Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zida za nkhondo: Anton Petrus/Moment via Getty Images; money: Wara1982/iStock via Getty Images Plus

KHALANI MASO

Ndalama Zambirimbiri Zikuthera Kunkhondo—Kodi Ndi Ndalama Zochuluka Bwanji?

Ndalama Zambirimbiri Zikuthera Kunkhondo—Kodi Ndi Ndalama Zochuluka Bwanji?

 Nkhondo zimawonongetsa ndalama zosaneneka.

  •   “Chaka chatha, mayiko anawononga madola okwana 2.2 thililiyoni pa nkhondo zosiyanasiyana. Ndalamazi ndi zambiri zedi kuposa zomwe akhala akuwonongera pa nkhondo zomwe zinachitikapo m’mbuyomu.”—The Washington Post, February 13, 2024.

 Komatu si ndalama zokha, palinso zinthu zina zomwe zawonongeka chifukwa cha nkhondozi. Mwachitsanzo, tione za nkhondo ya ku Ukraine.

  •   Asilikali. Kafukufuku wina akusonyeza kuti asilikali pafupifupi 500,000 anaphedwa kapenanso kuvulala kungochokera pamene nkhondoyi inayamba zaka ziwiri zapitazo.

  •   Anthu wamba. Malinga ndi bungwe la United Nations, anthu oposa 28,000 anafa kapena kuvulala. Komabe, mkulu wina wa bungwe la United Nations anati: “Ndi zovuta kudziwa chiwerengero chonse cha anthu wamba omwe akhudzidwa ndi nkhondoyi.” a

 Pali anthu ambirimbiri omwe akuvutika chifukwa cha nkhondo komanso kusamvana komwe kukuchitika padziko lonse.

  •   Anthu 114 miliyoni anathawa kwawo chifukwa cha nkhondo komanso zachiwawa padziko lonse kuyambira mu September 2023.

  •   Anthu 783 miliyoni alibe chakudya chokwanira. Bungwe Loona za Chakudya Padziko Lonse linati: “Nkhondo ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zimayambitsa vuto la kusowa kwa chakudya. Ndipo anthu 70 pa 100 aliwonse omwe akuvutika ndi njala padziko lonse, amakhala m’madera omwe kukuchitika nkhondo komanso zachiwawa.”

 Kodi nkhondo zidzatha? Kodi palidi chiyembekezo choti padzikoli padzakhala mtendere? Kodi idzafika nthawi pamene anthu onse sadzavutikanso ndi umphawi ndipo aliyense adzakhala ndi zinthu zokwanira kuphatikizapo chakudya? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

Nthawi ya nkhondo

 Baibulo linalosera kuti kudzakhala nkhondo m’madera osiyanasiyana ndipo linafotokoza za nkhondozi mophiphiritsira kuti wokwera pahatchi.

  •   Linanena kuti: “Panatuluka hatchi ina yofiira ngati moto. Amene anakwera pahatchi imeneyi analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi, kuti anthu aphane ndipo anapatsidwa lupanga lalikulu.”—Chivumbulutso 6:4.

 Wokwera pahatchi ameneyo akutsatiridwa ndi enanso awiri omwe akuimira njala ndi imfa chifukwa cha miliri ndi zinthu zina. (Chivumbulutso 6:5-8) Kuti mudziwe zambiri zokhudza ulosi wa m’Baibulo umenewu ndiponso chifukwa chake tingakhulupirire kuti ukukwaniritsidwa m’nthawi yathu ino, werengani nkhani yakuti, “Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?

Tsogolo la Mtendere

 Posachedwapa, sikudzakhalanso kusakaza chuma chifukwa cha nkhondo. Koma si anthu amene adzachite zimenezi. Baibulo limati:

  •   Mulungu “akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi.”—Salimo 46:9.

  •   Mulungu adzachotsa zinthu zonse zoipa zimene zimabwera chifukwa cha nkhondo. “Iye adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

  •   Mulungu adzaonetsetsa kuti aliyense padzikoli akukhala mwamtendere mpaka kalekale. “Anthu anga adzakhala pamalo amtendere, Adzakhala pamalo otetezeka komanso pamalo abata ndi ampumulo.”—Yesaya 32:18.

 Malinga ndi ulosi wina wa m’Baibulo, nkhondo ndi zinthu zina zoipa zimene timaona masiku ano ndi chizindikiro chakuti nthawi ya mtendere ili pafupi.

 Kodi Mulungu adzabweretsa bwanji mtendere? Adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito boma lake la kumwamba kapena kuti Ufumu. (Mateyu 6:10) Kuti mudziwe zokhudza Ufumuwu komanso zomwe udzakuchitireni, onerani vidiyo yaifupi iyi yakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

a Miroslav Jenca, wothandiza mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations ku Europe, December 6, 2023.