ndi ziboliboli zamitundu yambirimbiri. Ziboliboli zina zinali zooneka ngati ng’ombe zokhala ndi mapiko ndipo zina ngati anthu oponya mivi ndi uta. Nyumbayi inalinso ndi makoma a njerwa okhala ndi zithunzi za mikango, zipilala za miyala yosema ndiponso ziboliboli zina zochititsa chidwi kwambiri. Kuwonjezera pamenepa, nyumbayi anaimanga pamalo okwera kwambiri pafupi ndi mapiri a Zagros ndipo inayang’ana kumene kunali mtsinje wa Choaspes. Zinthu zonsezi anazipanga ndi cholinga choti aliyense wofika panyumbayi azizindikira kuti wafika pakhomo pa munthu wolemekezeka kwambiri. Esitere ankapita kukaonana ndi munthu ameneyo, yemwe ankadzitcha kuti “mfumu yaikulu.” Mfumu imene Esitere ankapita kukakumana nayoyi inali Ahasiwero, yemwe analinso mwamuna wake.

2 Koma Ahasiwero sanali munthu woti mtsikana aliyense wachiyuda wokhulupirika angalakelake atakhala mwamuna wake. * Sankatsatira chitsanzo chabwino cha anthu ngati Abulahamu, amene modzichepetsa anatsatira malangizo a Mulungu omuuza kuti amvere zimene mkazi wake Sara ankamuuza. (Gen. 21:12) Ahasiwero sankadziwa chilichonse chokhudza Yehova, Mulungu amene Esitere ankamulambira, komanso Chilamulo chake. Iye ankangodziwa malamulo a Aperisiya, kuphatikizapo lamulo loletsa zimene Esitere ankafuna kuchita pa nthawiyi. Kodi Esitere ankafuna kuchita chiyani? Panali lamulo lonena kuti munthu aliyense wopita kukaonekera pamaso pa mfumu ya Perisiya asanaitanidwe ndi mfumuyo, ayenera kuphedwa. Esitere sanaitanidwe, koma pa nthawiyi ankapita kukaonekera kwa mfumuyo. N’kutheka kuti mmene ankayandikira bwalo lamkati lomwe linali pamalo oonekera kwa mfumu, ankangoona kuti basi kwake kwatha.—Werengani Esitere 4:11; 5:1.

3 Kodi n’chifukwa chiyani Esitere anaika moyo wake pachiswe chonchi? Nanga tingaphunzire chiyani pa chikhulupiriro cha mtsikana ameneyu? Choyamba tiyeni tione chimene chinachititsa kuti Esitere akhale mfumukazi ku Perisiya.

Mbiri ya Esitere

4. Kodi tikudziwa zotani zokhudza Esitere, nanga zinatani kuti iye ayambe kukhala ndi Moredekai?

4 Esitere anali mwana wamasiye ndipo Baibulo silinena zambiri za makolo ake omwe anamutchula dzina lachiheberi lakuti Hadasa. Dzinali limatanthauza “mtengo wa mchisu,” womwe umakhala ndi maluwa okongola oyera. Makolo a Esitere atamwalira, wachibale wake wina dzina lake Moredekai anamuchitira chifundo ndipo anamutenga n’kumakhala naye. Esitere anali mlongo wake wa Moredekai (mwana wa m’bale wa bambo ake). Komabe Moredekai anali wamkulu kwambiri poyerekeza ndi Esitere. Moredekai anatenga Esitere n’kumakhala naye kunyumba kwake ndipo ankamusamalira ngati mwana wake weniweni.—Esitere 2:5-7, 15.

Moredekai anali ndi zifukwa zokwanira zosangalalira ndi mwana wakeyu

5, 6. (a) Kodi Moredekai ankamulera bwanji Esitere? (b) Kodi Esitere ndi Moredekai ankakhala moyo wotani ku Susani?

5 Moredekai ndi Esitere anali akapolo ochokera ku Yuda ndipo ankakhala mumzinda wa Susani, womwe unali likulu la Ufumu wa Perisiya. Iwo ayenera kuti ankasalidwa ndi anthu chifukwa cha chipembedzo chawo komanso Chilamulo chimene ankayesetsa kuchitsatira. Mosakayikira, Esitere anayamba kumukonda kwambiri Moredekai pamene ankamuphunzitsa za Yehova, yemwe ndi Mulungu wachifundo amene analanditsa anthu Ake m’mavuto osiyanasiyana, ndipo anali kudzawalanditsanso. (Lev. 26:44, 45) N’zodziwikiratu kuti Esitere ndi Moredekai ankakondana kwambiri komanso ankakhulupirirana.

