Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngati Mukudwala Matenda Aakulu

Ngati Mukudwala Matenda Aakulu

A Linda omwe ali ndi zaka 71 ananena kuti: “Adokotala atandiuza kuti andipeza ndi khansa ya m’mapapo komanso m’matumbo, ndinangoona kuti ndiye kuti basi ndifa. Koma nditafika kunyumba, ndinadziuza kuti, ‘N’zoona kuti zimenezi si zimene ndimayembekezera, koma zateremu ndikungofunika kupeza njira yondithandiza kupirira mavuto angawa.’”

A Elise azaka 49 anati: “Ndimadwala matenda enaake opweteka kwambiri amene amachititsanso kuti mitsempha yakumanzere kwa nkhope yanga isamagwire bwino ntchito. Nthawi zina ndimavutika maganizo chifukwa choti ndimamva kupweteka kwambiri. M’mbuyomu zikatero ndinkaona kuti ndili ndekhandekha ndipo ndinkaganiza zongodzipha.”

NGATI inuyo kapena munthu amene mumamukonda anapezeka ndi matenda aakulu, muyenera kuti mukudziwa mmene zoterezi zimapwetekera. Kuwonjezera pa matendawo, nthawi zambiri munthu amavutikanso ndi nkhawa, maganizo ofooketsa komanso amakhala ndi mantha. Zimenezi zimawonjezereka akamaganizira zoti akufunika kukaonana ndi dokotala, akamalephera kupeza thandizo loyenera la matendawo kapena ndalama zolipirira kuchipatala kapenanso akamakumana ndi mavuto ena chifukwa cha mankhwala amene akulandira. Zonsezi zikusonyeza kuti munthu amene akudwala matenda aakulu amakumana ndi mavuto ambiri.

Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize tikakumana ndi zoterezi? Anthu ambiri amaona kuti akamadalira Mulungu n’kumapemphera kwa iye komanso kuwerenga mavesi olimbikitsa a m’Baibulo, zimawathandiza. Tingapezenso thandizo kuchokera kwa achibale komanso anzathu omwe amatikonda.

ZIMENE ZATHANDIZA ENA

A Robert azaka 58 ananena kuti: “Muzidalira Mulungu ndipo adzakuthandizani kuti mupirire. Muzipemphera kwa iye n’kumuuza mmene mukumvera. Muzimupemphanso kuti akupatseni mzimu woyera komanso mphamvu kuti muzilimbikitsa banja lanu ndiponso kuti muthe kupirira.”

A Robert ananenanso kuti: “Zimakhala zothandiza anthu a m’banja lako akamakulimbikitsa kuti usamade nkhawa. Tsiku lililonse munthu mmodzi kapena awiri amandiimbira foni n’kundifunsa kuti, ‘Lero mwadzukako bwanji?’ Komanso anzanga amene amakhala m’madera osiyanasiyana amandilimbikitsa. Zimenezi zimandipatsa mphamvu komanso zimachititsa kuti ndizimvako bwino.”

Mukapita kukaona mnzanu amene akudwala muzikumbukira zimene a Linda ananena. Iwo anati: “Munthu amene akudwala amafuna kuti azikhala ngati munthu wina aliyense ndipo nthawi zambiri safuna kuti muzingokambirana za matenda akewo. Choncho yesetsani kuti muzicheza naye nkhani zina.”

Mothandizidwa ndi Mulungu, mfundo za m’Baibulo, achibale komanso anzathu, tingakwanitse kupirira n’kumaona kuti tingathe kupitirizabe kukhala ndi moyo ngakhale kuti tikudwala matenda aakulu.