Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 5

Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse

Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse
  • Kodi dipo n’chiyani?

  • Nanga linaperekedwa bwanji?

  • Kodi inuyo mungapindule bwanji ndi mphatso imeneyi?

  • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira mphatsoyi?

1, 2. (a) Kodi inuyo mumaona kuti mphatso imakhala yamtengo wapatali ikakhala yotani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti nsembe ya dipo ndi mphatso yamtengo wapatali kuposa zonse?

KODI munayamba mwalandirapo mphatso inayake imene mumaiona kuti ndi yamtengo wapatali kuposa zonse? Kuti mphatso ikhale yamtengo wapatali sizichita kufunikira kuti ikhale ya ndalama zambiri. Ngakhale mphatso itakhala ya ndalama zochepa, ikhoza kukhala yamtengo wapatali ngati yakusangalatsani kapena ngati yakuthandizani kupeza zinthu zimene mumazisowa.

2 Pali mphatso imodzi yomwe ndi yamtengo wapatali kwambiri kuposa zonse. Mphatso imeneyi ndi yomwe Mulungu anapereka kwa anthu. Yehova anatipatsa zinthu zambirimbiri koma mphatso yamtengo wapatali kuposa zonse ndi nsembe ya Mwana wake, Yesu Khristu. (Werengani Mateyu 20:28.) Monga mmene tionere m’mutuwu, nsembe imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri chifukwa ingakuthandizeni kukhala osangalala komanso ingakuthandizeni kupeza zinthu zimene mumazisowa. Zimene Yehova anachita potipatsa nsembeyi ndi umboni woti amatikonda kwambiri.

KODI DIPO LA YESU N’CHIYANI?

3. Kodi dipo la Yesu n’chiyani, nanga tikufunika kudziwa chiyani kuti timvetse kuti imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali?

3 Kunena mwachidule, dipo la Yesu ndi njira imene Yehova anagwiritsa ntchito kuti apulumutse anthu ku uchimo ndi imfa. (Aefeso 1:7) Kuti timvetse zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi, tiyenera kuganizira zomwe zinachitika m’munda wa Edeni. Tikadziwa bwino zimene Adamu anataya atachimwa, m’pomwe tingamvetse kuti nsembe ya dipo ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri.

4. Monga munthu wangwiro, kodi Adamu akanakhala ndi moyo wotani?

4 Yehova polenga Adamu anam’patsa chinthu chamtengo wapatali kwambiri, womwe ndi moyo wangwiro. Taganizirani moyo umene Adamu akanakhala nawo. Chifukwa choti anali wangwiro, sakanadwala, kukalamba kapena kufa. Monga munthu wangwiro, iye ankagwirizananso kwambiri ndi Yehova. Baibulo limanena kuti Adamu anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Zimenezi zikusonyeza kuti Adamu ankagwirizana kwambiri ndi Yehova ngati mmene mwana amagwirizanirana ndi abambo ake. Komanso Yehova ankalankhulana ndi Adamu pamene ankamupatsa ntchito yoti azigwira ndiponso malamulo oti azitsatira.—Genesis 1:28-30; 2:16, 17.

5. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena kuti Adamu analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu”?

5 Adamu analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.” (Genesis 1:27) Koma zimenezi si zikutanthauza kuti ankaoneka mofanana ndi Mulungu. Monga tinaphunzirira m’mutu woyamba, Yehova ndi mzimu ndipo sitingamuone. (Yohane 4:24) Choncho si kuti Yehova ali ndi thupi lofanana ndi la munthu. Mawu akuti Adamu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu akutanthauza kuti Adamu analengedwa ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu, ngati chikondi, nzeru, chilungamo ndi mphamvu. Adamu analinso wofanana ndi Mulungu pa nkhani yokhala ndi ufulu wotha kusankha zochita. Choncho Adamu sanalengedwe ngati matchini omwe saganiza, amangogwira ntchito zomwe anawakonzera kuti azigwira. Iye anali ndi ufulu wosankha zimene akufuna kuchita, kaya zabwino kapena zoipa. Adamu akanasankha kumvera Mulungu, akanakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansili.

