Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ine na mkazi wanga, Tabitha, mu ulaliki

BAIBO IMASINTHA ANTHU

N’nali Kukhulupilila Kuti Kulibe Mulungu

N’nali Kukhulupilila Kuti Kulibe Mulungu
  • CAKA COBADWA: 1974

  • DZIKO: GERMAN DEMOCRATIC REPUBLIC

  • MBILI: KUSAKHULUPILILA KUTI KULI MULUNGU

MBILI YANGA

N’nabadwila m’mudzi winawake m’tauni ya Saxony, m’dziko limene panthawiyo linali German Democratic Republic (GDR). Panyumba pathu tinali kugwilizana ndi kukondana, ndipo makolo anga anali kuniphunzitsa makhalidwe abwino. Dzikolo linali la Cikomyunizimu. Anthu ambili m’tauni ya Saxony analibe cidwi na zacipembedzo. N’nali kukhulupilila kuti kulibe Mulungu. Kuyambila nili mwana kudzafika zaka 18, zinthu ziŵili zinali zozika mizu mwa ine: Cikomyunizimu na cikhulupililo cakuti kulibe Mulungu.

N’cifukwa ciani n’nali kukonda Cikomyunizimu? Cifukwa n’nali kucilikiza mfundo yakuti anthu onse ni olingana. Kuwonjezela apo, n’nali kukhulupilila kuti cuma conse cifunika kugaŵidwa mosakondela, kuti pasakhale olemela kwambili kapena osauka. Conco, n’nali wotangwanika na kagulu ka anyamata kocilikiza Cikomyunizimu. Nili na zaka 14, n’nali kuthela nthawi yambili kutolela mapepa kuti akapangidwenso kukhala atsopano pofuna kuteteza zacilengedwe. Anthu a m’tauni ya Aue anayamikila kwambili khama langa cakuti akulu-akulu a boma ananipatsa mphoto. Olo kuti n’nali wam’ng’ono, n’nali kudziŵana ndi akulu-akulu andale ochuka a m’dziko la GDR. N’naona kuti n’nali n’zolinga zabwino, ndi kuti tsogolo langa linali lowala.

Mwadzidzidzi zinthu zinasintha. Mu 1989, mpanda wochedwa Berlin Wall unagwetsedwa, ndipo Cikomyunizimu m’cigawo ca kum’maŵa kwa Ulaya cinathela pomwepo. Zinthu zinanso zogwilitsa mwala zinatsatilapo. N’nazindikila kuti kupanda cilungamo kunali kofala m’dziko la GDR. Mwacitsanzo, anthu osacilikiza Cikomyunizimu anali kuonedwa kuti ni nzika zosafunika kweni-kweni. Kodi izi zinatheka bwanji, popeza kuti ise ocilikiza Cikomyunizimu tinali kukhulupilila kuti anthu onse ni olingana? Kodi Cikomyunizimu cinangotiphimba pamaso? Nkhawa zinanikulila kwambili.

Conco, zolinga zanga zinasintha. N’naika maganizo pa zoimba-imba na kujambula zithunzi ndi manja. N’nali kuphunzila zoimba-imba pa sukulu inayake, kuti mwina nikapite ku yunivesite, cifukwa n’nali kufunitsitsa kudzakhala katswili woimba. N’nasiyanso makhalidwe abwino amene n’naphunzila nili mwana. Cimene cinakhala cofunika kwa ine ni kusangalala na kufuna akazi ambili panthawi imodzi. Komabe, kuimba, kujambula zinthu, na kusangalala, sizinatsilize nkhawa zanga. Ngakhale zithunzi zimene n’najambula zinali kuonetsa nkhawa zanga. Kodi zinthu zidzakhala bwanji m’tsogolo? Nanga colinga ca moyo n’ciani?

N’tapeza mayankho pa mafunso anga, n’nadabwa kwambili. Tsiku lina m’madzulo nili ku sukulu, tinakhala pansi ndi anzanga kukambilana za tsogolo. Mandy, * amene anali kuphunzila pa sukululi, anali wa Mboni za Yehova. Madzulo amenewo, iye ananipatsa malangizo abwino. Ananiuza kuti: “Andreas, ngati ufuna kupeza mayankho pa mafunso ako okhudza moyo na tsogolo, uziŵelenga Baibo mwakhama.”

