Pitani ku nkhani yake

Kodi Zidzatheka Bwanji Kuti Padziko Lonse Lapansi Padzakhale Mtendere?

Kodi Zidzatheka Bwanji Kuti Padziko Lonse Lapansi Padzakhale Mtendere?

Yankho la m’Baibulo

 Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma la kumwamba lolamuliridwa ndi Khristu Yesu, ndi womwe udzabweretse mtendere padziko lonse, osati anthu. Taonani zomwe Baibulo limaphunzitsa pa nkhani yosangalatsayi.

  1.   Mulungu ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’ Iye adzachita zimenezi pokwaniritsa lonjezo lake lakuti “pansi pano [padzakhala] mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.”—Salimo 46:9; Luka 2:14.

  2.   Ufumu wa Mulungu, womwe uli kumwamba, udzalamulira dziko lonse lapansili. (Danieli 7:14) Popeza Ufumuwu udzakhala boma lokhalo padziko lonse lapansi, udzathetsa kusankhana chifukwa chosiyana mitundu ndi mayiko, ndipo limeneli ndi vuto lalikulu limene limayambitsa nkhondo.

  3.   Yesu, yemwe ndi Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu, amatchedwa “Kalonga wa Mtendere,” ndipo adzaonetsetsa kuti ‘mtendere usadzathe.’—Yesaya 9:6, 7.

  4.   Anthu omwe amakonda nkhondo sadzaloledwa kukhala nawo mu Ufumu umenewu chifukwa “Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”—Salimo 11:5; Miyambo 2:22.

  5.   Mulungu akuthandiza anthu omwe ndi nzika za Ufumu wake kuti aphunzire kukhala mwamtendere. Pofotokoza zomwe zidzachitike pambuyo poti anthuwo aphunzitsidwa, Baibulo limati: “Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:3, 4.

 Panopa, anthu mamiliyoni ambiri a Mboni za Yehova akuphunzitsidwa ndi Mulungu mmene angakhalire mwamtendere ndi ena. (Mateyu 5:9) Ngakhale kuti ndife anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana komanso m’mayiko oposa 230, sititenga zida n’kumamenyana ndi ena.

Anthu a Mboni za Yehova akuphunzira njira zimene zingawathandize kukhala mwamtendere ndi ena masiku ano