6 Zikuoneka kuti Moredekai anali ndi udindo winawake m’nyumba ya mfumu ku Susani ndipo nthawi zambiri ankakhala pakhomo la mpanda wa nyumbayo limodzi ndi atumiki ena a mfumu. (Esitere 2:19, 21; 3:3) Sitikudziwa kuti Esitere ankakonda kupanga chiyani ali wamng’ono, komabe zikuoneka kuti ankasamalira bwino Moredekai ndi nyumba yawo. N’kutheka kuti nyumba imeneyi inali tsidya lina la mtsinje, osati mbali imene kunali nyumba yachifumu ija. Iye ayenera kuti ankakonda kupita kumsika wa ku Susani kumene anthu ankagulitsa zinthu zosiyanasiyana zopangidwa ndi golide, siliva ndiponso zinthu zina. Koma pa nthawiyi, Esitere sankadziwa kuti m’tsogolo adzakhala ndi zinthu ngati zimenezi zambirimbiri.

Anali “Wokongola Kwambiri”

7. N’chifukwa chiyani Mfumu Ahasiwero inalamula kuti Vasiti asakhalenso mfumukazi, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

7 Tsiku lina nkhani inali m’kamwam’kamwa mumzinda wa Susani yonena za zomwe zinachitika kunyumba ya mfumu. Mfumu Ahasiwero inakonzera akuluakulu aboma phwando lalikulu la zakudya zapamwamba ndiponso vinyo. Phwandoli lili mkati, mfumuyo inaganiza zoitana mkazi wake wokongola, Vasiti, yemwe ankadyera kwina ndi azimayi anzake. Koma Vasiti anakana kubwera. Chifukwa chokwiya komanso kuchita manyazi ndi zimenezi, mfumuyo inafunsa alangizi ake chilango chimene ingam’patse Vasiti. Malinga ndi zimene alangiziwo ananena, mfumu inalengeza kuti iye sakhalanso mfumukazi ndipo apeza mkazi wina woti alowe m’malo mwake. Anthu ogwira ntchito kunyumba kwa mfumu anayamba kufufuza atsikana okongola m’dziko lonselo kuti pa atsikana amenewo, mfumuyo idzasankhepo mkazi wake.—Esitere 1:1-22; 2:1-4.

8. (a) N’chifukwa chiyani Moredekai ayenera kuti ankadera nkhawa Esitere pamene ankakula? (b) Kodi mukuganiza kuti tingatsatire bwanji mfundo ya m’Baibulo yonena za kukongola? (Onaninso Miyambo 31:30.)

8 Moredekai ayenera kuti ankanyadira komanso kuda nkhawa poona kuti Esitere akukula ndipo tsopano wayamba kuoneka bwino kwambiri. Baibulo limati: “Mtsikanayu anali wooneka bwino ndi wokongola kwambiri.” (Esitere 2:7) Kukongola n’kwabwino komabe munthu wokongola amakhala wosiririka akakhalanso kuti amachita zinthu mwanzeru ndiponso ndi wodzichepetsa. Ngati munthu wokongola alibe makhalidwe amenewa, amakhala wonyada komanso amakhala ndi makhalidwe ena oipa. (Werengani Miyambo 11:22.) Tikukhulupirira kuti inunso mukuvomereza kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Ndiye popeza Esitere anali wokongola, kodi kukongolako kunamuthandiza kapena kunamupangitsa kuti akhale munthu wonyada? Yankho la funso limeneli linadziwika patapita nthawi.

9. (a) Kodi chinachitika n’chiyani atumiki a mfumu ataona kuti Esitere ali m’gulu la atsikana okongola, ndipo n’chifukwa chiyani zinali zovuta kuti Esitere asiyane ndi Moredekai? (b) N’chifukwa chiyani Moredekai analola kuti Esitere akwatiwe ndi munthu wosakhulupirira? (Onaninso bokosi.)

