Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nimakondwela kuceza ndi acicepele a mu mpingo wathu

BAIBO IMASINTHA ANTHU

N’nali Kukonda Baseball Kuposa Cina Ciliconse

N’nali Kukonda Baseball Kuposa Cina Ciliconse
  • CAKA COBADWA: 1928

  • DZIKO: COSTA RICA

  • MBILI: ANALI WOLOŴELELA M’ZAMASEŴELA NA NJUGA

MBILI YANGA

N’nakulila m’tauni ya Puerto Limón ndi m’madela ena a kufupi ndi tauniyi. Tauni yokhala na doko imeneyi ili kum’maŵa kwa dziko la Costa Rica. Makolo anga anali ndi ana 8. Ine n’nali mwana wawo wa namba 7. Atate anamwalila pamene n’nali na zaka 8. Kucokela nthawi imeneyo, amayi ndiwo anatilela.

Maseŵela a Baseball * anali mbali ya umoyo wanga. Nili mwana, n’nali kukonda kucita maseŵela amenewa. N’tafika zaka zaunyamata, n’naloŵa m’timu inayake ya baseball. Nili m’timu imeneyi, munthu wina ananipempha kuyenda ku Nicaragua kukagwilizana ndi timu ya akatswili pa maseŵela amenewa. Apo n’kuti nili na zaka za m’ma 20. Komabe, sin’nafune kuyenda kukakhala ku Nicaragua cifukwa amayi anali kudwala-dwala, ndipo ndine n’nali kuwasamalila panthawiyo. Conco, n’nakana mwayi umenewu. Patapita nthawi, winanso ananipempha kuti nizichaya baseball m’timu ya dziko lathu la Costa Rica, imene inali ndi anthu osankhidwa kucokela m’matimu wamba. Apa n’navomela pempho limenelo. N’nakhala m’timu ya dziko lathu kucokela mu 1949 mpaka mu 1952, ndipo n’nakacitako maseŵelawa m’dziko la Cuba, Mexico, ndi Nicaragua. N’nafika pokhala katswili m’maseŵela amenewa. N’nali kukwanitsa kucita maseŵelawa maulendo ambili popanda kuphonya ciliconse. N’nali kukondwela maningi nikamvela anthu akunisapota.

Comvetsa cisoni n’cakuti n’nali kucitanso zaciwelewele. Ngakhale kuti n’nali na cibwenzi cimodzi cokha, n’nalinso kuyenda ndi akazi ena, komanso n’nali cakolwa. Tsiku lina n’nakolewa kwambili cakuti n’tadzuka m’maŵa, sin’nathe kukumbukila mmene n’nafikila panyumba. N’nalinso kuchova njuga za mitundu yosinaya-siyana.

Pamene n’nali na makhalidwe amenewa, amayi anakhala a Mboni za Yehova. Iwo anayesa-yesa kuti anikope na cikhulupililo cawo, koma poyamba sizinaphule kanthu cifukwa n’nali woloŵelela kwambili m’zamaseŵela. Nikamacita mapulakatisi m’bwalo la maseŵela panthawi ya cakudya, sin’nali kumvela njala. Maganizo anga onse anali pa maseŵela basi. N’nali kukonda baseball kuposa cina ciliconse.

Nili na zaka 29, n’navulala kwambili pamene n’nali kufuna kugwila bola poseŵela. N’tacila, n’naleka kuseŵela m’timu ya akatswili. Komabe, n’nali kuphunzitsa timu ya kufupi ndi kwathu za maseŵela amenewa.

MMENE BAIBO INASINTHILA UMOYO WANGA

Mu 1957, n’nalandila ciitano cakuti nikapezeke pa msonkhano wa Mboni za Yehova. Msonkhanowo unali kucitikila m’bwalo la maseŵela limene n’nali kuchailamo baseball. N’takhala m’gulu, n’nacita cidwi kuona kuti Mboni zinali zaulemu kusiyana ndi anthu ocita phokoso amene n’nali kuona pocita maseŵela a baseball. Zimene n’naona pa msonkhanowo zinapangitsa kuti niyambe kuphunzila Baibo na Mboni, na kupezeka pa misonkhano yawo ya mpingo.

