Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Salimo 46:10​—“Khalani Chete, Ndipo Dziwani Kuti Ine Ndine Mulungu”

Salimo 46:10​—“Khalani Chete, Ndipo Dziwani Kuti Ine Ndine Mulungu”

 “Gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu. Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu, ndidzakwezedwa padziko lapansi.”​—Salimo 46:10, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.”​—Salimo 46:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Salimo 46:10

 Mulungu akulimbikitsa anthu onse kuti azimulambira komanso kuvomereza kuti iye ndi woyenera kulamulira dziko lonse lapansi. Munthu aliyense amene akufuna kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale ayenera kuvomereza mfundo yosatsutsika yakuti iye ali ndi mphamvu zolamulira.​—Chivumbulutso 4:11.

 “Gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu.” M’Mabaibulo ena, mawu akuti “gonjerani” anawamasulira kuti “khalani chete.” Zimenezi zachititsa kuti anthu ena aziganiza kuti limeneli ndi lamulo lakuti azichita zinthu mwamantha kapena azikhala chete m’tchalitchi. Komabe, mawu a Chiheberi omwe anamasuliridwa kuti “gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu” ndi pempho lomwe Yehova a Mulungu akuuza anthu amitundu yonse kuti asiye kumutsutsa ndipo azindikire kuti ayenera kulambira iye yekha basi.

 Pempho lofanana ndi limeneli limapezeka pa Salimo 2. Palembali, Mulungu akulonjeza kuti adzawononga anthu onse amene amamutsutsa. Koma anthu amene amazindikira kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira amamudalira kuti aziwatsogolera, aziwapatsa mphamvu komanso nzeru. Anthu oterewa akakhala pamavuto, amakhala osangalala komanso otetezeka chifukwa “amathawira kwa Iye.”​—Salimo 2:9-12.

 “Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu, ndidzakwezedwa padziko lapansi.” M’mbuyomu, Yehova Mulungu ankakwezedwa akagwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu poteteza anthu ake. (Ekisodo 15:1-3) M’tsogolomu, Yehova adzakwezedwa kwambiri pamene aliyense padzikoli azidzagonjera ulamuliro wake komanso kumulambira.​—Salimo 86:9, 10; Yesaya 2:11.

Nkhani yonse ya pa Salimo 46:10

 Buku lina limanena kuti Salimo 46 ndi “nyimbo yotamanda Mulungu chifukwa cha mphamvu zake populumutsa anthu ake.” Pamene anthu a Mulungu ankaimba Salimo 46, ankasonyeza kuti amadalira Yehova kuti ali ndi mphamvu zowateteza ndiponso kuwathandiza. (Salimo 46:1, 2) Mawu amenewa ankawakumbutsa kuti Yehova ankakhala nawo nthawi zonse.​—Salimo 46:7, 11.

 Salimoli linalimbikitsa anthu a Mulungu kuti azikhulupirira kwambiri mphamvu zake zodabwitsa n’kumaona kuti ali ndi mphamvu zowateteza. (Salimo 46:8) Mfundo yake yaikulu ndi yakuti iye ali ndi mphamvu zothetseratu nkhondo. Ndipotu, m’mbuyomu Yehova anachitapo kale zimenezi pothetsa nkhondo komanso kuteteza anthu ake kwa adani awo. Komabe, Baibulo likulonjeza kuti posachedwapa, Mulungu adzasonyeza mphamvu zake zazikulu pothetsa nkhondo padziko lonse lapansi.​—Yesaya 2:4.

 Kodi Yehova akupitiriza kuthandiza atumiki ake masiku ano? Inde. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti akhale olimba mtima n’kumadalira Yehova kuti aziwathandiza. (Aheberi 13:6) Mfundo za mu Salimo 46 zimatilimbikitsa kuti tizikhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zotiteteza. Zimatithandizanso kuona kuti Mulungu “ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu.”​—Salimo 46:1.

 Onerani vidiyo yachidule kuti muone mfundo zokuthandizani kumvetsa buku la Masalimo.

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?