Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zomwe Baibulo Limanena pa Nkhani Yakusintha Kwa Nyengo Komanso Tsogolo Lathu

Zomwe Baibulo Limanena pa Nkhani Yakusintha Kwa Nyengo Komanso Tsogolo Lathu

 Nyuzipepala ina inanena kuti: “Nkhani yakusintha kwa nyengo yakhala vuto lalikulu kwambiri. Tsopano dziko lapansi ndi malo ovuta kukhalapo.”​—The Guardian.

 Anthu akukumana ndi mavuto aakulu omwe anawayambitsa okha. Asayansi ambiri akuvomereza kuti zochita za anthu ndi zomwe zachititsa kuti padzikoli pazitentha kwambiri. Kutenthaku kwachititsa kuti nyengo isinthe ndipo zotsatirapo zake zakhala zowononga kwambiri monga:

  •   Kutentha kwambiri, chilala komanso mphepo zamkuntho zomwe zikuchititsa kusefukira kwa madzi komanso moto wolusa. Ndipo zimenezi zikumachitika pafupipafupi komanso mwamphamvu kwambiri.

  •   Kusungunuka kwa ayezi m’madera ozizira kwambiri

  •   Kukwera kwa madzi am’nyanja

 Mavuto akusintha kwa nyengo, akhudza madera onse padzikoli. Pambuyo pochita kafukufuku m’mayiko 193, nyuzipepala ina inati: “Zili ngati kuti dzikoli likufuula kuti anthu alithandize.” Chifukwa choti kusintha kwa nyengo kwachititsa kuti anthu ena akhale pa mavuto komanso kufa, Bungwe Loona za Umoyo wa Anthu Padziko Lonse linati: “limeneli ndi vuto lalikulu kwambiri ku moyo wa anthu.”

 Ngakhale zili choncho, tili ndi chifukwa chomveka chotichititsa kuyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Baibulo linaneneratu za zinthu zomwe zikuchitika masiku ano komanso chifukwa chake tiyenera kuyembekezera kuti Mulungu adzachotsa zoipa zonse zomwe zikuchitikazi. Baibulo limatithandizanso kudziwa zomwe Mulungu adzachite kuti anthufe tikhale ndi tsogolo labwino.

Kodi kusintha kwa nyengo kukukwaniritsa maulosi a m’Baibulo?

 Inde. Mavuto a kusintha kwa nyengo omwe abwera chifukwa choti kunjaku kukutentha kwambiri masiku ano, akugwirizana ndi zomwe Baibulo linaneneratu.

 Ulosi: Mulungu ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’​—Chivumbulutso 11:18.

 Baibulo linaneneratu za nthawi imene anthu adzachita zinthu zomwe zidzachititse kuti chilengedwe chiwonongeke. Chifukwa cha kutentha kwambiri komwe kukuchitika padzikoli, anthu akuwononga kwambiri zachilengedwe kuposa m’mbuyo monsemu.

 Ulosiwu ukusonyeza chifukwa chimodzi chomwe chikutichititsa kuti tisamayembekezere kuti anthu adzabwezeretsa chilengedwechi mwakale. Tiyenera kudziwa kuti pa nthawi imene anthu “akuwononga dziko lapansi,” Mulungu adzalowererapo kuti akonze zinthu. Ngakhale kuti pali anthu amaganizo abwino omwe akuyesetsa kulimbana ndi mavuto akusintha kwa nyengo, koma ngakhale atayesetsa bwanji, sangaletse kuti anthu asamawononge zachilengedwe.

 Ulosi: “Kudzaoneka zoopsa.”​—Luka 21:11.

 Baibulo linaneneratu kuti nthawi yathu ino “kudzaoneka zoopsa” kapena kuti zinthu zochititsa mantha. Kusintha kwa nyengo kwayambitsa mavuto aakulu padziko lonse. Masiku ano, anthu ambiri amachita mantha kuti dzikoli lidzawonongekeratu moti nthawi ina sipadzapezekanso aliyense.

 Ulosi: “Koma dziwa kuti, masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osakhulupirika, . . . osafuna kugwirizana ndi anzawo, . . . achiwembu, osamva za ena.”​—2 Timoteyo 3:1-4.