6. Pamene Adamu sanamvere Mulungu, kodi anataya mwayi wotani, nanga zimenezi zinakhudza bwanji ana awo?

6 Choncho pamene Adamu anasankha kusamvera Mulungu anataya mwayi waukulu chifukwa anaweruzidwa kuti ayenera kufa. Kusamvera kwake kunachititsa kuti asakhalenso ndi moyo wangwiro komanso kuti asakhale ndi madalitso amene akanakhala nawo ngati akanamvera. (Genesis 3:17-19) N’zomvetsa chisoni kuti Adamu anataya moyo wamtengo wapatali ndipo zimene anachitazi zinakhudzanso ana ake. Mawu a Mulungu amanena kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Choncho tonse tinatengera uchimo kuchokera kwa Adamu. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti iye anadzigulitsa limodzi ndi ana ake ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Aroma 7:14) Adamu ndi Hava analibe mwayi womveredwa chisoni chifukwa anasankha dala kusamvera Mulungu. Nanga bwanji ana awo, kuphatikizapo ifeyo?

7, 8. Kodi dipo lingatanthauze zinthu ziwiri ziti?

7 Pofuna kuti apulumutse anthu, Mulungu anakonza zopereka dipo. Kodi dipo n’chiyani? Dipo lingatanthauze zinthu ziwiri. Choyamba, ndi ndalama kapena katundu amene amaperekedwa kwa chigawenga chomwe chagwira munthu, n’cholinga choti munthuyo amasulidwe. Chachiwiri, dipo ndi ndalama kapena katundu amene mtengo wake ndi wofanana ndi zinthu zimene zawonongedwa. Mwachitsanzo, ngati munthu wachititsa ngozi n’kuvulaza anthu kapena kuwononga katundu, amayenera kulipira ndalama zogwirizana ndi zinthu zimene zawonongekazo.

8 Koma kodi zikanatheka bwanji kulipirira zinthu zimene zinawonongeka pamene Adamu anachimwa n’kuchititsa kuti anthu akhale akapolo a uchimo ndi imfa? Tiyeni tikambirane za dipo limene Yehova anapereka n’cholinga choti timasulidwe ku ukapolowu. Tikambirananso madalitso amene tingapeze chifukwa cha dipo limeneli.

MMENE YEHOVA ANAPEREKERA DIPOLI

9. Kodi dipo limene linkafunika linali lotani?

9 Popeza moyo umene unatayika unali wangwiro, kupereka moyo wopanda ungwiro sikukanakhala kokwanira kuti anthu amasulidwe. (Salimo 49:7, 8) Panafunika dipo lofanana ndendende ndi zimene zinatayika. Zimenezi n’zogwirizana ndi mfundo yopezeka m’Mawu a Mulungu yosonyeza kuti zinthu ziyenera kuchitika mwachilungamo, yomwe imati: “Pazikhala moyo kulipira moyo.” (Deuteronomo 19:21) Ndiye kodi moyo wangwiro umene Adamu anataya ukanalipiridwa bwanji? Panafunika moyo winanso wangwiro kuti likhale “dipo lokwanira ndendende.”—1 Timoteyo 2:6.

10. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito ndani popereka dipo?

10 Kodi Yehova anagwiritsa ntchito ndani popereka dipo limeneli? Anatumiza padziko lapansi mmodzi mwa ana ake angwiro akumwamba. Komatu Yehova sanangotumiza mngelo aliyense. Anatumiza mwana wake wapadera kwambiri. (Werengani 1 Yohane 4:9, 10.) Mwana wakeyo analolera kuchoka kumwamba n’kubwera padziko lapansi. (Afilipi 2:7) Monga tinaphunzirira m’mutu wapita uja, Yehova anachita chozizwitsa pamene anasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya. Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti Yesu abadwe wangwiro moti chilango cha uchimo sichinkamukhudza.—Luka 1:35.

Yehova anapereka Mwana wake wapadera ngati dipo lotipulumutsa

11. Kodi zinatheka bwanji kuti munthu mmodzi apulumutse anthu ambiri?

11 Koma kodi munthu mmodzi angapulumutse bwanji anthu ambirimbiri? Kuti tipeze yankho la funso limeneli, tiyenera kukumbukira zimene zinachitika kuti anthu ambirimbiriwo akhale ochimwa. Kumbukirani kuti pamene Adamu anachimwa anataya mwayi wamtengo wapatali wokhala ndi moyo wangwiro. Choncho ana ake onse anabadwa ochimwa ndipo zimenezi zinachititsa kuti akhale opanda ungwiro komanso azifa. Yesu, amene Baibulo limamutchula kuti ndi “Adamu womalizira,” anali wangwiro ndipo sanachitepo tchimo. (1 Akorinto 15:45) Tingati Yesu analowa m’malo mwa Adamu kuti atipulumutse. Pamene Yesu anapereka nsembe moyo wake ndiponso kukhala wokhulupirika kwa Mulungu, analipira zimene Adamu anawononga atachimwa. Zimene Yesu anachitazi zinathandiza kuti ana a Adamu akhale ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wangwiro.—Aroma 5:19; 1 Akorinto 15:21, 22.