9 Atumiki a mfumu aja anaona kuti Esitere anali m’gulu la atsikana okongola ndipo anamutenga kuchoka m’manja mwa Moredekai kupita kunyumba ya mfumu. (Esitere 2:8) Ziyenera kuti zinali zovuta kwambiri pamene Esitere ankasiyana ndi Moredekai popeza iwo ankakondana kwambiri ndipo ankangokhala ngati mwana ndi bambo ake. Moredekai ayenera kuti sankafuna kuti mwana wakeyu adzakwatiwe ndi munthu wosalambira Yehova, ngakhale munthuyo atakhala mfumu. Koma pamene zinthu zinafikapa sakanatha kuletsa. * Esitere ayenera kuti asanatengedwe anamvetsera mwatcheru malangizo onse amene Moredekai anamupatsa. Mmene ankapita kunyumba yachifumu ku Susani, ayenera kuti anali ndi mafunso ambirimbiri mumtima mwake chifukwa sankadziwa kuti zikamuthera bwanji.

Ankakondedwa “Ndi Aliyense Womuona”

10, 11. (a) Kodi malo amene Esitere ankakhala akanamupangitsa kukhala wotani? (b) Kodi Moredekai anasonyeza bwanji kuti ankadera nkhawa Esitere?

10 Esitere anayamba kukhala kunyumba yosiyana kwambiri ndi kwawo ndipo zonse kumeneko zinali zachilendo zokhazokha. Iye ankakhala ndi “atsikana ambiri” amene anatengedwa kuchokera kumbali zonse za Ufumu wa Perisiya. N’zoonekeratu kuti atsikana amenewa anali osiyana kwambiri zikhalidwe, zilankhulo komanso mmene ankaonera zinthu. Atsikana amenewa ankayang’aniridwa ndi munthu wina, dzina lake Hegai. Kwa chaka chathunthu iwo ankapakidwa mafuta onunkhira komanso ankawakongoletsa m’njira zosiyanasiyana. (Esitere 2:8, 12) Moyo ngati umenewu ukanatha kusokoneza atsikanawo mosavuta. Maganizo awo onse akanakhala pa kudzikongoletsa ndipo zikanachititsa kuti ayambe kunyada komanso kukhala ndi mtima wampikisano. Kodi moyo woterewu unamukhudza bwanji Esitere?

11 Moredekai ankamudera nkhawa kwambiri Esitere. Baibulo limanena kuti tsiku lililonse ankafika kumalo kumene Esitere ankakhala, n’cholinga chakuti adziwe mmene alili. (Esitere 2:11) Akamva zokhudza Esitere, mwina kuchokera kwa anthu amene ankagwira ntchito pamalopa, mosakayikira iye ankasangalala kwambiri ndipo ankanyadira. N’chifukwa chiyani tikutero?

12, 13. (a) Kodi Esitere anali ndi mbiri yotani kwa anthu amene ankakhala naye? (b) N’chifukwa chiyani Moredekai anasangalala kudziwa kuti Esitere sanaulule zoti anali Myuda?

12 Hegai anasangalala kwambiri ndi Esitere moti ankamukomera mtima pa zinthu zambiri. Iye anapatsa Esitere atsikana 7 oti azimutumikira ndiponso anamupatsa malo abwino kwambiri m’nyumba ya akaziyo. Nkhaniyi imanenanso kuti: “Pa nthawi imeneyi Esitere anali kukondedwa ndi aliyense womuona.” (Esitere 2:9, 15) Kodi anthu ankamukonda chonchi Esitere chifukwa chakuti anali wokongola basi? Ayi, panali zinthu zina zimene zinachititsa kuti azikondedwa.

Esitere ankadziwa kuti munthu wokongola amakhala wosiririka akakhalanso kuti amachita zinthu mwanzeru ndiponso ndi wodzichepetsa

13 Mwachitsanzo, Baibulo limati: “Esitere sananene za mtundu wa anthu ake kapena za abale ake, pakuti Moredekai anali atamulamula kuti asanene kalikonse.” (Esitere 2:10) Moredekai anali atalangiza Esitere kuti asaulule zoti anali Myuda. Mosakayikira, iye anachita zimenezi chifukwa chodziwa kuti anthu a m’banja lachifumu ambiri sankasangalala ndi Ayuda. Moredekai ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona kuti ngakhale kuti Esitere ankakhala kwina, anapitirizabe kumumvera komanso kuchita zinthu mwanzeru.

