Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 18

Ubatizo Umatithandiza kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Mulungu

Ubatizo Umatithandiza kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Mulungu
  • Kodi ubatizo wachikhristu umachitika bwanji?

  • Kodi mufunika kuchita chiyani kuti muyenerere kubatizidwa?

  • Kodi munthu amadzipereka bwanji kwa Mulungu?

  • Kodi chifukwa chachikulu chobatizidwira n’chiyani?

1. N’chifukwa chiyani nduna ya ku Itiyopiya inapempha kuti ibatizidwe?

“TAONANI! Si awa madzi ambiri. Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?” Funso limeneli linafunsidwa ndi nduna ya ku Itiyopiya m’nthawi ya atumwi. Mkhristu wina dzina lake Filipo anali atafotokozera ndunayo umboni wosonyeza kuti Yesu anali Mesiya amene Mulungu ananeneratu kuti adzabwera. Mfundo za m’Malemba zimene anaphunzira zitamufika pa mtima anaona kuti sakufunika kungokhala, koma ndi bwino kuti abatizidwe.—Machitidwe 8:26-36.

2. Kodi n’chiyani chingakulimbikitseni kuti muyambe kuganizira zoti mubatizidwe?

2 Ngati mwaphunzira bwinobwino mitu yoyambirira ya bukuli ndi munthu wina wa Mboni za Yehova, mwina nanunso mukhoza kufunsa kuti, ‘Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?’ Panopa mwaphunzira kale zoti Baibulo limalonjeza kuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. (Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4) Mwaphunziranso zimene zimachitika munthu akamwalira ndiponso zoti anthu amene anamwalira adzauka. (Mlaliki 9:5; Yohane 5:28, 29) N’kuthekanso kuti mumasonkhana ndi Mboni za Yehova ndipo mwaona umboni wosonyeza kuti chimenechi ndi chipembedzo choona. (Yohane 13:35) Mwinanso mwayamba kale kuchita zinthu zimene zingathandize kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu ndipo zimenezi n’zofunika kwambiri.

3. (a) Kodi Yesu analamula otsatira ake kuti azichita chiyani? (b) Kodi ubatizo umachitika bwanji?

3 Kodi mungasonyeze bwanji kuti mukufuna kuti muzitumikira Mulungu? Yesu anauza otsatira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. [Ndipo] muziwabatiza.” (Mateyu 28:19) Yesu mwiniwakeyo anapereka chitsanzo pamene anabatizidwa m’madzi. Kubatizidwa kwake sikunali kongomuwaza madzi, kapena kungomuthira madzi pamutu. (Mateyu 3:16) Mawu akuti “kubatiza” achokera ku mawu achigiriki amene amatanthauza kuti “kuviika m’madzi.” Choncho, ubatizo wachikhristu umatanthauza kuviika, kapena kuti kumiza munthu yense m’madzi.

4. Kodi ubatizo umasonyeza chiyani?

4 Anthu onse amene akufuna kukhala pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu ayenera kubatizidwa m’madzi. Kubatizidwa kumakhala kusonyeza anthu onse kuti mukufuna muzitumikira Mulungu. Kumasonyeza kuti kuchita chifuniro cha Yehova kumakusangalatsani. (Salimo 40:7, 8) Komabe, pali zinthu zingapo zofunikira zimene muyenera kuchita kuti muyenerere kubatizidwa.

TIYENERA KUDZIWA ZINTHU MOLONDOLA NDIPONSO KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO

5. (a) Kodi chinthu choyamba chimene munthu amafunikira kuchita kuti ayenerere kubatizidwa n’chiyani? (b) Kodi misonkhano yachikhristu ndi yofunika bwanji?

5 Panopo munayamba kale kuchita chinthu choyamba. Chinthu chake ndi kudziwa Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, komwe kwatheka chifukwa chophunzira Baibulo mwakhama. (Werengani Yohane 17:3.) Komabe padakali zambiri zoti muphunzire. Akhristu amayenera kuti ‘azidziwa molondola chifuniro cha Mulungu.’ (Akolose 1:9) Chinthu chimene chingakuthandizeni kuchita zimenezi ndi kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova. Misonkhano imeneyi ndi yofunika kwambiri. (Aheberi 10:24, 25) Kupezeka pa misonkhano imeneyi nthawi zonse kungakuthandizeni kuti mumudziwe Mulungu molondola.

