Pitani ku nkhani yake

Kodi Angelo Ndi Otani?

Kodi Angelo Ndi Otani?

Yankho la m’Baibulo

 Angelo ndi zolengedwa zomwe zili ndi mphamvu kwambiri komanso amachita zinthu kuposa anthu. (2 Petulo 2:11) Angelo amakhala kumwamba, kumalo omwe kumakhala zolengedwa zauzimu, komwe n’kutali kwambiri kuposa komwe tingathe kuona ndi maso. (1 Mafumu 8:27; Yohane 6:38) N’chifukwa chake angelo amatchedwanso kuti mizimu.—1 Mafumu 22:21; Salimo 18:10.

Kodi angelo anachokera kuti?

 Mulungu analenga angelo pogwiritsa ntchito Yesu yemwe Baibulo limamutcha kuti “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” Pofotokoza mmene Mulungu anagwiritsira ntchito Yesu polenga zinthu, Baibulo limati: “Kudzera mwa [Yesu] zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka,” kuphatikizapo angelo. (Akolose 1:13-17) Angelo sakwatira kapena kuberekana. (Maliko 12:25) M’malo mwake, aliyense wa “ana a Mulungu woona” amenewa analengedwa mwachindunji.—Yobu 1:6.

 Angelo analengedwa kalekale kwambiri, dziko lapansi lisanalengedwe. Mulungu atalenga dziko lapansi, angelo “anayamba kufuula ndi chisangalalo.”—Yobu 38:4-7.

Kodi angelo alipo angati?

 Baibulo silitchula chiwerengero chenicheni cha angelo, koma limasonyeza kuti alipo ochuluka kwambiri. Mwachitsanzo, mtumwi Yohane anaona mamiliyoni ambiri a angelo m’masomphenya.—Chivumbulutso 5:11.

Kodi angelo ali ndi mayina komanso makhalidwe osiyanasiyana?

 Inde. Baibulo limatchula mayina awiri a angelo: Mikayeli komanso Gabirieli. (Danieli 12:1; Luka 1:26) a Angelo enanso anavomereza kuti anali ndi mayina koma sanafune kuwatchula.—Genesis 32:29; Oweruza 13:17, 18.

 Angelo ndi osiyanasiyana ndipo amatha kulankhulana. (1 Akorinto 13:1) Amatha kuganiza komanso kupanga mawu otamanda Mulungu. (Luka 2:13, 14) Ndipo ali ndi ufulu wotha kusankha pakati pa chabwino ndi cholakwika, monga mmene zinalili pamene angelo ena anachimwa n’kupandukira Mulungu limodzi ndi Satana Mdyerekezi.—Mateyu 25:41; 2 Petulo 2:4.

Kodi pali magulu osiyanasiyana a angelo?

 Inde. Mikayeli, yemwe ndi mkulu wa angelo, ndi amene ali ndi ulamuliro komanso mphamvu zambiri. (Yuda 9; Chivumbulutso 12:7) Aserafi ndi angelo apamwamba kwambiri omwe amakhala pafupi ndi mpando wachifumu wa Yehova. (Yesaya 6:2, 6) Akerubi ndi gulu linanso la angelo apamwamba omwe amagwira ntchito zapadera. Mwachitsanzo, akerubi ndi amene ankalondera khomo lolowera m’munda wa Edeni panthawi imene Adamu ndi Hava anathamangitsidwa m’mundawo.—Genesis 3:23, 24.

Kodi angelo amathandiza anthu?

 Inde, Mulungu amagwiritsa ntchito angelo ake okhulupirika pothandiza anthu masiku ano.

  •   Mulungu amagwiritsa ntchito angelo potsogolera atumiki ake pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 14:6, 7) Zimenezi zimathandiza anthu amene akulalikirawo komanso amene akumvetsera uthenga wabwino.—Machitidwe 8:26, 27.

  •   Angelo amathandiza kuti mpingo wa Chikhristu ukhale wosadetsedwa ndi anthu oipa.—Mateyu 13:49.

  •   Angelo amatsogolera komanso kuteteza anthu amene ndi okhulupirika kwa Mulungu.—Salimo 34:7; 91:10, 11; Aheberi 1:7, 14.

