Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mavuto—Kodi Ni Cilango Cocokela Kwa Mulungu?

Mavuto—Kodi Ni Cilango Cocokela Kwa Mulungu?

LUZIA AMATSIMPHINA NA MWENDO WA KUMANZELE. Pamene anali mwana, anadwala matenda a poliyo. Matendawo amayambukila ena mofulumila, komanso amawononga mitsempha m’thupi la munthu. Atafika zaka 16, mzimayi wina amene anali kuseŵenzela anamuuza kuti, “Mulungu akukulanga na nthenda iyi cifukwa cosamvela amayi ako komanso khalidwe lako loipa.” Ngakhale kuti papita zaka, Luzia akali kukumbukila mmene anamvelela atauzidwa zimenezo.

PAMENE DAMARIS ANAYAMBA KUDWALA MATENDA A KHANSA YA KU UBONGO, atate ake anamufunsa kuti: “Kodi unalakwa ciani kuti izi zikucitikile? Uyenela kuti unacita cina cake coipa kwambili. N’cifukwa cake Mulungu akukulanga.” Damaris atamva zimenezi, anakwetemukilatu.

Kwa zaka zambili anthu akhala akukhulupilila kuti matenda ni cilango cocokela kwa Mulungu. Buku yakuti, Manners and Customs of Bible Lands imakamba kuti, “anthu ambili m’nthawi ya Khristu anali kukhulupilila kuti munthu anali kudwala kaamba ka chimo lake kapena la abululu ake, ndipo matendawo anali kutumizidwa monga cilango ca chimolo.” Buku yakuti, Medieval Medicine and the Plague imati, “anthu ena m’zaka za m’ma 500 C.E. mpaka 1500 C.E., anali kukhulupilila kuti Mulungu ndiye anatumiza milili m’zaka zimenezo kuti aŵalange cifukwa ca macimo awo.” Kodi Mulungu anali kupeleka ciweluzo kwa anthu oipa pamene mamiliyoni ku Europe anafa na mlili wa matenda ca m’ma 1300 C.E? Kapena kodi mlili umenewo unangobwela na tulombo toyambitsa matenda, monga mmene ofufuza za mankhwala amakambila? Koma ena angafunse kuti, kodi n’zoona kuti Mulungu amaseŵenzetsa matenda pofuna kulanga anthu kaamba ka macimo awo? *

GANIZILANI IZI: Ngati matenda na mavuto zinali cilango cocokela kwa Mulungu, n’cifukwa ciani Yesu, anacilitsa anthu odwala? Kodi zimenezo sizikanapeputsa ciweluzo ca Mulungu na cilungamo cake? (Mateyu 4:23, 24) Yesu sakanacita zinthu motsutsana na cifunilo ca Mulungu. Iye anati: “Ndimacita zinthu zomukondweletsa nthawi zonse,” ndipo “ndikucita izi kutsatila lamulo limene Atatewo anandipatsa.”—Yohane 8:29; 14:31.

Baibo imakamba momveka bwino kuti: Yehova Mulungu “sacita cosalungama.” (Deuteronomo 32:4) Mwacitsanzo, Mulungu sangapangitse ngozi ya ndeke, na kupha anthu ambili-mbili osalakwa, pofuna kulanga munthu wina wake m’ndekeyo! Mogwilizana na cilungamo ca Mulungu, Abulahamu mtumiki wokhulupilika anakamba kuti, Mulungu ‘sangawononge olungama pamodzi ndi oipa.’ Anati, ‘sangacite zimenezo.’ (Genesis 18:23, 25) Baibo imakambanso kuti, “Mulungu sacita zoipa,” ndipo iye “sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.”—Yobu 34:10-12.

ZIMENE BAIBO IMATIPHUNZITSA PA NKHANI YA MAVUTO

Mavuto amene timakumana nawo si cilango cocokela kwa Mulungu pa chimo lina lake. Yesu anafotokoza momveka bwino nkhani imeneyi, pamene iye na ophunzila ake anaona munthu amene anali wakhungu cibadwile. “Ophunzila ake anamufunsa kuti: ‘Rabi, anacimwa ndani kuti munthu uyu abadwe wakhungu conci? Ndi iyeyu kapena makolo ake?’ Yesu anayankha kuti: ‘Munthuyu kapena makolo ake, onsewa palibe amene anacimwa. Izi zinacitika kuti nchito za Mulungu zionekele kudzela mwa iye.’”—Yohane 9:1-3.

Popeza kuti ambili panthawiyo anali na maganizo olakwika pa nkhaniyi, ophunzila a Yesu ayenela kuti anadabwa pamene iye anawauza kuti munthuyo, kapena makolo ake, sanalakwe ciliconse kuti iye abadwe wakhungu. Yesu sanacilitse cabe munthu wakhungu, koma anathetsanso cikhulupililo cabodza cakuti mavuto ni cilango cocokela kwa Mulungu. (Yohane 9:6, 7) Anthu amene amadwala matenda aakulu masiku ano, angalimbikitsidwe kudziŵa kuti si Mulungu amene amapangitsa kuti iwo adwale.

N’cifukwa ciani Yesu anacilitsa anthu odwala, ngati Mulungu anali kuwalanga pa zolakwa zawo?

Malemba amatitsimikizila kuti

  • “Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (YAKOBO 1:13) Inde, “zinthu zoipa” zimene zavutitsa anthu kwa zaka zambili, monga matenda, zoŵaŵa, na imfa, posacedwa zidzacotsedwapo.

  • “Onse amene sanali kumva bwino m’thupi [Yesu Khristu] anawacilitsa.” (MATEYU 8:16) Mwa kucilitsa onse amene anabwela kwa iye, Mwana wa Mulungu anaonetsa zimene Ufumu wa Mulungu udzacita padziko lonse.

  • “Iye [Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”CHIVUMBULUTSO 21:3-5.

KODI N’NDANI AMABWELETSA MAVUTO?

Nanga n’cifukwa ciani anthu amakumana na mavuto ambili-mbili conco? Kwa zaka zambili, anthu akhala akufunsa funso limeneli. Ngati Mulungu si ndiye amabweletsa mavuto, nanga n’ndani amawapangitsa? Tidzapeza mayankho pa mafunso amenewa m’nkhani yokonkhapo.

^ Ngakhale kuti nthawi zina kumbuyoku Mulungu anali kulanga anthu cifukwa ca macimo awo, Baibo sionetsa kuti masiku ano Yehova amaseŵenzetsa matenda kapena masoka a zacilengedwe pofuna kulanga anthu pa macimo awo.