Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

3 N’cifukwa Ciani Anthu Abwino Nawonso Amavutika?

3 N’cifukwa Ciani Anthu Abwino Nawonso Amavutika?

Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho

Zimaoneka zopanda cilungamo kuti anthu abwino nawonso azivutika. Izi zimaonetsa kuti kukhala munthu wabwino kulibe phindu kweni-kweni.

Zofunika Kuganizila

Ena amakhulupilila kuti anthu amafa na kubadwanso mobweleza-bweleza. Amakamba kuti aja amene anali kucita zabwino amabadwanso mu umoyo wabwino, ndipo amene anali kucita zoipa amabadwanso mu umoyo wovutika kwambili. Malinga na cikhulupililo cimeneci, ngakhale munthu amene akucita zabwino angavutike ngati anacita zinthu zoipa “asanamwalile kumbuyoku.” Komabe . . .

  • Kodi kuvutika kumeneko kungakwanilitse colinga canji, ngati munthu amene wabadwanso sakumbukila zimene anali kucita asanamwalile?

  • N’cifukwa ciani timayesetsa kukhala na thanzi labwino, komanso kupewa ngozi ngati kukhala na umoyo wabwino kumadalila pa zimene tinacita tisanamwalile?

    DZIŴANI ZAMBILI

    Tambani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika? pa jw.org.

Zimene Baibo Imakamba

Mavuto si cilango cocokela kwa Mulungu ayi.

Mavuto ambili amacitika mosayembekezeleka, ndipo kaŵili-kaŵili munthu angapezeke m’ngozi mwatsoka cabe.

“Anthu othamanga kwambili sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo, anzelu sapeza cakudya, omvetsa zinthu nawonso sapeza cuma, ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, cifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimagwela onsewo.” MLALIKI 9:11.

Cina cimene cimapangitsa kuti tizivutika ni ucimo umene timabadwa nawo.

Nthawi zambili anthu amaseŵenzetsa mawu akuti “ucimo” pokamba za zinthu zoipa zimene munthu anacita. Koma Baibo imaseŵenzetsa mawuwa ponena za mkhalidwe umene anthu onse abwino komanso oipa amabadwa nawo.

“Anandilandila mu zowawa za pobeleka ndili wocimwa. Ndipo ndine wocimwa kucokela pamene mayi anga anatenga pakati panga.”SALIMO 51:5.

Ucimo wakhala na zotulukapo zowononga kwambili pa anthu.

Ucimo unawononga ubale wathu na Mlengi, komanso unapangitsa mgwilizano wathu na zolengedwa zonse za Mulungu kusokonezeka. Izi zabweletsa mavuto osaneneka kwa munthu aliyense payekha, komanso ku mtundu wonse wa anthu.

“Pamene ndikufuna kucita cinthu cabwino, coipa cimakhala cili ndi ine.”AROMA 7:21.

“Cilengedwe conse cikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.”AROMA 8:22.