Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zimene Ena Amakhulupilila

Zimene Ena Amakhulupilila

Ahindu

amaona kuti mavuto, ni zotulukapo za zimene munthu anacita kumbuyoku mu umoyo uno, kapena mu wina asanamwalile na kubadwanso. Munthu angamasuke kuleka kufa na kubadwanso mobweleza-bweleza, akafika pa mkhalidwe wochedwa moksha. Ndipo angafike pa mkhalidwewu mwa kuleka kuganizila zinthu zakuthupi.

Asilamu

amaona kuti mavuto ni cilango pa macimo komanso mayeso oyesa cikhulupililo. Dr. Sayyid Syeed pulezidenti wa bungwe lacisilamu lochedwa Islamic Society of North America anakamba kuti matsoka ni cikumbutso cabe cakuti “tifunika kukhalabe oyamikila kwa Mulungu pamadalitso athu onse amene tili nawo, komanso kuti tifunika kuthandiza anthu ofunikila thandizo.”

Ayuda

amakhulupilila kuti mavuto amene munthu angakumane nawo ni zotulukapo za zocita zake. Ayuda ena amakhulupilila kuti akufa adzauka, ndipo pambuyo pake anthu amene anacitilidwa zosalungama adzacitilidwa cilungamo. Ayuda okhulupilila zamizimu amaphunzitsa kuti munthu akafa amabakadwanso, ndipo izi zimapeleka mipata yakuti munthuyo alipilile zolakwa zimene anacita asanamwalile, mwa kukumana na mavuto.

Abuda

nawonso amakhulupilila kuti munthu amapitiliza kukumana na mavuto maulendo ambili-mbili, cifukwa cakuti amabadwanso na kufa mobweleza-bweleza, ndipo munthuyo amamasuka ku mavutowo akaleka kucita zinthu zoipa, kuziganizila komanso kuzilaka-laka. Mwa kukhala wanzelu, kucita nchito zabwino, komanso kudziletsa, munthu angafike pa mkhalidwe wochedwa Nirvana. Ndipo akafika pamenepo, mavuto onse a munthuyo amatha.

Akomfyushasi

amakhulupilila kuti mavuto ambili amabwela cifukwa ca “kulephela kwa anthu komanso kulakwitsa zinthu,” linatelo buku lochedwa A Dictionary of Comparative Religion. Cipembedzoci cimati ngakhale kuti mavuto angacepe mwa kucita zabwino mu umoyo, mavuto ambili amabwela cifukwa ca “zolengedwa za mizimu zimene n’zamphamvu kuposa anthu. Conco, munthu amafunika cabe kuvomeleza zimene mizimuyo yasankha kucita.”

Zipembedzo Zina Zamiyambo

zimakhulupilila kuti mavuto amabwela cifukwa ca mfiti. Malinga na zikhulupililozi, mfiti zingabweletse mwayi kapena matsoka, ndipo mavuto amene mfitizo zingabweletse angacepetsedwe mwa kucita miyambo yosiyana-siyana ya zamatsenga. Conco, amakhulupilila kuti miyambo na mankhwala opatsidwa na ng’anga angalimbane na nchito za mfiti munthu akadwala.

Akhristu

amakhulupilila kuti mavuto anayamba cifukwa ca ucimo wa anthu aŵili oyamba, malinga na mmene buku la m’Baibo la Genesis limafotokozela. Komabe, machechi ambili aloŵetsapo maganizo awo pa ciphunzitso cimeneci. Mwacitsanzo, Akatolika ena amakamba kuti munthu angalolele kukumana na mavuto, n’colinga cakuti kuvutikako kukhale monga ‘nsembe kwa Mulungu,’ yom’pempha kuti adalitse mpingo kapena kuti wina wake alandile cipulumutso.

DZIŴANI ZAMBILI

Tambani vidiyo yakuti Kodi Mulungu Amavomeleza Kulambila Konse? pa jw.org.