Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda?

Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda?

Yankho la m’Baibulo

 Inde. Mulungu amaganizira atumiki ake amene akudwala. Ponena za mtumiki wa Mulungu wokhulupirika, Baibulo limati: ‘Yehova adzamuchirikiza pamene akudwala pabedi lake.’ (Salimo 41:3) Ngati mukudwala matenda enaake, mfundo zitatu zotsatirazi zingakuthandizeni kupirira.

  1.   Muzipempha Mulungu kuti akupatseni mphamvu. Mulungu angakupatseni ‘mtendere wake umene umaposa kuganiza mozama kulikonse,’ womwe ungakuthandizeni kuti mupirire komanso kuti musamade nkhawa kwambiri.​—Afilipi 4:​6, 7.

  2.   Muziyesetsa kukhala wosangalala. Baibulo limati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.” (Miyambo 17:22) Muziyesetsa kuseka kapena kuchita tinthabwala chifukwa zimenezi zimathandiza kuti muziiwalako mavuto. Izi zingathandizenso kuti musamavutike kwambiri ndi matendawo.

  3.   Muzikhulupirira zimene Mulungu walonjeza. Mukamayembekezera zinthu zabwino mukhoza kukhala osangalala ngakhale kuti mukuvutika ndi matenda. (Aroma 12:12) Baibulo limatiuza kuti m’tsogolomu, palibe munthu amene “adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Pa nthawiyo, Mulungu adzathetsa matenda onse, ngakhale amene anthu akulephera kuwachiza masiku ano. Mwachitsanzo, Baibulo limanena zimene Mulungu adzachite pothetsa ukalamba. Limati: “Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.”​—Yobu 33:25.

 Dziwani izi: A Mboni za Yehova amadziwa kuti Mulungu amathandiza anthu amene akudwala koma nawonso amalandira chithandizo chamankhwala akadwala. (Maliko 2:17) Sitilimbikitsa anthu kulandira chithandizo chinachake chifukwa munthu aliyense ayenera kusankha yekha chithandizo chimene akufuna.