Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BAIBULO IMASINTHA ANTHU

N’nali Woipa Mtima Kwambili ndi Waciwawa

N’nali Woipa Mtima Kwambili ndi Waciwawa
  • CAKA COBADWA: 1974

  • DZIKO: MEXICO

  • MBILI YANGA: MNYAMATA WOKONDA NDEWO

KUKULA KWANGA:

N’nabadwila m’dela lokongola la Ciudad Mante, m’tauni ya Tamaulipas, ku Mexico. Anthu ambili a m’dela limeneli ndi aubwenzi ndi okoma mtima. Koma cifukwa ca magulu a anthu aciwawa, delali n’loopsa kwambili.

M’banja lathu tinabadwa ana aamuna anayi, ndipo ine ndine waciŵili. Makolo anga ananibatiza ku Chalichi ca Katolika, ndipo m’kupita kwa nthawi ndinaloŵa m’gulu la oyimba khwaya. N’nali kufuna kukondweletsa Mulungu cifukwa coopa kuŵeluzidwa ndi kutenthedwa kumoto wa helo.

Pamene n’nali na zaka 5, atate anacoka panyumba n’kutisiya tokha ndi amayi. Zimenezi zinaniŵaŵa kwambili ndipo n’nali kudziona ngati wacabe-cabe. Sin’namvetsetse cifukwa cake anacoka panyumba cifukwa tinali kuwakonda kwambili. Amayi anali kugwila nchito nthawi yaitali kuti azitisamalila.

Cifukwa ca zimenezi, n’natengelapo mwayi woleka sukulu n’kuyamba kugwilizana ndi anzanga ena. Iwo ananiphunzitsa kutukwana, kupepa fwaka, kuba, na ndewo. Cifukwa cakuti n’nali kusangalala nikamavutitsa ena, n’naphunzila mitundu yosiyana-siyana ya ndewo. N’naphunzilanso kuseŵenzetsa zida pomenyana. N’nakhala waciwawa. Nthawi zambili, n’nali kumenyana ndi anthu pogwilitsila nchito mfuti. Kangapo konse, anzanga ananimenya kwambili n’kunisiya panjila poganiza kuti nafa, ndipo magazi anali kuyendelela thupi lonse. Akanipeza, amayi anali kuvutika kwambili na cisoni ndipo anali kunitenga n’kuthamangila nane ku cipatala.

Nitakwanitsa zaka 16, mnzanga wina wa paubwana, dzina lake Jorge, anabwela kunyumba kwathu. Iye anakamba kuti ni wa Mboni za Yehova ndipo afuna kutiuza uthenga wofunika kwambili. Anayamba kutifotokozela zimene amakhulupilila pogwilitsila nchito Baibulo. N’nali nisanaŵelengepo Baibulo, ndipo n’nakondwela kuphunzila za dzina la Mulungu na colinga cake. Jorge anatipempha kuti aziphunzila nafe Baibulo, ndipo tinavomela.

MMENE BAIBULO INASINTHILA UMOYO WANGA:

N’nakondwela kwambili nitaphunzila kuti moto wa helo si ciphunzitso ca m’Baibulo. (Salimo 146:4; Mlaliki 9:5) N’taphunzila zimenezi, n’nayamba kuopa Mulungu pa cifukwa coyenela osati cifukwa coopa kukatenthedwa ku moto wa helo. N’nayamba kumuona kuti ni Tate wacikondi amene amafunila zabwino ana ake.

Pamene n’naphunzila zambili za m’Baibulo, n’naona kuti nifunika kusintha khalidwe langa. N’nafunika kuyesetsa kukhala wodzicepetsa ndi kuleka ciwawa. Cimene cinanithandiza ndi malangizo a pa 1 Akorinto 15:33. Lembali limati: “Kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” N’nazindikila kuti cimene cinganithandize kusintha khalidwe langa ndi kupewa anthu amene anali kunisonkhezela kucita zoipa. Conco, n’naleka kugwilizana ndi anzanga oipawo, ndipo n’napeza mabwenzi mumpingo woona wacikhiristu. Anthu amenewa amathetsa kusamvana pogwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo osati ndewo.