14. Kodi masiku ano achinyamata angatsanzire bwanji Esitere?

14 Nawonso achinyamata a masiku ano akhoza kusangalatsa makolo awo kapenanso anthu amene akuwalera. Akakhala ndi achinyamata anzawo, angakane kuchita zinthu zoipa n’kupitirizabe kuchita zinthu zogwirizana ndi mfundo zimene akuona kuti n’zolondola. Iwo angachite zimenezi ngakhale pamene ali ndi anthu osaganiza bwino, akhalidwe loipa kapenanso aukali. Akamachita zimenezi, mofanana ndi Esitere, amasangalatsa mtima wa Atate wawo wakumwamba.—Werengani Miyambo 27:11.

15, 16. (a) Kodi Esitere anatani kuti akope mtima wa mfumu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Esitere ayenera kuti anavutika kuti azolowere moyo watsopano?

15 Ndiyeno nthawi itakwana yoti Esitere akaonekere kwa mfumu, anapatsidwa ufulu woti anene chilichonse chimene akufuna kuti am’patse, mwina kuti awonjezere kudzikongoletsa. Modzichepetsa, iye sanapemphe chilichonse chowonjezera pa zimene Hegai anatchula. (Esitere 2:15) Ayenera kuti anadziwa kuti kukongola pakokha sikungachititse kuti mfumuyo imusankhe. Ankadziwa kuti chofunika kwambiri n’kukhala wodzichepetsa. Koma kodi zimenezi zinathandizadi?

16 Nkhaniyi imati: “Mfumu inakonda kwambiri Esitere kuposa akazi ena onse, moti mfumu inakondwera naye ndipo inamusonyeza kukoma mtima kosatha kuposa anamwali ena onse. Pamenepo mfumu inamuveka duku lachifumu kumutu kwake ndi kumusandutsa mfumukazi m’malo mwa Vasiti.” (Esitere 2:17) Esitere anakhala mfumukazi yatsopano ndipo anali mkazi wa mfumu yamphamvu kwambiri padziko lonse pa nthawiyo. Iye ayenera kuti anavutika kuti azolowere moyo watsopanowu. Koma kodi udindo umenewu unamusokoneza maganizo n’kumupangitsa kuti ayambe kunyada? Ayi.

17. (a) Kodi Esitere anapitirizabe kumvera Moredekai m’njira ziti? (b) N’chifukwa chiyani chitsanzo cha Esitere n’chofunika kwambiri masiku ano?

17 Esitere anapitirizabe kumvera Moredekai, yemwe anamulera ngati bambo ake. Iye sanaulule zoti anali Myuda. Komanso pamene Moredekai anatulukira chiwembu chimene anthu anakonza choti aphe Ahasiwero, Esitere anamvera zimene Moredekai anamuuza ndipo anachenjeza mfumu za nkhaniyi. Izi zinachititsa kuti chiwembucho chilephereke. (Esitere 2:20-23) Iye anapitirizabe kukhala wodzichepetsa ndiponso womvera ndipo zimenezi zinasonyeza kuti ankakhulupirira Mulungu wake. Masiku ano anthu ambiri saona kuti kumvera n’kofunika chifukwa amaona kuti palibe vuto ndi kusamvera kapena kuchita zinthu mosatsatira malamulo. Koma anthu amene amakhulupiriradi Mulungu amaona kuti kumvera ndi khalidwe lamtengo wapatali ngati mmene Esitere ankaonera.

Chikhulupiriro cha Esitere Chinayesedwa

18. (a) N’chifukwa chiyani Moredekai ankakana kugwadira Hamani? (Onaninso mawu a m’munsi.) (b) Masiku ano kodi amuna ndi akazi okhulupirika amachita chiyani potsanzira Moredekai?

