Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

1 Kodi Mulungu Ndiye Amabweletsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?

1 Kodi Mulungu Ndiye Amabweletsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?

Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho

Anthu ambili safuna kutumikila Mulungu cifukwa amamuimba mlandu wakuti iye ndiye amapangitsa mavuto.

Zofunika Kuganizila

Mwacindunji kapena mwa njila ina, atsogoleli acipembedzo ambili amaphunzitsa kuti Mulungu ndiye amapangitsa mavuto amene timakumana nawo. Mwacitsanzo, ena amakamba izi:

  • Matsoka a zacilengedwe ni cilango cocokela kwa Mulungu.

  • Ana amafa cifukwa cakuti Mulungu afuna angelo ambili kumwamba.

  • Mulungu amathandiza mbali imodzi pankhondo. Ndipo izi zimabweletsa mavuto aakulu.

Kodi sizotheka kuti zimene atsogoleli acipembedzo amaphunzitsa ponena za Mulungu n’zabodza? Kodi tingaŵakhulupililebe ngati Mulungu anaŵakana cifukwa ca zimene amaphunzitsa?

DZIŴANI ZAMBILI

Tambani vidiyo yakuti: N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibo? pa jw.org.

Zimene Baibo Imakamba

Mulungu si ndiye amapangitsa mavuto amene timakumana nawo.

Kucita zimenezi kungakhale kosagwilizana na makhalidwe ake amene Baibo imakamba. Mwacitsanzo:

“Njila zake zonse [Mulungu] ndi zolungama. . . . Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”DEUTERONOMO 32:4.

“Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono!”YOBU 34:10.

“Wamphamvuyonse sakhotetsa cilungamo.”YOBU 34:12.

Mulungu amakana zipembedzo zimene zimaphunzitsa zabodza zokhudza iye.

Izi ziphatikizapo zipembedzo zimene zimaphunzitsa kuti Mulungu ndiye amacititsa mavuto amene timakumana nawo, komanso amene amatengako mbali pankhondo na ciwawa.

“Aneneliwo akulosela monama m’dzina langa [Mulungu]. Ine sindinawatume, kuwalamula, kapena kulankhula nawo. Maulosi amene akukuuzaniwo anthu inu, ndiwo masomphenya onama, . . . ndi cinyengo ca mumtima mwawo.”YEREMIYA 14:14.

Yesu anadzudzula mkhalidwe wacinyengo wa zipembedzo.

“Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akucita cifunilo ca Atate wanga wakumwamba. Ambili adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosele m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kucita nchito zambili zamphamvu m’dzina lanunso?’ Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: ‘Sindikukudziwani ngakhale pang’ono! Cokani pamaso panga, anthu osamvela malamulo inu!’” MATEYU 7:21-23.