Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | KODI MAPETO A DZIKOLI ALI PAFUPI?

Kodi “Mapeto A Dziko” N’ciani?

Kodi “Mapeto A Dziko” N’ciani?

Mukamva mau akuti “Mapeto ali pafupi,” kodi mumaganiza za ciani? Kodi mumaganiza za abusa ataimilila kuguwa, Baibulo lili m’manja, ndipo akulalikila mokweza mau za kutha kwa dziko? Kapena mumaganiza za mwamuna wacikulile, wandevu zazitali, atavala mkanjo ndipo waimilila pamseu kwinaku atanyamula cikwangwani ca kutha kwa dziko? Poganiza zinthu ngati zimenezi, anthu ena amacita mantha, ena amakayikila, ndipo ena zimawaseketsa.

Baibulo limati: “Mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Mapeto amenewa amachedwanso “tsiku lalikulu la Mulungu” kapena kuti “Haramagedo.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Komabe, zipembedzo zimaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana, zosokoneza ndi zoopsa pa nkhaniyi. Ngakhale n’telo, Baibulo limatiuza momveka bwino kuti mapeto n’ciani. Mau a Mulungu amatithandizanso kudziŵa kuti mapeto ali pafupi. Cacikulu koposa amatiuza zimene tingacite kuti tikapulumuke. Koma coyamba, tiyeni tione zoona zake. Kodi Baibulo limati “mapeto” n’ciani?

MAPETO A DZIKO

  1. SIKUONONGEDWA KWA DZIKO NDI MOTO.

    Baibulo limati: ‘[Mulungu] wakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.’ (Salimo 104:5) Lemba limeneli ndi malemba ena amatitsimikizila kuti Mulungu sadzaononga dziko kapena kulola kuti lionongedwe.—Mlaliki 1:4; Yesaya 45:18.

  2. SI COCITIKA CODZIDZIMUTSA.

    Baibulo limatiuza kuti Mulungu waika nthawi imene mapeto adzafika. Baibulo limati: “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziŵa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, koma Atate okha. Khalani maso, khalani chelu, pakuti simukudziŵa pamene nthawi yoikidwilatu idzafika.” (Maliko 13:32, 33) N’zoonekelatu kuti Mulungu (“Atate”) waika “nthawi yoikidwilatu” pamene mapeto adzafika.

  3. SADZABWELA NDI ZOCITA ZA ANTHU KAPENA ZINTHU ZAKUGWA KUTHAMBO.

    Nanga adzabwela bwanji? Lemba la Chivumbulutso 19:11 limati: “Nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyela. Wokwelapo wake dzina lake linali Wokhulupilika ndi Woona.” Vesi 19 imapitiliza kuti: “Ndipo ndinaona cilombo, mafumu a dziko lapansi, ndi magulu ao ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwela pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo.” (Chivumbulutso 19:11-21) Ngakhale kuti mau ambili a lemba limeneli ndi ophiphilitsa, tinganene kuti Mulungu adzagwilitsila nchito makamu a angelo kuononga adani ake.

Zimene Baibulo limanena zokhudza mapeto a dziko ndi nkhani yabwino

MAPETO A DZIKO NDI

  1. KUONONGEDWA KWA MABOMA A ANTHU.

    Baibulo limati: “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu [boma] umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2: 44) Monga tanenela kale pa mfundo yacitatu, amene adzaonongedwa ndi “mafumu a dziko lapansi, ndi magulu ao ankhondo,” amene adzasonkhana kuti “amenyane ndi wokwela pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo.”—Chivumbulutso 19:19.

  2. KUTHA KWA NKHONDO, CIWAWA NDI KUPANDA CILUNGAMO.

    Mulungu “akuletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Salimo 46:9) “Pakuti oongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda colakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzacotsedwa padziko lapansi ndipo acinyengo adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”—Chivumbulutso 21: 4, 5.

  3. KUONONGEDWA KWA ZIPEMBEDZO ZIMENE ZALAKWILA MULUNGU NDI ANTHU.

    “Aneneli akulosela monama, ndipo ansembe akupondeleza anthu ndi mphamvu zao. . . . Ndipo kodi anthu inu mudzacita ciani pamapeto pake?” (Yeremiya 5:31) “Ambili adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosele m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kucita nchito zambili zamphamvu m’dzina lanunso?’ Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: ‘Sindikukudziŵani ngakhale pang’ono! Cokani pamaso panga, anthu osamvela malamulo inu.’”—Mateyu 7:21-23.

  4. KUONONGEDWA KWA ANTHU AMENE AMAKONDA ZA DZIKOLI.

    Yesu Kristu anakamba kuti: “Tsopano maziko opelekela ciweluzo ndi awa, kuwala kwafika m’dziko koma anthu akonda mdima m’malo mwa kuwala, pakuti nchito zao n’zoipa.” (Yohane 3:19) Baibulo limasimba kuti kale dziko linaonongedwa m’masiku a Nowa, munthu wokhulupilika. Limati: “Dziko la pa nthawiyo linaonongedwa pamene linamizidwa ndi madzi. Ndipo mwa mau amodzimodziwo, kumwamba kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi, azisungila moto m’tsiku laciweluzo ndi cionongeko ca anthu osaopa Mulungu.”—2 Petulo 3:5-7.

Apa “tsiku laciweluzo ndi cionongeko” limene likubwela, aliyelekezela ndi kuonongeka kwa dziko m’masiku a Nowa. Kodi ndi dziko liti limene linaonongedwa? Dziko lathuli linapulumuka koma “anthu osaopa Mulungu,” adani ake, ndi amene anaphedwa. Pa “tsiku la ciweluzo” la Mulungu, onse amene si mabwenzi ake adzaphedwa. Koma mabwenzi a Mulungu adzapulumuka monga mmene Nowa ndi banja lake anapulumukila.—Mateyu 24:37-42.

Dziko lidzakhala losangalatsa pambuyo pakuti Mulungu waononga oipa onse. N’zoonekelatu kuti zimene Baibulo limanena zokhudza mapeto a dziko ndi nkhani yabwino. Koma mwina inu mungafunse kuti: Kodi Baibulo limanena nthawi pamene mapeto adzafika? Kodi mapeto ali pafupi? Nanga ndingapulumuke bwanji?