18 Mfumu inakweza pa udindo munthu wina, dzina lake Hamani, kuti akhale nduna yake yaikulu. Zimenezi zinachititsa kuti Hamani akhale mlangizi wake wamkulu ndiponso wachiwiri kwa mfumuyo. Komanso mfumu inalamula kuti aliyense akaona Hamani azimuweramira. (Esitere 3:1-4) Zinali zovuta kwa Moredekai kuti atsatire lamulo limeneli. Iye ankadziwa kuti ayenera kumvera mfumu koma osati pa zinthu zomwe zingakwiyitse Mulungu. Hamani anali “Mwagagi.” Zimenezi zikutanthauza kuti anali mbadwa ya Agagi, mfumu ya Aamaleki, yomwe inaphedwa ndi mneneri Samueli. (1 Sam. 15:33) Aamaleki anali anthu oipa kwambiri moti anadzipanga okha kukhala adani a Yehova ndi Aisiraeli. Mulungu sankasangalala ndi mtundu wa Aamaleki. * (Deut. 25:19) Ndiye kodi Myuda wokhulupirika akanagwadira bwanji Mwamaleki? Moredekai ankaona kuti kuchita zimenezi n’kosayenera moti sankagwadira Hamani. Masiku anonso, amuna ndi akazi okhulupirika amalolera kuika moyo wawo pachiswe potsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Mac. 5:29.

19. Kodi Hamani anakonza chiwembu chotani ndipo anatani kuti anyengerere mfumu?

19 Hamani ataona kuti Moredekai akukana kumugwadira anakwiya koopsa. Koma ankaona kuti kupha Moredekai yekha sikunali kokwanira. Iye ankafuna kufafaniza anthu onse a mtundu wa Moredekai. Hamani anauza mfumu zinthu zoipa zokhudza Ayuda n’cholinga chakuti mfumuyo iziwaona ngati anthu oipa. Iye sanawatchule dzina koma anangonena kuti ndi mtundu wa anthu osafunika “umene ukupezeka paliponse ndipo ukudzipatula pakati pa anthu.” Iye ananenanso kuti anthu amenewa samvera malamulo a mfumu ndipo ndi adani oopsa. Hamani analonjeza kuti apereka ndalama zambiri zoti zigwiritsidwe ntchito polipirira zonse zofunika kuti Ayuda onse amene anali mu ufumuwo aphedwe. * Ahasiwero anapatsa Hamani mphete yake yodindira kuti adinde lamulo lililonse lokhudza nkhaniyi limene akufuna kukhazikitsa.—Esitere 3:5-10.

20, 21. (a) Kodi Ayuda onse a mu Ufumu wa Perisiya kuphatikizapo Moredekai anatani atamva uthenga wa Hamani? (b) Kodi Moredekai anapempha Esitere kuti achite chiyani?

20 Pasanapite nthawi anatumiza anthu okwera pamahatchi kumadera onse a ufumuwo kuti akapereke uthenga woti Ayuda onse aphedwa. Taganizirani mmene Ayuda amene anali ku Yerusalemu anamvera atamva uthenga umenewu. Iwo anali atabwerera ku ukapolo ku Babulo ndipo ankayesetsa kumanganso mzinda wa Yerusalemu ndipo pa nthawiyi unali wosatetezeka chifukwa unalibe mpanda. N’kutheka kuti Moredekai atamva nkhani yomvetsa chisoniyi anaganizira za anthu amenewa, anzake komanso abale ake amene ankakhala ku Susani. Chifukwa chothedwa nzeru, Moredekai anang’amba zovala zake, kuvala chiguduli, n’kudzola phulusa ndipo anayamba kulira mofuula pakati pa mzindawo. Koma pa nthawiyi n’kuti Hamani ali phee ndi mfumu ku Susani, akungomwa vinyo. Zoti Ayuda ndiponso anzawo ena ali pa chisoni kwambiri chifukwa cha uthenga umene iyeyo anatumiza, sizinkamukhudza n’komwe.—Werengani Esitere 3:12–15; 4:1.

21 Moredekai anaona kuti ayenera kuchitapo kanthu. Koma kodi akanatani pamenepa? Moredekai anali ndi chisoni kwambiri moti Esitere atamutumizira zovala, anakana zovalazo komanso kutonthozedwa. N’kutheka kuti kwa nthawi yaitali Moredekai ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani Yehova Mulungu analola kuti mwana wake Esitere akhale mkazi wa mfumu yosalambira Yehova. Koma tsopano chifukwa chimene Mulungu analolera kuti zimenezi zichitike chinayamba kuoneka. Moredekai anatumiza uthenga kwa Mfumukazi Esitere, womupempha kuti akachonderere mfumu kuti isinthe maganizo. Pamenepatu Esitere anafunika kulimba mtima kuti achite zimenezi poteteza “anthu a mtundu wake.”—Esitere 4:4-8.

