Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

4 Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?

4 Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?

Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho

Yankho ya funso iyi ikhudza mmene timaonela moyo.

Zofunika Kuganizila

Kodi zingakhale zomveka kuti Mulungu amene analenga zinthu zokongola angalole kuti anthufe tizivutika?

Cifukwa ca mavuto, anthu osapembedza amayamba kukaikila zolinga za Mulungu, komanso zakuti iye aliko. Iwo amakhulupilila kuti mavuto amaonetsa kuti mwina (1) Mulungu alibe mphamvu zakuti awacotsepo, (2) Mulungu sasamala za ife kuti acotsepo mavuto, kapena (3)  Mulunguyo kulibe.

Kodi zifukwa zimenezi n’zoona?

DZIŴANI ZAMBILI

Tambani vidiyo yakuti, Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona? pa jw.org.

Zimene Baibo Imakamba

Mulungu sanatilenge kuti tizivutika ayi.

Iye amafuna kuti tizikondwela nawo moyo.

“Palibe cabwino kuposa kuti [anthu] asangalale ndiponso azicita zabwino pamene ali ndi moyo, komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, cifukwa coti wagwila nchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.”MLALIKI 3:12, 13.

Mulungu anapatsa anthu aŵili oyambilila zonse zofunikila kuti akhale na umoyo wabwino.

Iye sanafune kuti iwo kapena ana awo azivutika.

‘Mulungu anawauza kuti: Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.’ GENESIS 1:28.

Anthu aŵili oyambilila anasankha kupandukila Mulungu.

Zotulukapo zake n’zakuti iwo anadzibweletsela mavuto ambili kuphatikizapo ana awo onse.

“Monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.”AROMA 5:12. *

Mulungu sanatilenge na mphamvu zakuti tizidzilamulila tekha.

Sitinalengedwe kuti tizidzilamulila, monga mmene sitinalengedwele kuti tizikhala m’madzi.

“Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.”YEREMIYA 10:23.

Mulungu safuna kuti anthufe tizivutika.

Iye amafuna kuti tikhale na umoyo wopewa mavuto.

“Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje.”YESAYA 48:18.

^ ndime 17 M’Baibo, liwu lakuti “ucimo” limatanthauza zoipa zimene munthu angacite, komanso mkhalidwe umene anthu onse anatengela.