Kudziwa molondola Mawu a Mulungu ndi chinthu chofunikira kuti munthu ayenerere kubatizidwa

6. Kodi muyenera kudziwa mfundo za m’Baibulo zochuluka bwanji kuti muyenerere kubatizidwa?

6 Si kuti mukufunikira kudziwa zonse zimene Baibulo limanena kuti muyenerere kubatizidwa. Nduna ya ku Itiyopiya ija inkadziwa kale zinthu zina, komabe inkafunika kuthandizidwa kumvetsa mfundo zina za m’Malemba. (Machitidwe 8:30, 31) Nanunso mudakali ndi zinthu zina zoti muphunzire. Ndipotu kuphunzira za Mulungu sikudzatha. (Mlaliki 3:11) Komabe, musanabatizidwe muyenera kudziwa ndiponso kukhulupirira mfundo zoyambirira za m’Baibulo. (Aheberi 5:12) Mfundo zimenezi zikuphatikizapo kudziwa zimene zimachitika munthu akamwalira ndiponso kufunika kwa dzina la Mulungu ndi Ufumu wake.

7. Kodi kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni bwanji?

7 Komabe kungodziwa zinthu si kokwanira, chifukwa “popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Baibulo limatiuza kuti anthu ena a mumzinda wa Korinto atamva uthenga umene Akhristu ankalalikira, “anayamba kukhulupirira ndi kubatizidwa.” (Machitidwe 18:8) Nanunso mukamaphunzira Baibulo muyenera kukhulupirira kuti ndi Mawu a Mulungu. Zimene mukuphunzira m’Baibulo ziyenera kukuthandizani kukhulupirira kuti zomwe Mulungu analonjeza zidzachitikadi ndiponso kuti nsembe ya Yesu ingakupulumutseni.—Yoswa 23:14; Machitidwe 4:12; 2 Timoteyo 3:16, 17.

KUUZA ENA ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA

8. Kodi n’chiyani chingakuchititseni kuti muziuza ena zimene mwaphunzira?

8 Chikhulupiriro chanu chikamakula, mudzaona kuti n’zosatheka kungokhala osauza ena zimene mwaphunzira. (Yeremiya 20:9) Mudzafunitsitsa kuuza ena za Mulungu ndiponso zolinga zake.—Werengani 2 Akorinto 4:13.

Chikhulupiriro chidzakuthandizani kuti muziuza ena zimene mumakhulupirira

9, 10. (a) Kodi mungayambire kuuza ndani zimene mumaphunzira m’Baibulo? (b) Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukufuna kuyamba kumalalikira limodzi ndi Mboni za Yehova?

9 Mungayambe ndi kufotokoza mosamala mfundo za m’Baibulo kwa abale anu, anzanu ndiponso anthu amene mumagwira nawo ntchito. M’kupita kwa nthawi, mungafune kuti muyambe kumalalikira limodzi ndi Mboni za Yehova. Nthawi imeneyi ikafika, mukhoza kufotokoza cholinga chanucho kwa munthu wa Mboni amene amakuphunzitsani Baibulo. Ngati zikuoneka kuti mukhoza kuyamba kulalikira limodzi ndi Mboni za Yehova, padzakonzedwa zoti akulu awiri acheze nanu limodzi ndi amene mumaphunzira nayeyo.

10 Zimenezi zingathandize kuti mudziwane bwino ndi akulu, omwe amasamalira nkhosa za Mulungu. (Machitidwe 20:28; 1 Petulo 5:2, 3) Akuluwa akaona kuti mukumvetsa ndiponso kukhulupirira mfundo zoyambirira za m’Baibulo, mukutsatira mfundo za m’Baibulo komanso kuti mukufunitsitsa kukhala wa Mboni za Yehova, adzakuuzani kuti mukhoza kuyamba kumalalikira uthenga wabwino limodzi ndi mpingo monga wofalitsa wosabatizidwa.

11. Kodi ena angafunike kusintha zinthu ngati ziti kuti ayambe kulalikira limodzi ndi mpingo?

11 Komabe, nthawi zina akuluwo angaone kuti mudakali ndi makhalidwe enaake amene mukufunika kusintha musanayambe kulalikira limodzi ndi mpingo. Zimenezi zikuphatikizapo kusiya makhalidwe amene mumachita kumbali, omwe anthu ena sawadziwa. Choncho, musanapemphe zoti mukufuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa, muyenera kusiya machimo akuluakulu amene munkachita, monga chiwerewere, kuledzera ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.—Werengani 1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21.

