Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

2 Kodi Ife Eni Ndiye Timapangitsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?

2 Kodi Ife Eni Ndiye Timapangitsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?

Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho

Ngati yankho ni inde, ndiye kuti ungakhale udindo wathu kucepetsako mavuto.

Zofunika Kuganizila

Kodi anthu apangitsa mavuto otsatilawa kufika pa mlingo uti?

  • Nkhanza.

    Bungwe la World Health Organization (WHO) limakamba kuti pa anthu 4, mmodzi anacitilidwapo nkhanza ali mwana. Ndipo pa azimai atatu, mmodzi anamenyedwapo kapena kugonedwa mwacikakamizo, mwinanso zonse ziŵili pa nthawi ina mu umoyo wawo.

  • Cisoni Cobwela Cifukwa ca Imfa.

    Lipoti la mu 2018 lochedwa World Health Statistics lofalitsidwa na bungwe la World Health Organization linati “anthu pafupi-fupi 477,000 anaphedwa padziko lonse mu 2016.” Kuwonjezela apo, anthu pafupi-fupi 180,000 zioneka anaphedwa pa nkhondo zimene zinacitika mu caka cimeneco.

  • Matenda.

    M’nkhani yofalitsidwa m’magazini yakuti National Geographic, wolemba wina dzina lake Fran Smith anati: “Anthu oposa 1 biliyoni amakoka fodya, ndipo kaŵili-kaŵili fodya ndiye amabweletsa matenda akulu-akulu 5 akupha, monga matenda a mtima, sitroko, matenda otengela mu mphepo, matenda ovutika kupuma, komanso khansa ya kumapapo.”

  • Tsankho

    Jay Watts amene ni katswili wa zamaganizo anati: “Umphawi, kusiyana pa kapezedwe, kusankhana cifukwa cosiyana mitundu, cifukwa cokhala mkazi kapena mwamuna, kukakamizika kucoka kumalo kumene munthu amakhala, komanso mzimu wa mpikisano, zonsezi zimapangitsa anthu kuvutika maganizo kwambili.”

    DZIŴANI ZAMBILI

    Tambani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Mulungu Analenga Dziko Lapansi? pa jw.org

Zimene Baibo Imakamba

Mavuto ambili m’dzikoli amabwela cifukwa ca zocita za anthu.

Ambili mwa mavutowa amabwela cifukwa ca maboma opondeleza, ndipo izi zimapangitsa kuti umoyo ukhale wovuta kwa anthu amene maboma amenewo amati amaŵatumikila.

“Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.”MLALIKI 8:9.

Mavuto angacepetsedwe.

Mfundo za m’Baibo zimalimbikitsa anthu kukhala na thanzi labwino komanso kukhala pa mtendele na ena.

“Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu, koma nsanje imawoletsa mafupa.”MIYAMBO 14:30.

“Kuwawidwa mtima konse kwa njilu, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu acipongwe zicotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.” AEFESO 4:31.