Lemba lina limene linan’thandiza ni Aroma 12:17- 19. Lembali limati: “Musabwezele coipa pa coipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendele ndi anthu onse, monga mmene mungathele. . . . Musabwezele coipa, . . . pakuti Malemba amati: ‘ “Kubwezela ndi kwanga, ndidzawabwezela ndine,” watelo Yehova.’” N’nadziŵa kuti Yehova adzathetsa kupanda cilungamo m’njila yoyenela ndiponso panthawi yoyenela. Pang’ono ndi pang’ono, n’naleka zaciwawa.

Sinidzaiwala zimene zinacitika tsiku lina madzulo pamene n’nali kubwelela ku nyumba. Anyamata ena a m’gulu la acifwamba amene tinali kudana nawo poyamba, ananimenya, ndipo mtsogoleli wawo ananichaya pamsana ndi kukuwa kuti, “Dziteteze!” Panthawi imeneyo n’napeleka pemphelo lacidule kwa Yehova, n’kumupempha kuti anithandize kupilila. Mumtima cinaniwawa kwambili cakuti n’nafuna kubwezela, koma n’nathawa cabe. Tsiku lotsatila, n’nakumana ndi mtsogoleli wa gulu limenelo ali yekha. Panthawiyo n’nakwiya kwambili cakuti n’nafuna kubwezela, koma n’napemphanso Yehova camumtima kuti anithandize kubweza mkwiyo. Zimene zinanidabwitsa n’zakuti mnyamatayo anabwela pafupi n’kuniuza kuti: “Unikhululukile cifukwa ca zimene n’nakucitila dzulo usiku. Kunena zoona, ine nifuna kukhala monga iwe. Nifuna kuphunzila Baibulo.” N’nakondwela kwambili cifukwa n’nakwanitsa kubweza mkwiyo wanga. Cifukwa ca zimenezi, tinayamba kuphunzila Baibulo pamodzi ndi mnyamatayo.

Koma acibale anga sanapitilize kuphunzila Baibulo panthawiyo. Ngakhale zinali conco, n’napitiliza kuphunzila Baibulo ndipo sin’nalole wina aliyense kapena cina ciliconse kunibweza m’mbuyo. N’nadziwa kuti kugwilizana ndi anthu a Mulungu nthawi zonse kudzanithandiza kukhala wacimwemwe ndiponso kukhala m’banja labwino lauzimu. N’napitiliza kupita patsogolo, ndipo m’caka ca 1991, n’nabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

MAPINDU AMENE NAPEZA:

N’nali munthu woipa mtima, wopondeleza ena ndi waciwawa. Koma Mau a Mulungu asinthilatu umoyo wanga. Tsopano nimalengeza uthenga wamtendele wa m’Baibulo kwa aliyense amene angamvetsele. Nakhala na mwayi wotumikila monga mpainiya wa nthawi zonse kwa zaka 23 tsopano.

Kwa nthawi ndithu, n’natumikilako pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico monga wanchito wodzipeleka. Kumeneko n’nakumana ndi mlongo wina wodzipeleka potumikila Mulungu, dzina lake Claudia, ndipo tinamanga banja mu 1999. Ndine woyamikila kwambili kuti Yehova wanidalitsa ponipatsa mnzanga wokhulupilika ameneyu.

Tinakatumikila limodzi ku Mexico mumpingo wa cinenelo ca manja, ndipo tinali kuthandiza anthu ogontha kuphunzila za Yehova. Pambuyo pake, tinapemphedwa kupita ku Belize kukaphunzitsa anthu Baibulo. Ngakhale kuti tili na umoyo wosalila zambili, tili na zonse zimene zingatithandize kukhala osangalala. Sitingasithanitse mwayi umenewu na cina ciliconse.

M’kupita kwa nthawi, amayi anayambanso kuphunzila Baibulo ndipo anabatizidwa. Komanso mkulu wanga, mkazi wake ndi ana ake tsopano ndi Mboni za Yehova. Anzanga ena amene n’nali kuwauzako uthenga wa Ufumu naonso akutumikila Yehova tsopano.

N’zacisoni kuti abale anga ena anafa cifukwa sanasinthe mtima wawo wankhanza. Nimaona kuti n’kanapitiliza khalidwe la conco, inenso sembe n’nafa kale. Ndine woyamikila kwambili kuti Yehova ananikokela kwa iye ndi kwa olambila ake, amene ananiphunzitsa moleza mtima ndi mokoma mtima kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo pa umoyo wanga.