N’nakaikila zimene anakamba, koma n’naganiza zoŵelenga Baibo kuti nipeze mayankho. Mandy ananiuza kuti niŵelenge Danieli caputa 2, ndipo n’nadabwa na zimene n’naŵelenga. Ulosi wa pa lembali umakamba za maulamulilo amphamvu padziko lonse otsatizana-tsatizana mpaka masiku ano. Mandy ananionetsa maulosi enanso a m’Baibo okhudza tsogolo lathu. Apa lomba n’nali kupeza mayankho pa mafunso anga. Koma n’nadzifunsabe kuti, Ndani analemba maulosiwa? N’ndani angalosele za kutsogolo molondola conco? Kodi zingakhale kuti Mulungu alikodi?

MMENE BAIBO INASINTHILA UMOYO WANGA

Mandy ananidziŵikitsa kwa Horst na Angelika, amene anali a Mboni. Banjali linanithandiza kumvetsetsa Mau a Mulungu. Posapita nthawi, n’nazindikila kuti a Mboni za Yehova ndiwo okha amalemekeza dzina leni-leni la Mulungu lakuti Yehova na kuliseŵenzetsa. (Salimo 83:18; Mateyu 6:9) N’naphunzila kuti Yehova Mulungu amapatsa anthu onse ciyembekezo cokhala m’paradaiso padziko lapansi kosatha. Salimo 37:9 imati: “Oyembekezela Yehova ndi amene adzalandile dziko lapansi.” N’nacita cidwi kudziŵa kuti aliyense akhoza kukhala na ciyembekezoci, ngati ayesetsa kutsatila miyezo ya Mulungu ya makhalidwe abwino ya m’Baibo.

Komabe, n’navutika kusintha umoyo wanga kuti ugwilizane na mfundo za m’Baibo. N’nali wonyada cifukwa ca luso langa loimba. Conco, n’nafunika kuphunzila kukhala wodzicepetsa. Ndiponso, sicinali copepuka kuleka makhalidwe oipa. Niyamikila kwambili Yehova kuti ni woleza mtima ndi wacifundo, ndipo amawamvetsa anthu amene amayesetsa kucita zimene Baibo imaphunzitsa.

Cikomyunizimu na cikhulupililo cakuti kulibe Mulungu zinali zozika mizu mwa ine kwa zaka 18. Kucokela nthawiyo, Baibo yakhala ikusintha umoyo wanga. Zimene n’naphunzila zinathetsa nkhawa yanga yokhudza tsogolo, ndipo zinapangitsa kuti nikhale na umoyo waphindu. Mu 1993, n’nabatizika kukhala wa Mboni za Yehova, ndipo mu 2000 n’nakwatila Tabitha, mtumiki mnzanga wokangalika. Timathela nthawi yambili kuthandiza ena kuti adziŵe Baibo. Ambili amene timakumana nawo ali na umoyo umene n’nali nawo poyamba, wocilikiza Cikomyunizimu na kukhulupilila kuti kulibe Mulungu. Nimakhala wacimwemwe ngako pamene niwathandiza kudziŵa Yehova.

MAPINDU AMENE NAPEZA

N’tayamba kugwilizana ndi Mboni za Yehova, makolo anga anakalipa kwambili. Koma kuyambila nthawiyo, anaona kuti kugwilizana na Mboni za Yehova kunali kusintha umoyo wanga. Ndine wokondwa kuti iwo tsopano amaŵelenga Baibo na kupezeka ku misonkhano yacikhristu ya Mboni za Yehova.

Ine na mkazi wanga tikusangalala m’cikwati cathu cifukwa timayesetsa kutsatila kwambili malangizo a m’Baibo okhudza mabanja. Mwacitsanzo, kutsatila uphungu wakuti tizikhala okhulupilika kwa mnzathu wa m’cikwati kwathandiza cikwati cathu kukhalabe colimba.—Aheberi 13:4.

Sinimacitanso mantha kapena kuda nkhawa na za kutsogolo. Nimaona kuti nili m’banja la padziko lonse la abale okhulupilika, mmene muli mtendele weni-weni na mgwilizano. M’banjali palibe woposa mnzake. Izi n’zimene n’nali kukhulupilila, ndipo n’nali kufunitsitsa kuzikwanilitsa mu umoyo wanga wonse.

^ par. 12 Dzinali lasinthidwa.