  •   Posachedwapa, angelo adzamenya nkhondo limodzi ndi Yesu yochotsa anthu onse oipa ndipo zimenezi zidzathandiza kuti anthu azisangalala.—2 Atesalonika 1:6-8.

Kodi munthu aliyense ali ndi mngelo amene amamuteteza?

 Ngakhale kuti angelo amachita chidwi ndi zinthu zauzimu zimene atumiki a Mulungu akuchita, zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu amapereka mngelo kwa Mkhristu aliyense n’cholinga choti azimuteteza. b (Mateyu 18:10) Angelo sateteza atumiki a Mulungu ku mavuto kapena mayesero onse. Baibulo limasonyeza kuti nthawi zambiri Mulungu ‘amapereka njira yopulumukira’ ku mayeserowo popatsa munthu nzeru komanso mphamvu kuti athe kupirira.—1 Akorinto 10:12, 13; Yakobo 1:2-5.

Maganizo olakwika okhudza angelo

 Maganizo olakwika: Angelo onse ndi abwino.

 Zoona zake: Baibulo limanena za “makamu a mizimu yoipa” komanso “angelo amene anachimwa.” (Aefeso 6:12; 2 Petulo 2:4) Angelo oipawa ndi ziwanda zomwe zinakhala kumbali ya Satana n’kupandukira Mulungu.

 Maganizo olakwika: Angelo safa.

 Zoona zake: Angelo oipa, kuphatikizapo Satana Mdyerekezi, adzawonongedwa.—Yuda 6.

 Maganizo olakwika: Anthu akafa amasanduka angelo.

 Zoona zake: Angelo ndi zolengedwa zapadera za Mulungu, osati anthu amene afa kenako n’kuukitsidwa. (Akolose 1:16) Anthu amene aukitsidwa kuti akakhale ndi moyo kumwamba, Mulungu amawapatsa mphatso ya moyo womwe sungafe. (1 Akorinto 15:53, 54) Iwo adzakhala ndi malo apamwamba kuposa angelo.—1 Akorinto 6:3.

 Maganizo olakwika: Angelo analengedwa kuti azitumikira anthu.

 Zoona zake: Angelo amatsatira malamulo a Mulungu, osati athu. (Salimo 103:20, 21) Ngakhale Yesu pa nthawi ina ananena kuti akanatha kupempha thandizo kwa Mulungu, osati kwa angelo.—Mateyu 26:53.

 Maganizo olakwika: Tingathe kupemphera kwa angelo kuti atithandize.

 Zoona zake: Kupemphera ndi mbali ya kulambira kwathu, ndipo tiyenera kulambira Yehova Mulungu basi. (Chivumbulutso 19:10) Tiyenera kupemphera kwa Mulungu yekha, kudzera mwa Yesu.—Yohane 14:6.

a Pa Yesaya 14:12, ma Baibulo ena amagwiritsa ntchito mawu oti “Lusifala” omwe anthu ena amati ndi dzina la mngelo yemwe anakhala Satana Mdyerekezi. Komabe, mawu a Chiheberi oyambirira omwe anagwiritsidwa ntchito palembali amatanthauza kuti ‘wonyezimira.’ Nkhaniyi sikusonyeza kuti mawuwa akunena za Satana, koma akunena za mzera wa mafumu a Babulo, omwe Mulungu anali kudzawachititsa manyazi chifukwa cha kunyada kwawo. (Yesaya 14:4, 13-20) Mawu oti “wonyezimirawe” anawagwiritsa ntchito panthawi imene mafumu a Babulo anachotsedwa paudindo, posonyeza kuti anali opusa.

b Anthu ena amaganiza kuti nkhani yofotokoza za kutulutsidwa m’ndende kwa Petulo ikutanthauza kuti Petulo anali ndi mngelo wake womuteteza. (Machitidwe 12:6-16) Komabe, pamene ophunzirawo ananena kuti “mngelo [wa Petulo]”, n’kutheka kuti anaganiza molakwika kuti mngelo yemwe anali mthenga woimira Petulo wabwera, osati Petulo weniweniyo.