TIYENERA KULAPA NDI KUTEMBENUKA

12. Kodi kulapa n’kofunika chifukwa chiyani?

12 Komabe pali zinanso zimene munthu ayenera kuchita kuti ayenerere kubatizidwa. Mtumwi Petulo ananena kuti: “Lapani ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe.” (Machitidwe 3:19) Kulapa kumatanthauza kumva chisoni ndi zimene wachita. Kulapa ndi kofunikira kwambiri kwa anthu amene anali ndi makhalidwe oipa, komabe nawonso anthu amene sankachita zoipa amafunika kulapa. Zili choncho chifukwa anthu onse ndi ochimwa ndipo amafunikira kuti Mulungu aziwakhululukira. (Aroma 3:23; 5:12) Musanaphunzire Baibulo, simunkadziwa zimene Mulungu amafuna moti zinali zosatheka kukhala ndi makhalidwe amene iyeyo amasangalala nawo. N’chifukwa chake kulapa kuli kofunika.

13. Kodi kutembenuka kumatanthauza chiyani?

13 Munthu akalapa amafunikanso “kutembenuka,” kapena kuti kusiya khalidwe loipa limene anali nalo. Kungodzimvera chisoni sikokwanira. Muyenera kusiya khalidwe lanu lakale ndiponso kutsimikiza kuti kuyambira panopa muzichita zinthu zoyenera. Kulapa ndiponso kutembenuka ndi zinthu zimene muyenera kuchita musanabatizidwe.

KUDZIPEREKA

14. Kodi chinanso choyenera kuchita musanabatizidwe n’chiyani?

14 Pali chinthu chinanso chofunika kuchita musanabatizidwe. Muyenera kudzipereka kwa Yehova Mulungu.

Kodi munadzipereka kwa Mulungu m’pemphero?

15, 16. Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza chiyani, nanga n’chiyani chingam’pangitse munthu kuchita zimenezi?

15 Munthu amadzipereka kudzera m’pemphero lochokera pansi pa mtima ndipo amamulonjeza Yehova Mulungu kuti adzamumvera ndi kumutumikira mpaka kalekale. (Deuteronomo 6:15) Koma kodi n’chiyani chimene chingam’pangitse munthu kudzipereka mwa njira imeneyi? Kuti tipeze yankho, tiyerekeze kuti mnyamata waona mtsikana winawake amene akumufuna. Pamene akudziwa za makhalidwe abwino amene mtsikanayo ali nawo, m’pamenenso amakopeka naye kwambiri. Sitingakayikire kuti m’kupita kwa nthawi angamufunsire. Ndi zoona kuti kukwatira kumapangitsa munthu kukhala ndi udindo waukulu. Koma chikondi chingam’pangitse mnyamatayo kuti amukwatirebe mtsikanayo.

16 Mukamudziwa Yehova komanso kuyamba kumukonda, sipakhala chilichonse chokulepheretsani kuti muzimutumikira ndiponso kumulambira. Aliyense amene amafuna kutsatira Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, ayenera ‘kudzikana yekha.’ (Maliko 8:34) Tingasonyeze kuti tikudzikana tikamaonetsetsa kuti zofuna zathu sizikutilepheretsa kumvera Mulungu. Choncho, musanabatizidwe muyenera kusonyeza kuti chofunika kwambiri pa moyo wanu ndi kuchita chifuniro cha Yehova Mulungu.—Werengani 1 Petulo 4:2.

MUSAMAKAYIKIRE ZOTI MUKHOZA KUKWANITSA

17. N’chifukwa chiyani ena safuna kudzipereka kwa Mulungu?

17 Anthu ena safuna kudzipereka kwa Yehova chifukwa cha mantha. Iwo amaopa kuti akakhala Mkhristu wobatizidwa ndiye kuti Mulungu azifuna kuti azichita zolondola zokhazokha. Chifukwa choopa kuti akhoza kulakwitsa zinazake n’kukhumudwitsa Yehova, iwo amaona kuti ndi bwino kungokhala osadzipereka.

18. N’chiyani chingakulimbikitseni kuti mudzipereke kwa Mulungu?

18 Mukayamba kukonda kwambiri Yehova, mudzafunitsitsa kudzipereka ndiponso kuyesetsa kumachita zinthu zosonyeza kuti munadzipereka. (Mlaliki 5:4) Mukadzipereka, mungafunike kuti “muziyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti muzimukondweretsa pa chilichonse.” (Akolose 1:10) Kukonda Mulungu kungachititse kuti musamaone zimenezi ngati zovuta. Mudzakhala ndi maganizo ofanana ndi amene mtumwi Yohane anali nawo, yemwe analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yohane 5:3.