N’nakhudzidwa mtima na zinthu zambili zimene n’naphunzila m’Baibo. Mwacitsanzo, Yesu anakambilatu kuti m’masiku otsiliza, ophunzila ake adzalalikila uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) N’naphunzilanso kuti Akhristu oona sacita utumiki wawo kuti apezelepo ndalama. Yesu anati: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.”—Mateyu 10:8.

Pamene n’nayamba kuphunzila Baibo, n’nali kuyelekezela zimene imakamba na zimene n’nali kuona pakati pa Mboni za Yehova. N’nali kucita cidwi ndi khama lawo panchito yofalitsa uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu padziko lonse. N’naona kuti anali na mzimu wopatsa umene Yesu analamula Akhristu kukhala nawo. Conco, n’taŵelenga Maliko 10:21 limene pali ciitano ca Yesu cakuti, ‘Bwela ukhale wotsatila wanga,’ n’nafunitsitsa kukhala Mboni.

Komabe, panatenga nthawi kuti nisinthe. Mwacitsanzo, kwa zaka zambili n’nali na namba yanga ya “mwayi” yochovela njuga ya lottery wiki iliyonse. Koma n’naphunzila m’Baibo kuti Mulungu amazonda anthu amene amalambila “mulungu wa Mwayi,” komanso anthu adyela. (Yesaya 65:11; Akolose 3:5) Conco, n’naleka kuchova njuga. Pa Sondo mu wiki imene n’naleka kuchova lottery, namba yanga ya “mwayi” inawina. Anthu ananiseka cifukwa sin’nachoveko njuga wiki imeneyo, ndipo ananikakamiza kuti niyambenso, koma n’nakana. Kucokela nthawi imeneyo, sin’nachovenso njuga.

N’nakumananso na ciyeso cina pambuyo pakuti navala “umunthu watsopano.” Linali tsiku limene n’nabatizika pa msonkhano wacigawo wa Mboni za Yehova. (Aefeso 4:24) Ndiyeno m’madzulo, n’nabwelela ku hotela kumene n’nali kukhala, ndipo n’napeza cibwenzi canga cakale cikuniyembekeza pakhomo la cipinda canga. Iye ananiuza kuti: “Tabwela Sammy, tiye tisangalatsane!” Mwamsanga n’namuyankha kuti, “Ine toto!” N’namuuza kuti n’nali n’tayamba kutsatila miyezo ya makhalidwe abwino ya m’Baibo. (1 Akorinto 6:18) Pamenepo anazazuka kuti, “Wati ciani?” Ndiyeno anasuliza zimene Baibo imakamba pankhani ya ciwelewele, ndipo ananikakamiza kuti tiyambenso cibwenzi. Koma ine n’nangoloŵa m’cipinda canga na kukhoma citseko. Ndine wokondwa kuti kucokela nthawi imene n’nakhala Mboni mu 1958, nakhalabe wokhulupilika pa zosankha zimene n’napanga pa umoyo.

MAPINDU AMENE NAPEZA

Napeza mapindu ambili cifukwa cotsatila malangizo a m’Baibo, ndipo niona kuti n’tawalemba, angadzale m’buku. Ena mwa mapindu amenewo ni awa: napeza mabwenzi eni-eni, umoyo wopindulitsa, komanso cimwemwe ceni-ceni.

Nikali kusangalala ndi maseŵela a baseball, koma siniwakonda kwambili ngati kale. Maseŵela a baseball ananibweletsela ulemelelo na ndalama, koma zinthu zimenezi sizinakhalitse. Komabe, ubale wanga na Mulungu komanso kukhala m’gulu la abale la padziko lonse, zidzakhala kwamuyaya. Baibo imati: “Dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake, koma wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yohane 2:17) Tsopano, nimakonda Yehova Mulungu ndi anthu ake kuposa cina ciliconse.

[Mau apansi]

^ par. 9 Baseball ni maseŵela a bola amene matimu aŵili amapikisana. Timu iliyonse imakhala ndi anthu 9. Munthu mmodzi wa timu ina amaponya bola ndipo wa timu ina amayesa kumenya bolayo ndi ndodo yomenyela.