 Baibulo linaneneratu za makhalidwe oipa omwe anthu adzakhale nawo omwe adzachititse kuti pakhale mavuto akusintha kwa nyengo. Maboma komanso anthu ochita bizinesi azidzangoganizira zopanga ndalama, n’kunyalanyaza mmene moyo wa mibadwo yobwera m’tsogolo udzakhalire. Ngakhale anthu atayesetsa bwanji kugwirira ntchito limodzi, amalephera kupeza njira zabwino zoteteza kuti dzikoli lisamatenthe.

 Ulosiwu ukusonyeza kuti tisamayembekezere kuti anthu onse adzasintha zochita zawo ndi kuteteza dzikoli. Koma Baibulo limanena za anthu oipa omwe ali ndi mtima wodzikonda kuti “adzaipiraipirabe.”​—2 Timoteyo 3:13.

N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Mulungu adzathetsa vutoli?

 Baibulo limafotokoza kuti Yehova a Mulungu amene ndi Mlengi wathu, amasamala kwambiri za anthufe komanso za dziko lomwe tikukhalapoli. Taonani malemba atatu awa omwe akutitsimizira kuti Mulungu adzathetsadi vutoli.

  1.  1. Mulungu “[Dzikoli] sanalilenge popanda cholinga, . . . analiumba kuti anthu akhalemo”​—Yesaya 45:18.

     Mulungu adzakwaniritsa cholinga chomwe analengera dzikoli (Yesaya 55:11) Iye sadzalola kuti liwonongeke kapena kukhala lopanda anthu.

  2.  2. “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”​—Salimo 37:11, 29.

     Mulungu akulonjeza kuti anthu adzakhala padziko lapansili kwamuyaya komanso mwamtendere.

  3.  3. “Oipa adzachotsedwa padziko lapansi.”​—Miyambo 2:22.

     Mulungu akulonjeza kuti adzachotsa anthu omwe akukakamirabe kuchita zinthu zoipa kuphatikizapo omwe akuwononga dzikoli.

Zomwe Mulungu adzachite kuti tikhale ndi tsogolo labwino

 Kodi Mulungu adzachita zotani kuti adzakwaniritse zomwe analonjeza zokhudza dzikoli? Iye adzagwiritsa ntchito boma lomwe lidzalamulire dziko lonse. Bomali ndi lomwe limadziwikanso kuti Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 6:10) Ufumuwu uzidzalamulira kuchokera kumwamba ndipo sudzakhala ndi zokambirana zilizonse ndi maboma a anthu pa nkhani yokhudza dzikoli komanso zachilengedwe. Koma udzachotsa maboma onse a anthu ndipo iwo wokha ndi umene uzidzalamulira.​—Danieli 2:44.

 Ufumu wa Mulungu udzabweretsa zinthu zabwino zomwe anthu adzasangalale nazo ndipo chilengedwechi chidzakonzedwanso kukhala chabwino. (Salimo 96:10-13) Taganizirani zinthu izi zomwe Yehova Mulungu adzachite pogwiritsa ntchito Ufumu wake.

  •   Adzabwezeretsa chilengedwe m’malo mwake

     Zimene Baibulo limanena: “Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”​—Yesaya 35:1.

     Mmene zidzakhudzire tsogolo lathu: Yehova adzakonza dzikoli kukhala malo abwino kwambiri. Ngakhale malo omwe anawonongedwa kwambiri ndi anthu, adzakonzedwanso.

  •   Adzalamulira mphamvu zam’chilengedwe

     Zimene Baibulo limanena: “[Yehova] amachititsa mphepo yamkuntho kukhala bata, moti mafunde a panyanja amadekha.”​—Salimo 107:29.

     Mmene zidzakhudzire tsogolo lathu: Yehova ali ndi mphamvu zolamulira chilichonse m’chilengedwechi. Anthu sadzavutikanso ndi mphamvu zosalamulirika zam’chilengedwe.

  •   Adzaphunzitsa anthu kusamalira dzikoli

     Zimene Baibulo limanena: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.”​—Salimo 32:8.

     Mmene zidzakhudzire tsogolo lathu: Yehova anapatsa anthu udindo woti azisamalira dzikoli. (Genesis 1:28; 2:15) Iye adzatiphunzitsa mmene tingasamalire zachilengedwe kuti zisadzawonongeke

a Yehova, ndi dzina lenileni la Mulungu (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?