12. Kodi kukhulupirika kwa Yesu pamene ankazunzidwa kunali kofunika bwanji?

12 Baibulo limatifotokozera momveka bwino mavuto amene Yesu anakumana nawo asanaphedwe. Yesu anafa mozunzika kwambiri chifukwa anakwapulidwa kenako n’kukhomereredwa pamtengo. (Yohane 19:1, 16-18, 30; Zakumapeto, tsamba 204-206) Koma kodi zinali zofunika kuti Yesu avutike chonchi? M’mutu wina kutsogoloku tiona kuti Satana anakayikira zoti munthu angatumikire Yehova mokhulupirika atakumana ndi mavuto. Kupirira kwa Yesu pamene ankazunzidwa kunasonyeza kuti zimene Satana ananenazo zinali zabodza. Yesu anasonyeza kuti munthu wangwiro yemwe ali ndi ufulu wosankha zochita akhoza kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale Satana atamuzunza kwambiri. Yehova ayenera kuti anasangalala kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwa Mwana wake wokondedwayu.—Miyambo 27:11.

13. Kodi Yehova anapereka bwanji dipo?

13 Kodi Yehova anapereka bwanji dipoli? M’chaka cha 33 C.E., pa tsiku la 14 la mwezi womwe Ayuda ankautchula kuti Nisani, Mulungu analola kuti Mwana wake wangwiro aphedwe. Choncho Yesu anapereka nsembe moyo wake wangwiro “kamodzi kokha.” (Aheberi 10:10) Pa tsiku lachitatu, Yehova anamuukitsa ndipo anakhalanso mzimu ngati mmene analili asanabwere padziko lapansi. Atamaliza ntchito imene Mulungu anam’patsa, Yesu anabwerera kwa Mulungu kumwamba kumene Mulungu analandira mtengo wa moyo wangwiro umene Yesu anapereka kuti apulumutse ana a Adamu. (Aheberi 9:24) Yehova anaona kuti mtengo wa nsembe ya Yesu unali wokwanira kulipirira anthu kuti amasulidwe ku ukapolo wa uchimo ndi imfa.—Werengani Aroma 3:23, 24.

MMENE MUNGAPINDULIRE NDI DIPO LA YESU

14, 15. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu atikhululukire machimo athu?

14 Ngakhale kuti ndife ochimwa, tikhoza kulandira madalitso ambiri chifukwa cha nsembe ya Yesu. Tiyeni tikambirane madalitso ena amene tingalandire panopo komanso m’tsogolo chifukwa cha mphatso yamtengo wapatali imeneyi.

15 Mulungu amatikhululukira machimo athu. Chifukwa choti tinabadwa ochimwa, nthawi zina timalephera kuchita zinthu zoyenera. Tonse timachimwa chifukwa cha zimene timalankhula kapena kuchita. Koma chifukwa cha nsembe ya Yesu, ‘machimo athu amakhululukidwa.’ (Akolose 1:13, 14) Komabe kuti Mulungu atikhululukire tiyenera kulapa mochokera pansi pa mtima komanso kukhulupirira nsembeyo. Tiyeneranso kupemphera kwa Yehova modzichepetsa, kumupempha kuti atikhululukire machimo athu pogwiritsa ntchito nsembe ya Mwana wake.—Werengani 1 Yohane 1:8, 9.

16. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizitumikira Mulungu momasuka, nanga kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kofunika bwanji?

16 Timatumikira Mulungu momasuka. Munthu akalakwitsa zinazake amakhala wosasangalala ndipo amadziona ngati wachabechabe. Koma kudziwa kuti Yehova amatikhululukira chifukwa cha nsembe ya dipo kumatithandiza kuti tizimutumikira momasuka ngakhale kuti ndife ochimwa. (Aheberi 9:13, 14) Timathanso kulankhulana naye momasuka m’pemphero. (Aheberi 4:14-16) Kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kumatithandiza kuti tizisangalala ndiponso tisamadzione ngati achabechabe.