22. N’chifukwa chiyani Esitere ankachita mantha kukaonekera kwa mfumu yomwe inalinso mwamuna wake? (Onaninso mawu a m’munsi.)

22 Esitere ayenera kuti anachita mantha kwambiri atamva uthengawo. Pamenepa chikhulupiriro chake chinayesedwa kwambiri. Zimene Esitere anayankha Moredekai zinasonyeza kuti anali ndi mantha kwambiri. Iye anakumbutsa Moredekai za lamulo loletsa kukaonekera kwa mfumu usanaitanidwe lija. Munthu akaphwanya lamulo limeneli ankatha kuphedwa. Ankapulumuka pokhapokha ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yake yagolide. Ndipo akaganizira zimene zinachitikira Vasiti atakana kukaonekera kwa mfumuyo, Esitere ankaona kuti ngakhale kuti ndi mkazi wa mfumu, n’kutheka kuti mfumuyi singamuchitire chifundo. Esitere anauza Moredekai kuti panali patatha masiku 30 asanaitanidwe kuti akaonekere kwa mfumu. Zimenezi ziyenera kuti zinachititsa Esitere kuyamba kukayikira ngati mfumuyi, yomwe sinkachedwa kupsa mtima, inkamukondabe. *Esitere 4:9-11.

23. (a) Kodi Moredekai ananena chiyani pofuna kulimbikitsa chikhulupiriro cha Esitere? (b) Kodi Moredekai ndi chitsanzo chabwino chifukwa chiyani?

23 Moredekai anayankhanso Esitere ndi mawu amphamvu kuti chikhulupiriro chake chilimbe. Anamutsimikizira kuti ngati sangachitepo kanthu, chipulumutso cha Ayuda chichokera kwina. Koma kodi Esitere akanapulumuka ngati lamulo loti Ayuda aphedwe likanayamba kugwira ntchito? Apa Moredekai anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova, yemwe sangalole kuti anthu ake onse awonongedwe kapena kulola kuti malonjezo ake asakwaniritsidwe. (Yos. 23:14) Kenako Moredekai anafunsa Esitere kuti: “Ndani akudziwa? Mwina iwe wakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.” (Esitere 4:12-14) Moredekai ankakhulupirira Yehova Mulungu ndi mtima wonse. Kodi ifenso timatero?—Miy. 3:5, 6.

Anali ndi Chikhulupiriro Cholimba Moti Sanaope Kufa

24. Kodi Esitere anachita chiyani posonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro komanso anali wolimba mtima?

24 Apa Esitere anafunika kusankha zochita mwamsanga. Iye anatumiza uthenga kwa Moredekai womudziwitsa kuti iyeyo asala kudya kwa masiku atatu ndipo anapemphanso Moredekaiyo ndi Ayuda ena kuti nawonso asale kudya pa nthawiyo. Uthengawu unalinso ndi mawu osonyeza chikhulupiriro komanso kulimba mtima, amene anthu ambiri akhala akuwanena kwa zaka zambiri. Mawu ake ndi akuti: “Ngati n’kufa, ndife.” (Esitere 4:15-17) Pa masiku atatu amenewa Esitere ayenera kuti ankapemphera mochokera pansi pa mtima kuposa mmene ankachitira masiku ena onse. Ndiyeno tsiku loti akaonane ndi mfumu litakwana, iye anavala zovala zachifumu zokongola kwambiri kuti akaoneke bwino pamaso pa mfumuyo.

