Pitani ku nkhani yake

Kodi Chipembedzo, Mulungu Kapena Baibulo Zingandithandize Kuti Ndikhale Wosangalala?

Kodi Chipembedzo, Mulungu Kapena Baibulo Zingandithandize Kuti Ndikhale Wosangalala?

Yankho la m’Baibulo

 Inde. Baibulo ndi buku lakale kwambiri lokhala ndi malangizo anzeru. Mungapezemo mayankho a mafunso amene angakuthandizeni kuti muzisangalala ndi moyo. Taonani mafunso ena amene Baibulo lingayankhe.

  1.   Kodi Mlengi alipodi? Baibulo limati Mulungu ‘analenga zinthu zonse.’ (Chivumbulutso 4:11) Popeza Mulungu ndi amene anatilenga, amadziwa zimene timafunika kuti tizikhala osangalala.

  2.   Kodi Mulungu amandikonda? Anthu ena amaganiza kuti Mulungu saganizira anthu, koma Baibulo limati: “Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Iye amachita chidwi ndi zimene zikukuchitikirani ndipo amafuna kukuthandizani kuti zinthu zizikuyenderani bwino.​—Yesaya 48:​17, 18; 1 Petulo 5:7.

  3.   Kodi kudziwa Mulungu kungandithandize bwanji kuti ndizisangalala? Potilenga, Mulungu anatipatsa mtima wofuna kumvetsa cholinga cha moyo. (Mateyu 5:3) Mtima umenewu umatichititsanso kufuna kudziwa bwino Mlengi wathu ndiponso kukhala naye pa ubwenzi. Mukamayesetsa kuti mukhale pa ubwenzi ndi Mulungu, iye amakuthandizani kuti zitheke. Baibulo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”​—Yakobo 4:8.

 Anthu ambirimbiri aona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu kwawathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino pa moyo n’kumasangalala. Sikuti mukadziwa Mulungu mudzakhala ndi moyo wopanda mavuto koma nzeru zake zimene zili m’Baibulo zingakuthandizeni kuti:

Zipembedzo zambiri zimene zimagwiritsa ntchito Baibulo sizitsatira mfundo zake. Mosiyana ndi zimenezi, chipembedzo choona, chimene chimatsatira mfundo zoona za m’Baibulo, chidzakuthandizani kuti mudziwe Mulungu.