Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuyankha Mafunso A m’Baibulo

Kuyankha Mafunso A m’Baibulo

N’ciani cingakuthandizeni kukhala kholo labwino?

Makolo angalele bwino ana ao ngati akukondana ndi kulemekezana. (Akolose 3:14, 19) Makolo abwino amakonda ndi kuyamikila ana ao monga mmene Yehova Mulungu anacitila kwa mwana wake.Ŵelengani Mateyu 3:17.

Kodi mumaphunzitsa mwana wanu kukonda mulungu?

Atate wathu wakumwamba amamvetsela atumiki ake akamamuuza maganizo ao ndi zakukhosi kwao. Conco makolo angacite bwino kutengela citsanzo ca Mulungu pa nkhani ya kumvetsela pamene ana ao akulankhula. (Yakobo 1:19) Iwo ayenela kuzindikila mmene ana ao akumvela, ndipo angazindikile zimenezi ngakhale kudzela m’zimene anao angalankhule.Ŵelengani Numeri 11:11, 15.

Kodi mungaphunzitse bwanji ana anu kuti adzathe kudziimila paokha?

Monga kholo muli ndi udindo wopeleka malamulo kwa ana anu. (Aefeso 6:1) Tengelani citsanzo ca Mulungu. Iye amaonetsa cikondi kwa ana ake mwa kufotokoza momveka bwino malamulo ndi mavuto amene angakhalepo ngati sanamvele malamulowo. (Genesis 3:3) Komabe iye sakakamiza anthu kuti azimumvela, m’malo mwake amawalimbikitsa kucita zabwino kuti apindule.Ŵelengani Yesaya 48:18, 19.

Khalani ndi colinga cothandiza ana anu kukonda Mulungu. Kucita zimenezi kudzawathandiza kucita zinthu mwanzelu ngakhale pamene ali kwa okha. Mofanana ndi mmene Mulungu amaphunzitsila, citsanzo canu makolo, cingathandize pophunzitsa ana anu kukonda Mulungu.—Ŵelengani Deuteronomo 6:5-7; Aefeso 4:32; 5:1.