Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinaphunzila Kuti Yehova ndi Wacifundo ndi Wokhululukila

Ndinaphunzila Kuti Yehova ndi Wacifundo ndi Wokhululukila
  • CAKA COBADWA: 1954

  • DZIKO: CANADA

  • MBILI YANGA: NDINALI WACINYENGO NDI WANJUNGA

KUKULA KWANGA:

Ndinakulila ku dela kumene kunali mavuto azacuma mumzinda wa Montreal. Atate anamwalila ndili ndi zaka 6 ndipo zimenezi zinapangitsa kuti amai akhale ndi nchito yaikulu yotisamalila. Ndinali mwana wothela m’banja la ana 8.

Ndinakula ndi umoyo wokonda mankhwala osokoneza ubongo, njunga, ciwawa, ndi kugwilizana ndi zigaŵenga. Nditafika zaka 10, ndinayamba kutumikila mahule ndi anthu amene anali kucita katapila kapena kuti kukongoza ndalama zakaloŵa. Ndinali kukonda kunama mabodza ndi kucita zinthu zacinyengo za mtundu uliwonse. Kucita zimenezi kunali ngati cakudya canga.

Nditafika zaka 14, ndinali nditaphunzila kale njila zambili zonamizila anthu. Mwacitsanzo, ndinali kugula zinthu zambili zopakidwa golide mwacinyengo monga mphete, zibangili, ndolo kapena kuti masikiyo n’kuzidinda mau akuti golide wolemela magalamu 2.8. Ndipo zinthu zimenezi ndinali kuzigulitsila m’malo oimikapo magalimoto pa masitolo akuluakulu. Ndinali kupeza ndalama mosavuta pogwilitsila nchito njila zimenezi. Nthawi ina ndinapeza ndalama zokwanila $10,000 pa tsiku limodzi lokha.

Ndili ndi zaka 15, ndinacotsedwa pa sukulu yophunzitsa cikhalidwe ndipo ndinasowa kokhala. Ndinali kugona m’makwalala, m’mapaki, kapenanso kwa anzanga.

Nthawi zambili a polisi anali kundikaikila cifukwa ca zocita zanga zacinyengo. Popeza sindinali kugulitsa zinthu zakuba, sanapeze cifukwa condiikila m’ndende. Komabe, anali kundilipilitsa ndalama zambili kaamba ka cinyengo canga ndi kugulitsa katundu popanda cilolezo. Popeza sindinali kuopa aliyense, ndinali kutumidwa kukatenga ndalama zakaloŵa. Zimenezo zinali zoopsa cakuti nthawi zina ndinali kunyamula mfuti. Ndipo mwa apa ndi apo, ndinali kugwila nchito ndi gulu la zigaŵenga.

MMENE BAIBULO LINASINTHILA UMOYO WANGA:

Ndinamvapo za Baibulo koyamba ndili ndi zaka 17. Panthawiyi ndinali kukhala ndi cisumbali canga cimene cinali kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komabe ndinali kudana ndi malamulo amakhalidwe abwino a m’Baibulo. Conco ndinacoka n’kukakhala ndi mkazi wina amene ndinatomela.

Zinthu zinasintha pamene cisumbali canga caciŵili cinayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anasintha umoyo wake ndipo anakhala wofatsa ndi wodzicepetsa, conco ndinakondwela naye kwambili. Atandipempha kukasonkhana ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ndinavomela. Anthu amene anandilandila anali aulemu ndi okoma mtima. Iwo anali osiyana kwambili ndi anthu ena amene ndinali kukhala nao. Kucokela pa umwana wanga ndinali ndisanawonetsedwepo cikondi cotelo ngakhale ndi anthu a m’banja langa. Kunena zoona cikondi cimene a Mboni za Yehova anandionetsa ndi cimene ndinali kufunika. Pamene a Mboni anandipempha kuphunzila Baibulo ndinavomela.

Kukamba zoona zimene ndinali kuphunzila m’Baibulo zandithandiza kukhalapo ndi moyo. Popeza ndinali ndi ngongole za njunga zoculuka kuposa pa $50,000 ndinapangana ndi anzanga aŵili kuti tikabe ndalama n’colinga cakuti ndibweze ngongolezo. Ndine wokondwela kwambili kuti sindinapite nao. Iwo anapitabe ndipo mmodzi anamangidwa, wina anaphedwa.

Pamene ndinali kuphunzila Baibulo ndinaona kuti ndifunika kusintha zinthu zambili. Mwacitsanzo ndinaphunzila zimene Baibulo limanena pa 1 Akorinto 6:10 kuti: “Akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.” Nditaŵelenga vesili ndinagwetsa misozi poona mmene zinthu zinalili ndi ineyo. Ndinazindikila kuti ndifunika kusintha umoyo wanga kothelatu. (Aroma 12:2) Ndinali munthu waciwawa, wamkali ndipo ndinali kukhalila kunama mabodza.

Komabe ndinaphunzila kuti Yehova ndi wacifundo ndi wokhululukila. (Yesaya 1:18) Ndinacondelela Yehova m’pemphelo kuti andithandize kuleka khalidwe langa. Mothandizidwa ndi iye ndinasintha umoyo wanga mwapang’onopang’ono. Ine ndi cisumbali canga tinazindikila kuti tifunika kulembetsa ukwati wathu ku boma.

Ndilipo ndi moyo cifukwa cotsatila mfundo za m’Baibulo

Panthawiyi ndinali ndi ana atatu, apo n’kuti ndili ndi zaka 24. Ndinali kufunika kupeza nchito yabwino koma ndinalibe mapepala a kusukulu. Ndinapemphelanso kwa Yehova ndi mtima wonse ndipo ndinapita kukafuna nchito. Ndinauza wolemba nchito kuti ndifuna kusintha umoyo wanga ndi kuti ndizigwila nchito yabwino. Nthawi zina ndinali kuwauza kuti ndinali kuphunzila Baibulo ndi kuti ndinali kufuna kukhala nzika yabwino. Koma olemba nchito ambili anakana kundilemba. Pomalizila pake, nditawafotokozela zonse za umoyo wanga wa kale anavomela kundilemba nchito ndipo anati: “Ndikulembabe nchito, ngakhale kuti sindikudziŵa cimene cikundicititsa kuti ndikulembe.” Ndikukhulupilila ndi mtima wanga wonse kuti limeneli linali yankho la mapemphelo anga. Mkupita kwa nthawi, ine ndi mkazi wanga tinabatizika n’kukhala Mboni za Yehova.

MAPINDU AMENE NDAPEZA:

Ndilipo ndi moyo cifukwa cotsatila mfundo za m’Baibulo ndi kukhala ndi umoyo wacikristu. Ndikusangalala ndi banja langa ndipo ndikutumikila ndi cikumbumtima coyela cifukwa ndikutsimikiza kuti Yehova anandikhululukila.

Ndakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 14. Pa zaka zonsezi ndakhala ndikuthandiza anthu kudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo posacedwapa mkazi wanga anayamba utumiki wa nthawi zonse. Ndine wokondwela kwambili kuti pa zaka 30 zapitazi ndathandiza anzanga akunchito 22 kuyamba kulambila Yehova. Ndimapitabe ku masitolo akuluakulu osati kukacitila anthu zacinyengo, koma kukawauza za cikhulupililo canga. Ndimafuna kuwathandiza kukhala ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano mmene simudzakhala cinyengo.—Salimo 37:10, 11.