Pitani ku nkhani yake

Kodi Ziwanda Zilipodi?

Kodi Ziwanda Zilipodi?

Yankho la m’Baibulo

 Inde zilipodi. Ziwanda ndi “angelo amene anachimwa,” ndipo anaukira Mulungu. (2 Petulo 2:4) Mngelo woyambirira amene anakhala chiwanda ndi Satana Mdyerekezi ndipo Baibulo limamutchula kuti “wolamulira ziwanda.”—Mateyu 12:24, 26.

Angelo amene sanamvere m’nthawi ya Nowa

 Baibulo limanena za angelo amene sanamvere Mulungu Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chisanachitike. Limanena kuti: “Ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.” (Genesis 6:2) Angelo oipawo “anasiya malo awo okhala” kumwamba n’kuvala matupi aumunthu n’cholinga choti achite chiwerewere ndi akazi.—Yuda 6.

 Chigumula chitayamba, angelo oipawo anavula matupi aumunthu aja n’kuthawira kumwamba. Komabe Mulungu sanawalole kuti akhalenso m’gulu la angelo ake. Zitatero angelowa sanathenso kuvala matupi a anthu ndipo chimenechi chinali chilango chawo.—Aefeso 6:11, 12.