17. Kodi tidzapeza madalitso ati chifukwa choti Yesu anatifera?

17 Tidzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Lemba la Aroma 6:23 limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa,” koma limapitirizanso kuti: “Mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” M’mutu 3, tinakambirana madalitso amene anthu adzasangalale nawo m’Paradaiso. (Chivumbulutso 21:3, 4) Madalitso onse a m’tsogolo kuphatikizapo kukhala ndi moyo wosatha komanso wangwiro, adzatheka chifukwa Yesu anatifera. Kuti tidzalandire madalitso amenewa, tiyenera kusonyeza kuti timayamikira mphatso ya dipo.

KODI MUNGASONYEZE BWANJI KUYAMIKIRA MPHATSO IMENEYI?

18. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha dipo la Yesu?

18 N’chifukwa chiyani tiyenera kuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha dipo la Yesu? Mphatso imakhala yamtengo wapatali ukaganizira nthawi, mphamvu komanso zinthu zina zimene munthu amene wakupatsa mphatsoyo wawononga. Timayamikira kwambiri poona kuti mphatsoyo ndi umboni wakuti woperekayo amatikonda kwambiri. Dipo ndi mphatso yamtengo wapatali kuposa mphatso zonse, chifukwa Mulungu anawononga zambiri kuti apereke mphatsoyi. Lemba la Yohane 3:16 limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.” Choncho dipo la Yesu ndi umboni wakuti Yehova amatikonda kwambiri. Komanso ndi umboni wakuti Yesu amatikonda chifukwa analolera kupereka moyo wake kuti atipulumutse. (Werengani Yohane 15:13.) Mphatso ya dipo iyenera kutithandiza kudziwa kuti Yehova ndi Mwana wake amatikonda, aliyense payekha.—Agalatiya 2:20.

Kuphunzira za Yehova ndi njira imodzi yosonyezera kuti timayamikira mphatso ya dipo imene anatipatsa

19, 20. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira mphatso ya dipo?

19 Koma kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira mphatso imeneyi? Choyamba, muyenera kuyesetsa kuti mumudziwe Yehova yemwe anapereka mphatsoyi. (Yohane 17:3) Kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito bukuli kungakuthandizeni kuti mumudziwe. Mukadziwa zambiri zokhudza Yehova, m’pamene mudzayambe kumukonda kwambiri. Zimenezi zidzakuchititsani kuti muzifunitsitsa kuchita zinthu zimene amasangalala nazo.—1 Yohane 5:3.

20 Muzisonyeza kuti mumakhulupirira nsembe ya Yesu. Ponena za Yesu Baibulo limati: “Wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:36) Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yesu? Si zingatheke kuchita zimenezi ndi mawu okha. Lemba la Yakobo 2:26 limati: “Chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” Choncho chikhulupiriro chenicheni chimaoneka ndi “ntchito,” kapena kuti zochita zathu. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakhulupirira Yesu ndi kuyesetsa kumutsanzira, osati pa zolankhula zokha komanso pa zimene timachita.—Yohane 13:15.

21, 22. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupezeka pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye? (b) Kodi Mitu 6 ndi 7 idzafotokoza chiyani?

21 Muzipezeka pa mwambo wa Mgonero wa Ambuye. Madzulo a pa Nisani 14, 33 C.E., Yesu anayambitsa mwambo wapadera umene Baibulo limautchula kuti “Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.” (1 Akorinto 11:20; Mateyu 26:26-28) Mwambo umenewu umatchulidwanso kuti Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Yesu anayambitsa mwambo umenewu n’cholinga choti ophunzira ake komanso Akhristu onse oona azikumbukira kuti iye anapereka moyo wake wangwiro ngati nsembe. Ponena za dipo limeneli, Yesu analamula kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Kupezeka pa Chikumbutso kumatikumbutsa chikondi chimene Yehova komanso Yesu anatisonyeza popereka dipo. Tingasonyeze kuti timayamikira mphatso ya dipo ngati timapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu womwe umachitika chaka chilichonse. *

22 Mfundo zimene takambirana m’nkhaniyi zikusonyeza kuti dipo limene Yehova anapereka ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri. (2 Akorinto 9:14, 15) Mphatso imeneyi ndi yothandizanso kwa anthu amene anamwalira. Mitu 6 ndi 7 idzafotokoza chifukwa chake tikunena choncho.

^ ndime 21 Kuti mumve mfundo zambiri zokhudza mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, werengani Zakumapeto, tsamba 206-208.