19. N’chifukwa chiyani simuyenera kuopa kudzipereka kwa Mulungu?

19 Si kuti mukufunikira kukhala angwiro kuti mudzipereke kwa Mulungu. Yehova amadziwa kuti pali zinthu zina zimene simungakwanitse ndipo safuna kuti muzichita zimene simungakwanitse. (Salimo 103:14) Iye amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino ndipo ndi wofunitsitsa kukuthandizani. (Werengani Yesaya 41:10.) Musamakayikire kuti ngati mumakhulupirira Yehova ndi mtima wanu wonse, ‘iye adzawongola njira zanu.’—Miyambo 3:5, 6.

MUYENERA KUBATIZIDWA POSONYEZA KUTI MUNADZIPEREKA

20. N’chifukwa chiyani munthu amene wadzipereka kwa Yehova ayenera kulengeza poyera zimenezi?

20 Kuganizira zimene tangokambiranazi kungakuthandizeni kuti mudzipereke kwa Yehova m’pemphero. Aliyense amene amakonda Mulungu ayenera ‘kulengeza poyera chikhulupiriro chake kuti adzapulumuke.’ (Aroma 10:10) Kodi mungalengeze bwanji chikhulupiriro chanu?

Ubatizo umatanthauza kufa ku moyo wakale ndi kuukitsidwa kuti uyambe moyo wochita chifuniro cha Mulungu

21, 22. Kodi ‘mungalengeze’ bwanji poyera za chikhulupiriro chanu?

21 Muyenera kufotokozera wogwirizanitsa ntchito za akulu wa mpingo wanu kuti mukufuna kubatizidwa. Iye adzakonza zoti akulu ena akambirane nanu mafunso angapo okhudza mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Ngati akulu amenewa ataona kuti mukuyenera kubatizidwa, adzakudziwitsani kuti mubatizidwa pa msonkhano wotsatira. * Pamisonkhano imeneyi pamakambidwa nkhani imene imafotokoza tanthauzo la ubatizo. Kenako wokamba nkhaniyo amapempha onse amene akuyembekezera kubatizidwa kuti ayankhe mafunso awiri osavuta. Mafunso amenewa ndi njira imodzi ‘yolengezera poyera’ chikhulupiriro chawo.

22 Kubatizidwaku ndi kumene kumasonyeza anthu onse kuti munadzipereka kwa Mulungu ndipo tsopano ndinu wa Mboni za Yehova. Munthu akamabatizidwa, amamizidwa yense m’madzi posonyeza kwa anthu kuti wadzipereka kwa Yehova.

ZIMENE UBATIZO UMATANTHAUZA

23. Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera” kumatanthauza chiyani?

23 Yesu ananena kuti otsatira ake ayenera kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” (Mateyu 28:19) Zimenezi zikutanthauza kuti munthu amene akubatizidwayo ayenera kudziwa udindo umene Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu ali nawo. (Salimo 83:18; Mateyu 28:18) Zimasonyezanso kuti munthuyo akudziwa ntchito imene mzimu woyera umagwira. Mzimu umenewu ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito.—Agalatiya 5:22, 23; 2 Petulo 1:21.

24, 25. (a) Kodi ubatizo umaimira chiyani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’mutu womaliza?

24 Komatu ubatizo ndi mwambo wapadera wosafunika kuuona mopepuka. Pamene mukuviikidwa m’madzi zimasonyeza kuti mwafa ku moyo wanu wakale. Mukamavuulidwa zimasonyeza kuti tsopano mwaukitsidwa kuti muyambe moyo wochita chifuniro cha Mulungu. Muyeneranso kukumbukira kuti munadzipereka kwa Yehova Mulungu, osati kwa munthu mnzanu, ku ntchito inayake, kapena kugulu linalake. Mukadzipereka ndiponso kubatizidwa mumayamba kugwirizana kwambiri ndi Mulungu, moti amakhala ngati mnzanu.—Salimo 25:14.

25 Komatu si kuti munthu akabatizidwa ndiye kuti basi adzapulumuka. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera.” (Afilipi 2:12) Kubatizidwa kwangokhala poyambira chabe. Chinthu chofunika ndi kuyesetsa kuti Mulungu apitirize kukukondani. Mutu womaliza wa bukuli ufotokoza mmene tingachitire zimenezi.

^ ndime 21 Ubatizo umachitika pamisonkhano yonse ikuluikulu ya pa chaka ya Mboni za Yehova.