Esitere anaika moyo wake pachiswe n’cholinga choti ateteze anthu a Mulungu

25. Fotokozani zimene zinachitika pamene Esitere ankakaonekera kwa mwamuna wake.

25 Monga tafotokozera kumayambiriro kwa nkhaniyi, Esitere ananyamuka ulendo wopita kunyumba ya mfumu. N’zachidziwikire kuti anali ndi nkhawa komanso ankapemphera chamumtima. Iye anafika pabwalo la nyumba ya mfumu ndipo anamuona Ahasiwero atakhala pampando wake wachifumu. N’kutheka kuti ankayang’anitsitsa nkhope ya Ahasiwero, yemwe anali watsitsi lanzindo ndiponso ankadulira mwaluso kwambiri ndevu zake. Esitere ayenera kuti ankafuna kuona ngati mfumuyo yakwiya kapena ayi. Ngati panapita nthawi mfumuyo isanamuone, ndiye kuti mtima wake unali phaphapha posadziwa kuti zimuthera bwanji. Koma kenako mfumuyo inamuona. Mfumuyo iyenera kuti inadabwa kwambiri itamuona. Komabe nkhope yake inayamba kuoneka kuti sanakwiye ndi kubwera kwa Esitere ndipo inamuloza ndi ndodo yake yagolide.—Esitere 5:1, 2.

26. N’chifukwa chiyani Akhristu oona ayenera kukhala olimba mtima ngati Esitere, nanga ndi zinthu zinanso ziti zimene Esitere anafunika kuchita?

26 Ahasiwero anamvetsera zimene Esitere ankafuna kumuuza. Pamenepa Esitere anasonyeza kulimba mtima ndipo anasonyezanso kuti ali kumbali ya Mulungu komanso anthu a mtundu wake. Zimene anachitazi zinasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo Esitere ndi chitsanzo chabwino kwa atumiki onse a Mulungu mpaka pano. Akhristu oona masiku ano amalimbikitsidwa ndi zitsanzo ngati zimenezi. Yesu ananena kuti otsatira ake adzadziwika ndi chikondi chololera kuvutikira ena. (Werengani Yohane 13:34, 35.) Kuti munthu asonyeze chikondi chimenechi amafunika kukhala wolimba mtima ngati mmene Esitere analili. Komabe zimene Esitere anachita pa tsikuli pofuna kuthandiza anthu a Mulungu, chinali chiyambi chabe. Kodi iye akanatani kuti apangitse mfumu kukhulupirira kuti Hamani, mlangizi wake yemwe ankamukonda zedi, anali woipa kwambiri ndipo anali atakonza chiwembu? Kodi iye akanachita chiyani kuti apulumutse anthu a mtundu wake? Tikambirana mafunso amenewa m’mutu wotsatira.

^ ndime 2 Anthu ambiri amakhulupirira kuti Ahasiwero anali Sasita Woyamba, amene analamulira Ufumu wa Perisiya kumayambiriro kwa zaka za m’ma 400 B.C.E.

^ ndime 9 Onani bokosi lakuti “Mafunso Okhudza Esitere,” m’Mutu 16.

^ ndime 18 Hamani ayenera kuti anali m’gulu la Aamaleki ochepa kwambiri omwe analipobe pa nthawiyi, chifukwa anthu “otsala” a mtundu umenewu anali ataphedwa kale m’nthawi ya Mfumu Hezekiya.—1 Mbiri 4:43.

^ ndime 19 Hamani analonjeza kupereka matalente 10,000 asiliva ndipo masiku ano ndalama zimenezi ndi zokwana madola mamiliyoni ambiri. Ngati Ahasiwero analidi Sasita Woyamba, ndiye kuti anakopeka kwambiri ndi ndalama zimene Hamani analonjezazi. Sasita ankafunikira ndalama zambiri zoti agwiritse ntchito pa nkhondo yomenyana ndi Agiriki, yomwe pamapeto pake analuza.

^ ndime 22 Sasita Woyamba ankadziwika kuti anali munthu wosachedwa kupsa mtima. Mwachitsanzo, katswiri wina wa ku Greece wolemba mbiri yakale, dzina lake Herodotus, analemba zinthu zina zimene Sasita anachita pamene ankamenyana ndi Agiriki. Mfumuyi inalamula kuti panyanja ya Hellespont pamangidwe mlatho pogundaniza mabwato. Mphepo yamkuntho itaphwasula mlathowo, Sasita analamula kuti anthu amene anamanga mlathowo adulidwe mitu. Analamulanso asilikali ake kuti alange nyanjayo mwa kukwapula madzi kwinaku akuwerenga mokweza mawu olalata. Pa nkhondo yomweyi, munthu wina wolemera atapempha kuti mwana wake asalowe usilikali, Sasita analamula kuti mwanayo adulidwe pakati ndipo mtembo wake uikidwe poonekera kuti anthu ena atengerepo phunziro.